Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
125 Amene amadalira Yehova ali ngati phiri la Ziyoni,
limene silingagwedezeke koma ndi lokhala mpaka muyaya.
2 Monga mapiri azungulira Yerusalemu,
momwemonso Yehova azungulira anthu ake
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
3 Ndodo yaufumu ya anthu oyipa sidzakhala
pa dziko limene lapatsidwa kwa anthu olungama,
kuti anthu olungamawo
angachite nawonso zoyipa.
4 Yehova chitirani zabwino amene ndi abwino,
amene ndi olungama mtima
5 Koma amene amatembenukira ku njira zokhotakhota,
Yehova adzawachotsa pamodzi ndi anthu ochita zoyipa.
Mtendere ukhale pa Israeli.
16 Ndipo woopa Yehova anayamba kukambirana, ndipo Yehova anamvetsera. Buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, lonena za amene amaopa Yehova ndi kulemekeza dzina lake.
17 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu amenewo adzakhala anga, tsiku limene Ine ndidzachita izi, adzakhala angaanga. Ndidzawaleka osawalanga monga mmene munthu amachitira chifundo mwana wake amene amamutumikira. 18 Pamenepo mudzaonanso kusiyana pakati pa anthu olungama ndi oyipa, pakati pa amene amatumikira Mulungu ndi amene satumikira Mulungu.”
Tsiku la Yehova
4 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndithu tsiku likubwera; lidzayaka ngati ngʼanjo. Anthu onse odzikuza, ndi aliyense ochita zoyipa adzapsa ngati chiputu, ndipo pa tsiku limene likubweralo adzapserera ndi moto. Sipadzatsalira muzu kapena nthambi. 2 Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani. Ndipo inu mudzatuluka ndi kulumphalumpha ngati ana angʼombe amene atulutsidwa mʼkhola. 3 Tsiku limenelo inu mudzapondereza anthu oyipa; adzakhala phulusa ku mapazi anu pa tsiku limene Ine ndidzachite zinthu zimenezi,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
4 Kumbukirani zophunzitsa za mtumiki wanga Mose, malamulo ndi malangizo amene ndinamupatsa pa Horebu kuti awuze Aisraeli onse.
5 “Taonani, ndidzakutumizirani mneneri Eliya lisanafike tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova. 6 Iye adzabweza mitima ya makolo kwa ana awo, ndi mitima ya ana kwa makolo awo. Kupanda kutero ndidzabwera kudzakantha dziko lanu ndi temberero.”
9 Pamene ankatsika kuchokera ku phiri, Yesu anawalamulira kuti asawuze aliyense zimene anaona mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa. 10 Iwo anayisunga nkhaniyo nakambirana za tanthauzo lake la “Kuuka kwa akufa.”
11 Ndipo anamufunsa Iye kuti, “Nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amati Eliya ayenera kuyamba wabwera?”
12 Yesu anayankha kuti, “Kunena motsimikiza, Eliya ayeneradi kuyamba kubwera kudzakonzanso zinthu zonse. Nʼchifukwa chiyani tsono zinalembedwa, kuti Mwana wa Munthu ayenera kuvutika kwambiri ndi kukanidwa? 13 Koma ndikuwuzani, kuti Eliya wabweradi, ndipo amuchitira iye zonse zimene iwo anafuna, monga momwe zalembedwera za iye.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.