Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
111 Tamandani Yehova.
Ndidzathokoza Yehova ndi mtima wanga wonse
mʼbwalo la anthu olungama mtima ndi pa msonkhano.
2 Ntchito za Yehova nʼzazikulu;
onse amene amakondwera nazo amazilingalira.
3 Zochita zake ndi za ulemerero ndi zaufumu,
ndipo chilungamo chake ndi chosatha.
4 Iye wachititsa kuti zodabwitsa zake zikumbukirike;
Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo.
5 Amapereka chakudya kwa amene amamuopa Iye;
amakumbukira pangano lake kwamuyaya.
6 Waonetsa anthu ake mphamvu ya ntchito zake,
kuwapatsa mayiko a anthu a mitundu ina.
7 Ntchito za manja ake ndi zokhulupirika ndi zolungama;
malangizo ake onse ndi odalirika.
8 Malamulo ndi okhazikika ku nthawi za nthawi,
ochitidwa mokhulupirika ndi molungama.
9 Iyeyo amawombola anthu ake;
anakhazikitsa pangano lake kwamuyaya
dzina lake ndi loyera ndi loopsa.
10 Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru;
onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu.
Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.
23 Nthawi imeneyo ndinachonderera Yehova kuti, 24 “Ambuye Mulungu, mwayamba tsopano kuonetsa mtumiki wanu ukulu wanu ndi dzanja lanu lamphamvu. Ndi mulungu uti ali kumwamba kapena pa dziko lapansi amene angachite ntchito zozizwitsa zimene mumachita? 25 Mundilole ndipite ndi kukaona dziko labwinolo kutsidya kwa Yorodani dziko la mapiri abwinowo ndi Lebanoni.”
26 Koma chifukwa cha inu, Yehova anakwiya nane osandimvera. Yehova anati, “Basi pakwana, usayankhulenso ndi ine zimenezi. 27 Pita pamwamba pa phiri la Pisiga ndipo uyangʼane kumadzulo, kumpoto, kummwera ndi kummawa. Ulione dzikolo ndi maso ako pakuti suwoloka Yorodaniyu. 28 Koma langiza Yoswa ndipo umulimbikitse ndi kumupatsa mphamvu pakuti adzatsogolera anthu awa kuwoloka ndipo adzawathandiza kuti atenge dziko limene ulioneli.” 29 Ndipo tinakhala mʼchigwa pafupi ndi Beti-Peori.
6 Sikuti mawu a Mulungu analephera. Pakuti si onse obadwa mwa Israeli amene ndi Israeli. 7 Kapena kuti ana ake chifukwa anachokera mwa Abrahamu. Koma zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake. 8 Kutanthauza kuti, si ana obadwa mʼthupi amene ndi ana a Mulungu koma ndi ana a lonjezano amene amatengedwa kukhala zidzukulu za Abrahamu. 9 Pakuti Mulungu analonjeza ponena kuti, “Pa nthawi yake ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”
10 Ndipo si pokhapo ayi. Ana awiri a Rebeka aja abambo awo anali mmodzi, kholo lathu Isake. 11 Komabe, ana amapasawa asanabadwe kapena asanachite chilichonse chabwino kapena choyipa, nʼcholinga choti chifuniro cha Mulungu chosankhiratu munthu aliyense chipitirire, 12 osati chifukwa cha ntchito za munthu koma chifuniro cha Iye mwini, anawuza Rebeka kuti, “Wamkulu adzatumikira wamʼngʼono.” 13 Monga momwe kwalembedwa kuti, “Ine ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.”
14 Nanga tsono tidzanena chiyani? Kodi Mulungu ndi osalungama? Ayi, ndi pangʼono pomwe! 15 Pakuti Mulungu anawuza Mose kuti,
“Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo,
ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.”
16 Nʼchifukwa chake, izi sizitengera zokhumba za munthu kapena kuyesetsa koma chifundo cha Mulungu. 17 Malemba akuti Mulungu anamuwuza Farao kuti, “Ine ndakuyika kukhala mfumu ndi cholinga choti ndionetse mphamvu zanga, kuti mwa iwe dzina langa litchuke pa dziko lonse lapansi.” 18 Choncho Mulungu amachitira chifundo munthu amene akufuna kumuchitira chifundo ndipo amawumitsa mtima munthu amene Iye akufuna kumuwumitsa mtima.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.