Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 96

96 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano;
    Imbirani Yehova dziko lonse lapansi.
Imbirani Yehova, tamandani dzina lake;
    lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko,
    ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.

Pakuti wamkulu ndi Yehova ndipo ndi woyenera kwambiri kumutamanda;
    ayenera kuopedwa kupambana milungu yonse.
Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano,
    koma Yehova analenga mayiko akumwamba.
Ulemu ndi ufumu zili pamaso pake,
    mphamvu ndi ulemerero zili mʼmalo ake opatulika.

Perekani kwa Yehova, inu mabanja a anthu a mitundu ina,
    perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake;
    bweretsani chopereka ndipo mulowe mʼmabwalo ake.
Lambirani Yehova mu ulemerero wa chiyero chake;
    njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi.

10 Nenani pakati pa mitundu ya anthu, “Yehova akulamulira.”
    Dziko lonse lakhazikika molimba, silingasunthidwe;
    Iye adzaweruza mitundu ya anthu molungama.
11 Mayiko akumwamba asangalale, dziko lapansi likondwere;
    nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo;
12     minda ikondwere pamodzi ndi chilichonse chili mʼmenemo.
Pamenepo mitengo yonse ya mʼnkhalango idzayimba ndi chimwemwe;
13     idzayimba pamaso pa Yehova,
    pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi;
adzaweruza dziko lonse mwachilungamo
    ndi mitundu ya anthu onse mʼchoonadi.

Zefaniya 3:8-13

Choncho mundidikire,” akutero Yehova,
    “chifukwa cha tsiku limene ndidzaperekera umboni.
Ndatsimikiza kusonkhanitsa pamodzi mitundu ya anthu,
    kusonkhanitsa maufumu
ndi kutsanulira ukali wanga pa iwo;
    mkwiyo wanga wonse woopsa.
Dziko lonse lidzatenthedwa
    ndi moto wa mkwiyo wa nsanje yanga.

“Pamenepo ndidzayeretsa milomo ya anthu a mitundu yonse
    kuti anthu onsewo ayitane dzina la Yehova
    ndi kumutumikira Iye pamodzi.
10 Kuchokera kutsidya kwa mitsinje ya ku Kusi
    anthu anga ondipembedza, omwazikana,
    adzandibweretsera zopereka.
11 Tsiku limenelo simudzachita manyazi
    chifukwa cha zoyipa zonse munandichitira,
popeza ndidzachotsa onse mu mzinda uwu
    amene amakondwera chifukwa cha kunyada kwawo.
Simudzakhalanso odzikuza
    mʼphiri langa lopatulika.
12 Koma ndidzasiya pakati panu
    anthu ofatsa ndi odzichepetsa,
    amene amadalira dzina la Yehova.
13 Aisraeli otsala sadzachitanso zolakwika;
    sadzayankhulanso zonama,
    ngakhale chinyengo sichidzatuluka mʼkamwa mwawo.
Adzadya ndi kugona
    ndipo palibe amene adzawachititse mantha.”

Aroma 10:5-13

Mose akulemba motere zachilungamo cha malamulo, “Munthu amene achita zinthu izi adzakhala ndi moyo pozichita.” Koma chilungamo cha chikhulupiriro chikuti, “Usanene mu mtima mwako kuti, ‘Kodi ndani amene akwere kumwamba?’ ” (ndiko, kukatsitsa Khristu) “kapena ‘Ndani adzatsikira ku dziko la anthu akufa?’ ” (ndiko, kukamutenga Khristu kwa akufa). Nanga akuti chiyani? “Mawu ali pafupi ndi inu. Ali mʼkamwa mwanu ndi mu mtima mwanu.” Ndiwo mawu achikhulupiriro amene ife tikuwalalikira, kuti ngati udzavomereza ndi pakamwa pako kuti, “Yesu ndiye Ambuye,” ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. 10 Pakuti ndi mtima wanu mukhulupirira ndi kulungamitsidwa, ndipo ndi pakamwa panu muvomereza ndi kupulumutsidwa. 11 Pakuti Malemba akuti, “Aliyense amene akhulupirira Iye, sadzachititsidwa manyazi.” 12 Pakuti palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina, pakuti Ambuye mmodzi yemweyo ndi Ambuye wa onse ndipo amadalitsa mochuluka onse amene ayitana pa Iye 13 pakuti, “Aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.