Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 80:1-7

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Salimo la Asafu.

80 Tcherani khutu Inu mʼbusa wa Israeli,
    Inu amene mumatsogolera Yosefe monga nkhosa;
Inu amene mumakhala pa mpando waufumu pakati pa akerubi, walani
    kwa Efereimu, Benjamini ndi Manase.
Utsani mphamvu yanu;
    bwerani ndi kutipulumutsa.

Tibwezereni mwakale Inu Mulungu;
    nkhope yanu itiwalire
    kuti tipulumutsidwe.

Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
    mpaka liti mkwiyo wanu udzanyeka
    kutsutsana ndi mapemphero a anthu anu?
Mwawadyetsa buledi wa misozi;
    mwachitisa iwo kumwa misozi yodzaza mbale.
Mwachititsa kuti tikhale gwero la mikangano pakati pa anansi athu,
    ndipo adani athu akutinyoza.

Tibwezereni mwakale Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
    nkhope yanu itiwalire
    kuti tipulumutsidwe.

Masalimo 80:17-19

17 Dzanja lanu likhale pa munthu amene ali ku dzanja lanu lamanja,
    mwana wa munthu amene mwalera nokha.
18 Ndipo ife sitidzatembenukira kumbali kuchoka kwa Inu;
    titsitsimutseni ndipo tidzayitana pa dzina lanu.

19 Tibwezereni mwakale Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse
    nkhope yanu itiwalire
    kuti tipulumutsidwe.

Zekariya 13

Kuyeretsedwa ku Tchimo

13 “Pa tsiku limenelo nyumba ya Davide adzayitsekulira kasupe wa madzi pamodzi ndi okhala mu Yerusalemu, kuti awachotsere tchimo lawo ndi chodetsa chawo.

“Pa tsiku limenelo, ndidzafafaniziratu mayina a mafano mʼdziko, ndipo sadzawakumbukiranso,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndidzachotsa mʼdziko aneneri pamodzi ndi mzimu wonyansa. Ndipo ngati wina aliyense adzafuna kunenera, abambo ndi amayi ake amene anamubereka, adzamuwuza kuti, ‘Uyenera kufa, chifukwa wayankhula bodza mʼdzina la Yehova.’ Pamene anenera, makolo ake omwe adzamubaya.

“Pa tsiku limenelo mneneri aliyense adzachita manyazi chifukwa cha masomphenya ake. Sadzavala chovala chake chaubweya ndi cholinga chonamiza anthu. Iye adzati, ‘Sindine mneneri. Ndine mlimi; ndakhala ndi kulima munda kuyambira ubwana wanga.’ Ngati wina adzamufunsa, ‘Zilonda zili mʼthupi lakoli ndi chiyani?’ Iye adzayankha kuti, ‘Zilondazi ndinazilandira mʼnyumba ya abwenzi anga.’

Kukantha Mʼbusa, Nkhosa Kubalalika

“Dzambatuka iwe lupanga, ukanthe mʼbusa wanga,
    ukanthe munthu amene ali pafupi ndi Ine!”
    akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Kantha mʼbusa
    ndipo nkhosa zidzabalalika,
    ndipo ndidzatambalitsa dzanja langa kuwononga zazingʼono.
Mʼdziko monse, akutero Yehova Wamphamvuzonse,
    “zigawo ziwiri mwa zigawo zitatu za anthu zidzakanthidwa ndi kuwonongeka;
    koma chigawo chimodzi chidzatsala mʼdzikomo.
Chigawo chachitatuchi ndidzachiyika pa moto;
    ndidzawayeretsa monga momwe amayeretsera siliva
    ndi kuwayesa monga momwe amayesera golide.
Adzayitana pa dzina langa
    ndipo Ine ndidzawayankha;
Ine ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’
    ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndiye Mulungu wathu.’ ”

Chivumbulutso 14:6-13

Angelo Atatu

Kenaka ndinaona mngelo wina akuwuluka mu mlengalenga ndipo anali ndi Uthenga Wabwino wamuyaya woti akalalikire kwa anthu okhala pa dziko lapansi, kwa a mtundu uliwonse, a fuko lililonse, a chiyankhulo chilichonse ndi kwa anthu onse. Mngeloyo anayankhula mokweza mawu kuti, “Wopani Mulungu ndi kumutamanda, chifukwa nthawi yoweruza anthu yafika. Mumupembedze Iye amene analenga thambo, dziko lapansi, nyanja ndi akasupe amadzi.”

Mngelo wachiwiri anatsatana naye ndipo anati, “Wagwa! Wagwa Babuloni womveka uja, amene anachititsa anthu a mitundu yonse kumwa vinyo wa zilakolako zake zachigololo.”

Mngelo wachitatu anatsatana nawo ndi mawu ofuwula anati, “Ngati wina apembedza chirombo chija ndi fano lake ndi kulembedwa chizindikiro pa mphumi kapena pa dzanja, 10 nayenso adzamwa vinyo waukali wa Mulungu, umene wathiridwa popanda kuchepetsa mphamvu zake mʼchikho cha ukali wa Mulungu. Munthuyo adzazunzidwa ndi moto wamiyala yasulufure pamaso pa angelo oyera ndi pa Mwana Wankhosa. 11 Ndipo utsi wa moto wowazunzawo udzakwera kumwamba mpaka muyaya. Sikudzakhala kupumula usana ndi usiku kwa amene anapembedza chirombo chija ndi fano lake kapena kwa aliyense amene analembedwa chizindikiro cha dzina lake lija.” 12 Pamenepa ndi pofunika kupirira kwa anthu oyera mtima amene amasunga malamulo a Mulungu ndi kukhalabe okhulupirika kwa Yesu.

13 Kenaka ndinamva mawu kuchokera kumwamba akuti, “Lemba kuti, Odala anthu amene akufa ali mwa Ambuye kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo.”

“Inde,” akutero Mzimu, “akapumule ntchito zawo zotopetsa pakuti ntchito zawo zidzawatsata.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.