Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 111

111 Tamandani Yehova.

Ndidzathokoza Yehova ndi mtima wanga wonse
    mʼbwalo la anthu olungama mtima ndi pa msonkhano.

Ntchito za Yehova nʼzazikulu;
    onse amene amakondwera nazo amazilingalira.
Zochita zake ndi za ulemerero ndi zaufumu,
    ndipo chilungamo chake ndi chosatha.
Iye wachititsa kuti zodabwitsa zake zikumbukirike;
    Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo.
Amapereka chakudya kwa amene amamuopa Iye;
    amakumbukira pangano lake kwamuyaya.
Waonetsa anthu ake mphamvu ya ntchito zake,
    kuwapatsa mayiko a anthu a mitundu ina.
Ntchito za manja ake ndi zokhulupirika ndi zolungama;
    malangizo ake onse ndi odalirika.
Malamulo ndi okhazikika ku nthawi za nthawi,
    ochitidwa mokhulupirika ndi molungama.
Iyeyo amawombola anthu ake;
    anakhazikitsa pangano lake kwamuyaya
    dzina lake ndi loyera ndi loopsa.

10 Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru;
    onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu.
    Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.

Deuteronomo 13:1-5

Kupembedza Milungu Ina

13 Ngati mneneri kapena wina aliyense amene amanena zamʼtsogolo mwa maloto atuluka pakati panu, nalengeza za chizindikiro chozizwitsa kapena chodabwitsa, chinthu nʼkuchitikadi, tsono iyeyo nʼkunena kuti, “Tiyeni titsatire milungu ina, tiyeni tiyipembedze,” (kunena milungu imene simunayidziwe), musamumvere mneneriyo kapena wolotayo. Yehova Mulungu wanu afuna akuyeseni kuti aone ngati mumamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. Muyenera kutsatira Yehova Mulungu wanu, ndipo ndi Iyeyo amene muyenera kumuopa. Muzisunga malamulo ake ndi kumamumvera, muzimutumikira ndipo kumukangamira Iyeyo. Mneneri kapena wolotayo ayenera kuphedwa, popeza analalikira zopandukira Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto ndi kukupulumutsani ku dziko la ukapolo. Wolalikirayo anafuna kukupatutsani pa njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani kuti muyitsatire. Muzichotsa choyipa pakati panu.

Mateyu 8:28-9:1

Ogwidwa ndi Ziwanda a ku Gadara

28 Ndipo atafika ku mbali ina ya dera la Gadara, anakumana ndi anthu awiri ogwidwa ndi ziwanda akuchokera ku manda. Iwowa anali woopsa kwambiri kotero kuti panalibe munthu akanatha kudzera njira imeneyo. 29 Ndipo iwo anafuwulira kwa Yesu nati, “Mukufuna chiyani kwa ife, Inu Mwana wa Mulungu? Kodi mwabwera kuno kudzatizunza nthawi yake isanafike?”

30 Ndipo patali pake panali gulu la nkhumba zimene zimadya. 31 Ndipo ziwandazo zinamupempha Yesu kuti, “Ngati mutitulutsa ife mutitumize mu nkhumba izo.”

32 Iye anati kwa ziwandazo, “Pitani!” Ndipo pamenepo zinatuluka ndi kukalowa mʼnkhumbazo ndipo nkhumba zonse zinathamangira mʼnyanja ndi kufera momwemo. 33 Koma amene amaziweta anathawa nalowa mʼmudzi nafotokoza zonse, kuphatikizapo zimene zinachitika ndi anthu ogwidwa ndi ziwanda aja. 34 Ndipo anthu onse a mʼmudziwo anatuluka kukakumana ndi Yesu. Ndipo atamuona Iye, anamupempha kuti achoke mʼdera lawo.

Munthu Wakufa Ziwalo wa ku Kaperenawo

Yesu analowa mʼbwato nawoloka, ndipo anabwera ku mudzi wa kwawo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.