Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide.
28 Kwa Inu ine ndiyitana, Yehova ndinu Thanthwe langa;
musakhale osamva kwa ine.
Pakuti mukapitirira kukhala chete,
ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.
2 Imvani kupempha chifundo kwanga
pomwe ndikuyitana kwa Inu kuti mundithandize,
pomwe ndikukweza manja anga
kuloza ku malo anu oyeretsetsa.
3 Musandikokere kutali pamodzi ndi anthu oyipa,
pamodzi ndi iwo amene amachita zoyipa,
amene amayankhula mwachikondi ndi anzawo
koma akusunga chiwembu mʼmitima mwawo.
4 Muwabwezere chifukwa cha zochita zawo
ndi ntchito zawo zoyipa;
abwezereni chifuwa cha zimene manja awo achita
ndipo mubweretse pa iwo zimene zowayenera.
5 Popeza iwowo sakhudzidwa ndi ntchito za Yehova,
ndi zimene manja ake anazichita,
Iye adzawakhadzula
ndipo sadzawathandizanso.
6 Matamando apite kwa Yehova,
popeza Iye wamva kupempha chifundo kwanga.
7 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa;
mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa.
Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe
ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.
8 Yehova ndi mphamvu ya anthu ake,
linga la chipulumutso kwa wodzozedwa wake.
9 Pulumutsani anthu anu ndipo mudalitse cholowa chanu;
mukhale mʼbusa wawo ndipo muwakweze kwamuyaya.
10 “Imvani mawu a Yehova inu anthu a mitundu ina;
lalikirani mawuwa kwa anthu a mayiko akutali a mʼmbali mwa nyanja;
‘Iye amene anabalalitsa Israeli adzawasonkhanitsanso
ndipo adzayangʼanira nkhosa zake ngati mʼbusa.’
11 Pakuti Yehova wawombola fuko la Yakobo
anawapulumutsa mʼdzanja la anthu owaposa mphamvu.
12 Anthuwo adzabwera akuyimba mofuwula pa mapiri a Ziyoni;
adzasangalala ndi zinthu zabwino zochokera kwa Yehova.
Zinthu zabwinozo ndi izi: tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta,
ana ankhosa ndi ana angʼombe.
Iwo adzakhala ngati munda wothiriridwa bwino,
ndipo sadzamvanso chisoni.
13 Pamenepo anamwali adzavina ndi kusangalala.
Anyamata ndi okalamba nawonso adzasangalala.
Kulira kwawo ndidzakusandutsa chisangalalo;
ndidzawasangalatsa nʼkuchotsa chisoni chawo.
14 Ansembe ndidzawadyetsa chakudya chabwino,
ndipo anthu anga adzakhuta ndi zabwino zanga,”
akutero Yehova.
19 Yesu anawapatsa yankho ili: “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Mwana sangathe kuchita kanthu pa Iye yekha. Iye amachita zokhazo zimene amaona Atate ake akuchita, chifukwa chilichonse chimene Atate amachita Mwana amachitanso. 20 Pakuti Atate amakonda Mwana, amamuonetsa zonse zimene Iwo amachita. Inde, Atate adzamuonetsa zinthu zazikulu kuposa zimenezi ndipo mudzadabwa. 21 Pakuti monga Atate amaukitsa akufa nawapatsa moyo, momwemonso Mwana amapereka moyo kwa amene Iye akufuna. 22 Komanso, Atate saweruza aliyense koma wapereka kwa Mwana ulamuliro woweruzawo, 23 kuti aliyense alemekeze Mwanayo monga momwe amalemekezera Atate. Munthu amene salemekeza Mwana salemekezanso Atate amene anamutuma Mwanayo.
24 “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo. 25 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo iwo amene amva adzakhala ndi moyo. 26 Pakuti monga Atate ali gwero la moyo, momwemonso anapereka mphamvu zopereka moyo mwa Mwana. 27 Ndipo wamupatsa Iye ulamuliro woweruza chifukwa ndi Mwana wa Munthu.
28 “Musadabwe ndi zimenezi. Pakuti nthawi ikubwera pamene onse amene ali mʼmanda adzamva mawu ake 29 ndi kutuluka. Iwo amene anachita zabwino adzauka ndi kupita ku moyo wosatha ndipo amene anachita zoyipa adzauka ndi kupita ku chilango chamuyaya. 30 Pakuti sindingathe kuchita kena kalikonse pa ndekha. Ine ndimaweruza molingana ndi zomwe Mulungu wandiwuza ndipo kuweruza kwanga ndi kolungama. Ine sindifuna kudzikondweretsa ndekha koma Iye amene anandituma.
Maumboni Onena za Yesu
31 “Ngati ndidzichitira umboni ndekha, umboni wanga si woona. 32 Alipo wina amene amandichitira umboni wabwino. Ine ndikudziwa kuti umboni wake wonena za Ine ndi woona.
33 “Inu munatumiza amithenga kwa Yohane ndipo iye anachitira umboni choona. 34 Sikuti Ine ndikudalira umboni wa munthu; koma ndikunena zimenezi kuti mupulumutsidwe. 35 Yohane anali ngati nyale imene imayaka ndi kuwala, ndipo inu kwa kanthawi munasankha kusangalala ndi kuwala kwakeko.
36 “Koma Ine ndili ndi umboni woposa uja wa Yohane. Pakuti ntchito imene Atate andipatsa kuti ndiyikwaniritse ndi imene ndikugwira, ndipo ikundichitira umboni kuti Atate andituma Ine. 37 Ndipo Atate amene anandituma Ine, Iye mwini wandichitira umboni. Inu simunamvepo mawu ake kapena kuona maonekedwe ake, 38 kapena mawu ake kukhala mwa inu, pakuti simukhulupirira Iye amene anamutuma. 39 Inu mumasanthula malemba chifukwa mumaganiza kuti mʼmalembamo muli moyo wosatha. Awa ndi malemba amene akundichitira umboni. 40 Koma inu mukukana kubwera kwa Ine kuti mukhale ndi moyo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.