Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yoweli 2:1-2

Chilango cha Mulungu

Lizani lipenga mu Ziyoni.
    Chenjezani pa phiri langa loyera.
Onse okhala mʼdziko anjenjemere,
    pakuti tsiku la Yehova likubwera,
layandikira;
    tsiku la mdima ndi chisoni,
    tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani.
Ngati mʼbandakucha umene wakuta mapiri,
    gulu lalikulu ndi la ankhondo amphamvu likubwera,
gulu limene nʼkale lomwe silinaonekepo
    ngakhale kutsogolo kuno silidzaonekanso.

Yoweli 2:12-17

Ngʼambani Mtima Wanu

12 “Ngakhale tsopano,
    bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse
    posala zakudya ndi kukhetsa misozi,” akutero Yehova.

13 Ngʼambani mtima wanu
    osati zovala zanu.
Bwererani kwa Yehova Mulungu wanu,
    pakuti Iye ndi wokoma mtima ndi wachifundo,
wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka,
    ndipo amaleka kubweretsa mavuto.
14 Akudziwa ndani? Mwina adzasintha maganizo nʼkutimvera chisoni,
    nʼkutisiyira madalitso,
a chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa
    kwa Yehova Mulungu wanu.

15 Lizani lipenga mu Ziyoni,
    lengezani tsiku losala zakudya,
    itanitsani msonkhano wopatulika.
16 Sonkhanitsani anthu pamodzi,
    muwawuze kuti adziyeretse;
sonkhanitsani akuluakulu,
    sonkhanitsani ana,
    sonkhanitsani ndi oyamwa omwe.
Mkwati atuluke mʼchipinda chake,
    mkwatibwi atuluke mokhala mwake.
17 Ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova,
    alire pakati pa guwa lansembe ndi khonde la Nyumba ya Yehova.
Azinena kuti, “Inu Yehova, achitireni chifundo anthu anu.
    Musalole kuti cholowa chanu chikhale chinthu chonyozeka,
    kuti anthu a mitundu ina awalamulire.
Kodi nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina amanena kuti,
    ‘Ali kuti Mulungu wawo?’ ”

Yesaya 58:1-12

Kusala Kwenikweni

58 “Fuwula kwambiri, usaleke.
    Mawu ako amveke ngati lipenga.
Uwawuze anthu anga za kulakwa kwawo;
    uwuze nyumba ya Yakobo za machimo awo.
Pakuti tsiku ndi tsiku amafunafuna Ine;
    amaoneka ngati a chidwi chofuna kudziwa zimene ndimafuna,
kukhala ngati kuti ndi dziko limene limachita zolondola
    ndipo silinasiye zolamulira za Mulungu wake.
Amandipempha kuti ndigamule mlandu wawo mwachilungamo
    ndipo amaonetsa chidwi chofuna kukhala pafupi ndi Mulungu.
Anthu akufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani ife tasala
    kudya pamene Inu simukulabadirapo?
Kodi ife tavutikiranji nʼkudzichepetsa
    pamene Inu simunasamalepo?’ ”

Yehova akuti, “Komatu tsiku lanu losala kudya, mumachita zinthu zokukondweretsani,
    ndipo mumazunza antchito anu onse.
Mumati uku mukusala kudya, uku mukukangana ndi kumenyana,
    mpaka kumenyana ndi nkhonya zopweteka.
Kusala kudya mukuchitiramu musayembekezere kuti mawu anu amveka kumwamba.
Kodi kusala kudya kumene ndimakufuna Ine nʼkumeneku,
    kungokhala tsiku loti munthu adzichepetse basi?
Kodi ndi tsiku loti munthu angowerama pansi ngati bango
    ndi kumayala ziguduli nʼkuthirapo phulusa nʼkugonapo?
Kodi ndiye mumati kusala kudya kumeneko,
    tsiku lokondweretsa Yehova?

“Kodi si uku kusala kudya kumene Ine ndimakufuna:
Kumasula maunyolo ozunzizira anthu
    ndi kumasula zingwe za goli,
kupereka ufulu kwa oponderezedwa
    ndi kuphwanya goli lililonse?
Anthu anjala kodi mwawagawira chakudya chanu?
    Osowa ndi ongoyendayenda,
kodi mwawapatsa malo ogona?
    Munthu wausiwa kodi mwamupatsa chovala?
Mukatero chipulumutso chanu chidzabwera ngati mʼbandakucha,
    ndipo mabala anu adzachira msangamsanga;
chilungamo chanu chidzakutsogolerani
    ndipo ulemerero wa Yehova udzakhala chokutchinjirizani kumbuyo kwanu.
Mukamadzapemphera Yehova adzakuyankhani;
    mukadzapempha thandizo, Iye adzati: Ine ndili pano.

“Ngati muleka kuzunza anzanu,
    ngati musiya kuloza chala ndiponso kunena zoyipa za anzanu.
10 Ndipo ngati mudyetsa anthu anjala,
    ndi kuthandiza anthu oponderezedwa,
pamenepo kuwala kwanu kudzaonekera mu mdima,
    ndipo usiku wanu udzakhala ngati usana.
11 Yehova adzakutsogolerani nthawi zonse;
    adzakwaniritsa zosowa zanu mʼdziko longʼalukangʼaluka dzuwa
    ndipo adzalimbitsa matupi anu.
Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri,
    ngati kasupe amene madzi ake saphwa.
12 Anthu ako adzamanganso nyumba zimene zakhala mabwinja nthawi yayitali,
    ndipo adzamanganso pa maziko akalekale;
inu mudzatchedwa okonza makoma opasuka.
    Anthu okonza misewu ndi nyumba zake.

Masalimo 51:1-17

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pamene Mneneri Natani anabwera kwa iye atachita chigololo ndi Batiseba.

51 Mundichitire chifundo, Inu Mulungu,
    molingana ndi chikondi chanu chosasinthika;
molingana ndi chifundo chanu chachikulu
    mufafanize mphulupulu zanga.
Munditsuke zolakwa zanga zonse
    ndipo mundiyeretse kuchotsa tchimo langa.

Pakuti ndikudziwa mphulupulu zanga,
    ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse.
Motsutsana ndi Inu, Inu nokha, ndachimwa
    ndipo ndachita zoyipa pamaso panu,
Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama
    pamene muyankhula ndi pamene muweruza.
Zoonadi ine ndinali wochimwa pomwe ndimabadwa,
    wochimwa kuyambira pa nthawi imene amayi anga anakhala woyembekezera ine.
Zoonadi inu mumafuna choonadi mu ziwalo zamʼkati mwanga;
    mumandiphunzitsa nzeru mʼkati mwanga mwenimweni.

Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera,
    munditsuke ndipo ndidzayera kuposa matalala
Mundilole ndimve chimwemwe ndi chisangalalo,
    mulole kuti mafupa amene mwawamphwanya akondwere.
Mufulatire machimo anga
    ndi kufafaniza zolakwa zanga zonse.

10 Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu
    ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.
11 Musandichotse pamaso panu
    kapena kuchotsa Mzimu wanu Woyera mwa ine.
12 Bwezeretsani mwa ine chimwemwe cha chipulumutso chanu
    ndipo mundipatse mzimu wofuna kumvera kuti undilimbitse.

13 Pamenepo ndidzaphunzitsa anthu amphulupulu njira zanu
    kuti ochimwa adzabwerere kwa inu.
14 Mundipulumutse ku tchimo lokhetsa magazi, Inu Mulungu,
    Mulungu wa chipulumutso changa,
    ndipo lilime langa lidzayimba zachilungamo chanu.
15 Inu Ambuye tsekulani milomo yanga,
    ndipo pakamwa panga padzalengeza matamando anu.
16 Inu simusangalatsidwa ndi nsembe wamba.
    Ndikanapereka nsembe yopsereza, Inu simukondwera nayo.
17 Nsembe za Mulungu ndi mzimu wosweka;
    mtima wosweka ndi wachisoni
    Inu Mulungu simudzawunyoza.

2 Akorinto 5:20-6:10

20 Choncho ife ndi akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu akudandaulira anthu kudzera mwa ife. Ife tikukupemphani inu mʼmalo mwa Khristu kuti, yanjanitsidwani ndi Mulungu. 21 Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.

Pogwira naye ntchito pamodzi, tikukudandaulirani kuti musangolandira chisomo cha Mulungu pachabe. Pakuti akunena kuti,

“Pa nthawi yanga yabwino yokomera anthu mtima ndinakumvera,
    ndipo pa nthawi yopulumutsa ndinakuthandiza.

Taonani, ndikukuwuzani kuti, ino ndiyo nthawi yabwino ya Ambuye, lero ndiye tsiku la chipulumutso.”

Masautso a Paulo

Ife sitikuyika chokhumudwitsa pa njira ya wina aliyense, kuti utumiki wathu usanyozeke. Mʼmalo mwake, mwanjira iliyonse timasonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu popirira kwambiri mʼmasautso, mʼzowawa ndi mʼzodetsa nkhawa. Pomenyedwa, kuponyedwa mʼndende ndi mʼzipolowe. Pogwira ntchito mwamphamvu, posagona usiku onse, posowa chakudya; pokhala moyo woyera mtima, pomvetsa zinthu, wokoma mtima ndi wachifundo mwa Mzimu Woyera ndi mwachikondi choonadi ndi poyankhula choonadi mwamphamvu ya Mulungu. Zida zimene zili mʼdzanja lamanja ndi lamanzere ndizo chilungamo. Timatumikira Mulungu ngakhale ena amatinyoza ndi ena amatilemekeza, ena amatinenera chipongwe, enanso amatiyamikira. Ena amatitenga kukhala ngati onena zoona, ndipo enanso amatitenga kukhala ngati onena zabodza. Amatiyesa osadziwika komatu ndife odziwika kwambiri. Amatiyesa wooneka ngati tikufa, koma tikupitirirabe ndi moyo, okanthidwa, koma osaphedwa. 10 Amatiyesa achisoni, koma ndife achimwemwe nthawi zonse, aumphawi, koma olemeretsa ambiri; wopanda kanthu, koma tili ndi zonse.

Mateyu 6:1-6

Zopereka Zachifundo

“Samalani kuti musachite ntchito zanu zolungama pamaso pa anthu kuti akuoneni. Popeza ngati mutero simudzalandira mphotho yochokera kwa Atate anu akumwamba.

“Pamene mupereka zachifundo, musachite modzionetsera monga amachita achiphamaso mʼmasunagoge ndi pa misewu kuti atamidwe ndi anthu. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwowo alandiriratu mphotho yawo yonse. Koma pamene mupereka zachifundo, dzanja lanu lamanzere lisadziwe chimene dzanja lanu lamanja likuchita, kotero kuti kupereka kwanu kukhale mwachinsinsi. Ndipo Atate anu amene amaona zochitika mwachinsinsi, adzakupatsani mphotho.

Za Kupemphera

“Pamene mupemphera, musakhale ngati achiphamaso, chifukwa iwo amakonda kupemphera choyimirira mʼmasunagoge ndi pa mphambano za mʼmisewu kuti anthu awaone. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse. Koma pamene mupemphera, lowani mʼchipinda chanu chamʼkati, ndi kutseka chitseko ndipo mupemphere kwa Atate anu amene saoneka. Ndipo Atate anu, amene amaona zochitika mseri, adzakupatsani mphotho.

Mateyu 6:16-21

Kusala Kudya

16 “Pamene mukusala kudya, musaonetse nkhope yachisoni monga achita achiphamaso, pakuti iwo amasintha nkhope zawo kuonetsa anthu kuti akusala kudya. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse. 17 Koma pamene ukusala kudya, samba mʼmaso nudzole mafuta kumutu, 18 kuti usaonekere kwa anthu kuti ukusala kudya koma kwa Atate ako ali mseri; ndipo Atate ako amene amaona za mseri adzakupatsa mphotho.

Za Chuma cha Kumwamba

19 “Musadziwunjikire chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga ndi pamene mbala zimathyola ndi kuba. 20 Koma mudziwunjikire chuma kumwamba kumene njenjete ndi dzimbiri siziwononga ndipo mbala sizithyola ndi kuba. 21 Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako udzakhala komweko.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.