Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 89:1-4

Ndakatulo ya Etani, wa banja la Ezara.

89 Ndidzayimba za chikondi chachikulu cha Yehova kwamuyaya;
    ndi pakamwa panga ndidzachititsa kuti kukhulupirika kwanu kudziwike ku mibado yonse.
Ndidzalalikira kuti chikondi chanu chidzakhazikika mpaka muyaya,
    kuti Inu munakhazikitsa kukhulupirika kwanu kumwamba kwenikweniko.

Inu munati, “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga,
    ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga kuti,
‘Ndidzakhazikitsa zidzukulu zako mpaka muyaya.
    Ndidzachititsa kuti mpando wako waufumu ukhazikike ku mibado yonse,’ ”
            Sela.

Masalimo 89:19-26

19 Kale munayankhula mʼmasomphenya,
    kwa anthu anu okhulupirika munati,
“Ndapatsa mphamvu wankhondo;
    ndakweza mnyamata wochokera pakati pa anthu.
20 Ndamupeza mtumiki wanga Davide;
    ndamudzoza ndi mafuta opatulika.
21 Dzanja langa lidzamuchirikiza;
    zoonadi, mkono wanga udzamupatsa mphamvu.
22 Adani sadzamulamula kuti apereke msonkho;
    anthu oyipa sadzamusautsa.
23 Ndidzaphwanya adani ake pamaso pake
    ndi kukantha otsutsana naye.
24 Chikondi changa chokhulupirika chidzakhala naye,
    ndipo kudzera mʼdzina langa nyanga yake idzakwezedwa.
25 Ndidzayika dzanja lake pa nyanja,
    dzanja lake lamanja pa mitsinje.
26 Iyeyo adzafuwula kwa Ine kuti, ‘Ndinu Atate anga,
    Mulungu wanga, Thanthwe ndi Chipulumutso changa.’

2 Samueli 6:1-11

Bokosi la Chipangano Libwera ku Yerusalemu

Davide anasonkhanitsanso pamodzi ankhondo 3,000 osankhidwa pakati pa Aisraeli. Iye pamodzi ndi ankhondo ake onse anapita ku Baalahi ku Yuda kukatenga Bokosi la Chipangano la Mulungu, limene limadziwika ndi Dzina lake, dzina la Yehova Wamphamvuzonse, amene amakhala pakati pa Akerubi amene ali pa Bokosi la Chipanganolo. Iwo anayika Bokosi la Mulungu pa ngolo yatsopano nachoka nalo ku nyumba ya Abinadabu, imene inali pa phiri. Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu ndiwo ankayendetsa ngolo yatsopanoyo, imene inanyamula Bokosi la Mulungu, ndipo Ahiyo mwana wa Abinadabu ankayenda patsogolo pake. Davide pamodzi ndi Aisraeli onse ankakondwerera ndi mphamvu zawo zonse pamaso pa Yehova poyimba nyimbo pogwiritsa ntchito azeze, apangwe, matambolini, maseche ndi malipenga.

Atafika pa malo opunthira tirigu a Nakoni, Uza anatambalitsa dzanja lake kuti agwire Bokosi la Mulungu, chifukwa ngʼombe zinkafuna kugwa. Yehova anapsera mtima Uza chifukwa chochita chinthu chosayenera kuchitika. Choncho Mulungu anamukantha ndipo anafera pomwepo pambali pa Bokosi la Mulungulo.

Ndipo Davide anakhumudwa chifukwa Yehova anakantha Uza ndipo mpaka lero malowo amatchedwa Perezi Uza.

Tsiku limenelo Davide anachita mantha ndi Yehova ndipo anati, “Kodi Bokosi la Yehova lingafike bwanji kwathu?” 10 Iye sanafunenso kubwera ndi Bokosi la Yehova kawo ku mzinda wake wa Davide. Mʼmalo mwake anapita nalo ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti. 11 Bokosi la Yehova linakhala mʼnyumba ya Obedi-Edomu Mgiti kwa miyezi itatu, ndipo Yehova anamudalitsa kwambiri iyeyo ndi banja lake lonse.

Ahebri 1:1-4

Khristu Mwana wa Mulungu Aposa Angelo

Kale lija Mulungu ankayankhula ndi makolo athu pa nthawi zosiyanasiyana ndiponso mwa njira zosiyanasiyana kudzera mwa aneneri. Koma masiku otsiriza ano, Mulungu wayankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Mwanayu anamusankha kuti akhale mwini wa zinthu zonse, ndiponso Mulungu analenga dziko lonse kudzera mwa Iye. Mwanayo ndiye kuwala kwa ulemerero wa Mulungu, chithunzithunzi chenicheni cha khalidwe lake. Iyeyu amachirikiza zinthu zonse ndi mphamvu ya mawu ake. Iye atayeretsa anthu kuchoka ku machimo awo, anakhala pansi kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu waulemerero. Mwanayu ndi wamkulu koposa angelo, monga momwe dzina limene analandira limaposa dzina la angelo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.