Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Potsata mayimbidwe a “Akakombo.”
69 Pulumutseni Inu Mulungu,
pakuti madzi afika mʼkhosi
2 Ine ndikumira mʼthope lozama
mʼmene mulibe popondapo.
Ndalowa mʼmadzi ozama;
mafunde andimiza.
3 Ndafowoka ndikupempha chithandizo;
kummero kwanga kwawuma gwaa,
mʼmaso mwanga mwada
kuyembekezera Mulungu wanga.
4 Iwo amene amadana nane popanda chifukwa
ndi ochuluka kuposa tsitsi la kumutu kwanga;
ambiri ndi adani anga popanda chifukwa,
iwo amene akufunafuna kundiwononga.
Ndikukakamizidwa kubwezera
zomwe sindinabe.
5 Mukudziwa uchitsiru wanga, Inu Mulungu,
kulakwa kwanga sikuli kobisika kwa Inu.
30 Ine ndidzatamanda dzina la Mulungu mʼnyimbo,
ndidzalemekeza Iye ndi chiyamiko.
31 Izi zidzakondweretsa Yehova kupambana ngʼombe,
kupambananso ngʼombe yayimuna, pamodzi ndi nyanga ndi ziboda zake.
32 Wosauka adzaona ndipo adzasangalala,
Inu amene mumafunafuna Mulungu, mitima yanu ikhale ndi moyo!
33 Yehova amamvera anthu osowa
ndipo sanyoza anthu ake omangidwa.
34 Kumwamba ndi dziko lapansi zitamanda Iye,
nyanja ndi zonse zomwe zimayenda mʼmenemo,
35 pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni
ndi kumanganso mizinda ya Yuda,
anthu adzakhala kumeneko ndipo dzikolo lidzakhala lawo;
36 ana atumiki ake adzalitenga kukhala cholowa chawo,
ndipo iwo amene amakonda dzina lake adzakhala kumeneko.
Pangano la Mdulidwe
17 Pamene Abramu anali ndi zaka 99, Yehova anamuonekera nati, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse. Ukhale munthu wochita zolungama nthawi zonse. 2 Ndipo Ine ndikulonjeza kuti ndidzakupatsa zidzukulu zambiri.”
3 Pomwepo Abramu anadziponya pansi ndipo Mulungu anati kwa iye, 4 “Pangano langa ndi iwe ndi ili: Udzakhala kholo la mitundu yambiri ya anthu. 5 Sudzatchedwanso Abramu; dzina lako lidzakhala Abrahamu, chifukwa ndakusandutsa kukhala kholo la mitundu yambiri ya anthu. 6 Ndidzakupatsa zidzukulu zambiri motero kuti mitundu yambiri ya anthu idzatuluka mwa iwe. Mafumunso adzatuluka mwa iwe. 7 Pangano langa ndi iwe pamodzi ndi zidzukulu za mibado ya mʼtsogolo lidzakhala la muyaya. Ndidzakhala Mulungu wako ndi Mulungu wa zidzukulu zako. 8 Dziko lonse la Kanaani, limene iwe ukukhala tsopano, ndalipereka kwa iwe ndi kwa zidzukulu zako kuti likhale chuma chanu mpaka muyaya. Ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wa zidzukulu zako.”
9 Kenaka Mulungu anati kwa Abrahamu, “Koma iwe pamodzi ndi zidzukulu zako zobwera pambuyo pako mʼmibado ya mʼtsogolomo, sungani pangano langali. 10 Iwe pamodzi ndi zidzukulu zako zobwera pambuyo pako muzisunga pangano ili loti mwamuna aliyense pakati panupa azichita mdulidwe. 11 Kuyambira tsopano muzichita mdulidwe ndipo ichi chidzakhala chizindikiro cha pangano langa ndi iwe. 12 Kuyambira tsopano mpaka mibado ya mʼtsogolomo mwana wamwamuna aliyense pakati panu amene wakwana masiku asanu ndi atatu ayenera kuchita mdulidwe. Awa ndi ana obadwa mʼbanja lako, kapena akapolo ochita kugula ndi ndalama, mlendo osakhala wa mʼmbumba yako. 13 Achite mdulidwe ndithu mwana wamwamuna aliyense, mbadwa ngakhale kapolo wochita kugula ndi ndalama, ndipo ichi chidzakhala chizindikiro pa thupi lanu cha pangano langa lamuyaya.
Abrahamu Analungamitsidwa Mwachikhulupiriro
4 Nanga tsono tidzati chiyani za Abrahamu kholo lathu, iyeyu anapezana ndi zotani pa nkhani imeneyi? 2 Kunena zoona, Abrahamu akanalungamitsidwa ndi ntchito zake, akanakhala nako kanthu kodzitamandira, koma osati pamaso pa Mulungu. 3 Kodi Malemba akuti chiyani? “Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo ichi chinamuchititsa kukhala wolungama.”
4 Tsopano munthu amene wagwira ntchito, malipiro ake satengedwa kukhala ngati mphatso koma zimene anayenera kulandira. 5 Koma kwa munthu amene sanagwire ntchito ndipo akhulupirira Mulungu amene amalungamitsa ochimwa, chikhulupiriro chakecho chimatengedwa kukhala chilungamo. 6 Davide ponena zomwezi pamene anayankhula za kudala kwa munthu amene Mulungu amulungamitsa osati chifukwa cha ntchito zake akuti,
7 “Odala ndi amene
zoyipa zawo zakhululukidwa;
amene machimo awo afafanizidwa.
8 Ngodala munthu amene
machimo ake Ambuye sadzawakumbukiranso.”
9 Kodi madalitso amenewa ali kwa ochita mdulidwe okha kapena kwa amene sanachitepo mdulidwe? Ife takhala tikunena kuti chikhulupiriro cha Abrahamu chinamuchititsa kukhala wolungama. 10 Kodi chinatengedwa bwanji? Kodi nʼkuti iye atachita mdulidwe kapena asanachite? Osati atachita mdulidwe koma asanachite! 11 Ndipo iye anachita mdulidwe ngati chizindikiro ndi chitsimikizo cha kulungama kumene anali nako mwachikhulupiriro pomwe anali asanachite mdulidwe. Choncho, iye ndi kholo la onse amene akhulupirira koma sanachite mdulidwe, ndi cholinga chakuti alungamitsidwe. 12 Ndipo iyenso ndiyenso kholo la ochita mdulidwe osati amene anangochita mdulidwe kokha koma amene amatsata chitsanzo cha chikhulupiriro chimene kholo lathu Abrahamu anali nacho asanachite mdulidwe.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.