Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 60:1-6

Ulemerero wa Ziyoni

60 “Dzuka, wala, pakuti kuwala kwako kwafika,
    ndipo ulemerero wa Yehova wakuwalira.
Taona, mdima waphimba dziko lapansi
    ndipo mdima wandiweyani wagwa pa anthu a mitundu ina,
koma Yehova adzakuwalira iwe,
    ndipo ulemerero wake udzaoneka pa iwe.
Mitundu ya anthu idzatsata kuwunika kwako
    ndipo mafumu adzalondola kunyezimira kwa mʼbandakucha wako.

“Tukula maso ako, yangʼanayangʼana ndipo ona zimene zikuchitika.
    Onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe;
ana ako a amuna akubwera kuchokera kutali
    ndipo ana ako aakazi anyamulidwa mʼmanja.
Ukadzaona zimenezi udzasangalala kwambiri,
    mtima wako udzalumpha ndi kudzaza ndi chimwemwe;
chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe
    chuma cha mitundu ya anthu chidzabwera kwa iwe.
Gulu la ngamira lidzaphimba dziko lako,
    ngamira zingʼonozingʼono zidzachokera ku Midiyani ndi ku Efai.
Ndipo onse a ku Seba adzabwera
    atanyamula golide ndi lubani
    uku akutamanda Yehova.

Masalimo 72:1-7

Salimo la Solomoni.

72 Patsani mwana wa mfumu nzeru zanu zoweruzira mwa chilungamo,
    Inu Mulungu mupatseni mwana wa mfumu chilungamo chanu.
Iye adzaweruza anthu anu mwachilungamo,
    anthu anu ozunzika mosakondera.
Mapiri adzabweretsa chuma kwa anthu anu,
    timapiri tidzabweretsa zipatso zachilungamo.
Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu
    ndi kupulumutsa ana a anthu osowa;
    adzaphwanya ozunza anzawo.

Adzakhala ndi moyo pa mibado yonse,
    nthawi zonse pamene dzuwa ndi mwezi zikuwala.
Iye adzakhala kugwa kwa mvula pa minda yolimidwa
    ngati mivumbi yothirira dziko lapansi.
Mʼmasiku a munthu wolungama adzakhazikika;
    chuma chidzachuluka mpaka mwezi utaleka kuwala.

Masalimo 72:10-14

10 Mafumu a ku Tarisisi ndi a ku zilumba zakutali
    adzabweretsa mitulo kwa iye,
mafumu a ku Seba ndi Seba
    adzapereka mphatso kwa iyeyo.
11 Mafumu onse adzamuweramira
    ndipo mitundu yonse idzamutumikira.

12 Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira,
    wozunzika amene alibe wina womuthandiza.
13 Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowa
    ndi kupulumutsa osowa ku imfa.
14 Iye adzalanditsa iwo ku mazunzo ndi chiwawa
    pakuti magazi awo ndi amtengo wapatali pamaso pake.

Aefeso 3:1-12

Paulo Mlaliki wa Anthu a Mitundu Ina

Nʼchifukwa chake ine Paulo, ndili wamʼndende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu anthu a mitundu ina.

Ndithudi, inu munamva za ntchito yachisomo cha Mulungu imene anandipatsa chifukwa cha inu, ndicho chinsinsi chimene chinawululidwa kwa ine mwa vumbulutso, monga ndinakulemberani kale mwachidule. Pamene mukuwerenga izi, inu mudzazindikira za chidziwitso changa pa chinsinsi cha Khristu, chimene sichinawululidwe kwa anthu amibado ina monga momwe tsopano chawululidwa ndi Mzimu wa Mulungu mwa atumwi oyera ndi aneneri. Chinsinsicho nʼchakuti, kudzera mu Uthenga Wabwino anthu a mitundu ina ndi olowamʼmalo pamodzi ndi Aisraeli, ndi ziwalo za thupi limodzi, ndi olandira nawo pamodzi malonjezo a mwa Khristu Yesu.

Mwachisomo cha Mulungu ndi mphamvu zake, ine ndinasanduka mtumiki wa Uthenga Wabwinowu. Ngakhale ndili wamngʼono kwambiri pakati pa anthu onse a Mulungu, anandipatsa chisomo chimenechi cholalikira kwa anthu a mitundu ina chuma chopanda malire cha Khristu. Ndinasankhidwa kuti ndifotokoze momveka bwino kwa munthu aliyense za chinsinsi chimenechi, chinsinsi chimene kuyambira kale chinali chobisika mwa Mulungu amene analenga zinthu zonse. 10 Cholinga chake tsopano nʼchakuti, kudzera mwa mpingo, mafumu ndi a ulamuliro onse a kumwamba adziwe nzeru zochuluka za Mulungu. 11 Chimenechi chinali chikonzero chamuyaya cha Mulungu, chimene chinachitika kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye athu. 12 Mwa Khristu ndi mwa chikhulupiriro chathu mwa Iye, timayandikira kwa Mulungu momasuka ndi molimbika mtima.

Mateyu 2:1-12

Anzeru a Kummawa

Atabadwa Yesu mʼBetelehemu wa ku Yudeya, mʼnthawi ya mfumu Herode, Anzeru a kummawa anabwera ku Yerusalemu nafunsa kuti, “Ali kuti amene wabadwa kukhala mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kummawa ndipo tabwera kudzamupembedza.”

Mfumu Herode atamva zimenezi, anavutika mu mtima kwambiri pamodzi ndi anthu onse a mu Yerusalemu. Ndipo anayitanitsa anthu onse, akulu ansembe ndi aphunzitsi amalamulo nawafunsa kuti, “Kodi Khristu adzabadwira kuti?” Ndipo anamuyankha kuti, “Ku Betelehemu wa ku Yudeya chifukwa izi ndi zimene mneneri analemba kuti,

“ ‘Koma iwe Betelehemu, chigawo cha Yudeya,
    sindiwe wamngʼonongʼono mwa olamulira a Yudeya;
pakuti otsogolera adzachokera mwa iwe,
    amene adzaweta anthu anga Aisraeli.’ ”

Pomwepo Herode anawayitanira mseri Anzeruwo nawafunsitsa nthawi yeniyeni yomwe nyenyeziyo inaoneka. Ndipo anawatumiza ku Betelehemu nawawuza kuti, “Pitani mukafufuze za mwanayo mosamalitsa. Ndipo mukamupeza mudzandiwuze kuti inenso ndikamupembedze.”

Atamva mawu a mfumu, ananyamuka ulendo wawo, ndipo taonani nyenyezi anayiona kummawa ija, inawatsogolera mpaka inayima pamwamba pa nyumba yomwe munali mwanayo. 10 Pamene iwo anaona nyenyeziyo, anasangalala kwambiri. 11 Pofika ku nyumbayo, anaona mwanayo pamodzi ndi amayi ake Mariya, ndipo anagwada namulambira Iye. Pomwepo anamasula chuma chawo ndi kupereka mphatso zawo za ndalama zagolide, lubani ndi mure. 12 Ndipo atachenjezedwa mʼmaloto kuti asapitenso kwa Herode, anabwerera ku dziko la kwawo podzera njira ina.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.