Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 40:21-31

21 Kodi simukudziwa?
    Kodi simunamve?
Kodi sanakuwuzeni kuyambira pachiyambi pomwe?
    Kodi simunamvetsetse chiyambire cha dziko lapansi?
22 Yehova amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba ndiye analenga dziko lapansi,
    Iye amaona anthu a dziko lapansi ngati ziwala.
Ndipo anafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchinga,
    nayikunga ngati tenti yokhalamo.
23 Amatsitsa pansi mafumu amphamvu
    nasandutsa olamula a dziko kukhala achabechabe.
24 Inde, iwo ali ngati mbewu zimene zangodzalidwa kumene
    kapena kufesedwa chapompano,
    ndi kungoyamba kuzika mizu kumene
ndi pamene mphepo imawombapo nʼkuziwumitsa
    ndipo kamvuluvulu amaziwulutsa ngati mankhusu.

25 Woyera uja akuti, “Kodi mudzandiyerekeza Ine ndi yani?
    Kapena kodi alipo wofanana nane?”
26 Tayangʼanani mlengalenga ndipo onani.
    Kodi ndani analenga zonsezi mukuzionazi?
Yehova ndiye amene amazitsogolera ngati gulu la ankhondo,
    nayitana iliyonse ndi dzina lake.
Ndipo popeza Iye ali ndi nyonga zambiri,
    palibe ndi imodzi yomwe imene inasowapo.

27 Iwe Yakobo, chifukwa chiyani umanena
    ndi kumadandaula iwe Israeli, kuti,
“Yehova sakudziwa mavuto anga,
    Mulungu wanga sakusamala zomwe zikundichitikira ine?”
28 Kodi simukudziwa?
    Kodi simunamve?
Yehova ndiye Mulungu wamuyaya,
    ndiyenso Mlengi wa dziko lonse lapansi.
Iye sadzatopa kapena kufowoka
    ndipo palibe amene angadziwe maganizo ake.
29 Iye amalimbitsa ofowoka
    ndipo otopa amawawonjezera mphamvu.
30 Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufowoka,
    ndipo achinyamata amapunthwa ndi kugwa;
31 koma iwo amene amakhulupirira Yehova
    adzalandira mphamvu zatsopano.
Adzawuluka ngati chiwombankhanga;
    adzathamanga koma sadzalefuka,
    adzayenda koma sadzatopa konse.

Masalimo 147:1-11

147 Tamandani Yehova.

Nʼkwabwino kwambiri kuyimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wathu,
    nʼkokondweretsa ndi koyenera kumutamanda!

Yehova akumanga Yerusalemu;
    Iye akusonkhanitsa amʼndende a Israeli.
Akutsogolera anthu osweka mtima
    ndi kumanga mabala awo.

Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi,
    ndipo iliyonse amayitchula dzina.
Yehova ndi wamkulu ndi wamphamvu kwambiri;
    nzeru zake zilibe malire.
Yehova amagwiriziza anthu odzichepetsa,
    koma amagwetsa pansi anthu oyipa.

Imbirani Yehova ndi mayamiko;
    imbani nyimbo kwa Mulungu ndi pangwe.
Iye amaphimba mlengalenga ndi mitambo;
    amapereka mvula ku dziko lapansi
    ndi kumeretsa udzu mʼmapiri.
Iye amapereka chakudya kwa ngʼombe
    ndi kwa ana a makwangwala pamene akulira chakudya.

10 Chikondwerero chake sichili mʼmphamvu za kavalo,
    kapena mʼmiyendo ya anthu amphamvu.
11 Yehova amakondwera ndi amene amamuopa,
    amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosasinthika.

Masalimo 147:20

20 Sanachitepo zimenezi kwa mtundu wina uliwonse wa anthu;
    anthu enawo sadziwa malamulo ake.

Tamandani Yehova.

1 Akorinto 9:16-23

16 Komatu ndikamalalikira Uthenga Wabwino, sindingadzitamandire popeza ndimawumirizidwa kulalikira. Tsoka kwa ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino! 17 Ngati ndikugwira ntchitoyi mwakufuna kwanga, ndili ndi mphotho; koma ngati si mwakufuna kwanga, ndiye kuti ntchitoyi ndi Ambuye anandipatsa. 18 Tsono mphotho yanga ndi chiyani? Ndi iyi: kuti polalikira Uthenga Wabwino ndiwupereke kwaulere komanso kuti ndisagwiritse ntchito ufulu wanga polalikira uthengawo.

Ufulu wa Paulo

19 Ngakhale ndine mfulu ndipo sindine kapolo wa munthu, ndimadzisandutsa kapolo wa aliyense kuti ndikope ambiri mmene ndingathere. 20 Kwa Ayuda ndimakhala ngati Myuda kuti ndikope Ayuda. Kwa olamulidwa ndi Malamulo ndimakhala ngati wolamulidwa nawo (ngakhale kuti sindine wolamulidwa ndi Malamulowo) kuti ndikope amene amalamulidwa ndi Malamulo. 21 Kwa amene alibe Malamulo ndimakhala wopanda Malamulo (ngakhale kuti sindine wopanda Malamulo a Mulungu koma ndili pansi pa ulamuliro wa Khristu) kuti ndikope wopanda Malamulo. 22 Kwa ofowoka ndimakhala wofowoka, kuti ndikope ofowoka. Ndimachita zinthu zilizonse kwa anthu onse kuti mwanjira ina iliyonse ndipulumutse ena. 23 Ndimachita zonsezi chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndigawane nawo madalitso ake.

Marko 1:29-39

Yesu Achiritsa Anthu Ambiri

29 Atangochoka mu sunagoge, Yesu pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane anakalowa mʼnyumba ya Simoni ndi Andreya. 30 Mpongozi wa Simoni anali chigonere akudwala malungo, ndipo anamuwuza Yesu za iye. 31 Ndipo Yesu anapita kwa iye, namugwira dzanja namuthandiza kudzuka. Malungo anachoka ndipo anayamba kuwatumikira.

32 Madzulo omwewo dzuwa litalowa anthu anabweretsa kwa Yesu anthu onse odwala ndi ogwidwa ndi ziwanda. 33 Anthu onse a mʼmudzimo anasonkhana pa khomo, 34 Yesu anachiritsa ambiri amene anali ndi matenda osiyanasiyana, komanso anatulutsa ziwanda zambiri, ndipo sanalole kuti ziwandazo ziyankhule chifukwa zinkamudziwa Iye.

Yesu Apemphera Kumalo a Yekha

35 Mmamawa, kukanali kamdima, Yesu anadzuka, nachoka pa nyumbapo kupita kumalo kwa yekha, kumene anakapemphera. 36 Simoni ndi anzake anapita kokamufunafuna Iye, 37 ndipo atamupeza, anamuwuza kuti, “Aliyense akukufunani!”

38 Yesu anayakha kuti, “Tiyeni tipite kwina ku midzi ya pafupi kuti ndikalalikirenso kumeneko. Ichi ndi chifukwa chimene ndinabwerera.” 39 Potero anayendayenda mu Galileya, kulalikira mʼmasunagoge awo ndi kutulutsa ziwanda.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.