Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 28

Salimo la Davide.

28 Kwa Inu ine ndiyitana, Yehova ndinu Thanthwe langa;
    musakhale osamva kwa ine.
Pakuti mukapitirira kukhala chete,
    ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.
Imvani kupempha chifundo kwanga
    pomwe ndikuyitana kwa Inu kuti mundithandize,
pomwe ndikukweza manja anga
    kuloza ku malo anu oyeretsetsa.

Musandikokere kutali pamodzi ndi anthu oyipa,
    pamodzi ndi iwo amene amachita zoyipa,
amene amayankhula mwachikondi ndi anzawo
    koma akusunga chiwembu mʼmitima mwawo.
Muwabwezere chifukwa cha zochita zawo
    ndi ntchito zawo zoyipa;
abwezereni chifuwa cha zimene manja awo achita
    ndipo mubweretse pa iwo zimene zowayenera.
Popeza iwowo sakhudzidwa ndi ntchito za Yehova,
    ndi zimene manja ake anazichita,
Iye adzawakhadzula
    ndipo sadzawathandizanso.

Matamando apite kwa Yehova,
    popeza Iye wamva kupempha chifundo kwanga.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa;
    mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa.
Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe
    ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.

Yehova ndi mphamvu ya anthu ake,
    linga la chipulumutso kwa wodzozedwa wake.
Pulumutsani anthu anu ndipo mudalitse cholowa chanu;
    mukhale mʼbusa wawo ndipo muwakweze kwamuyaya.

Zekariya 11:4-17

Abusa Awiri

Yehova Mulungu wanga akuti, “Dyetsa nkhosa zimene zikukaphedwa. Amene amagula nkhosazo amazipha ndipo salangidwa. Amene amazigulitsa amanena kuti, ‘Alemekezeke Yehova, ine ndalemera!’ Abusa ake omwe sazimvera chisoni nkhosazo. Pakuti Ine sindidzamveranso chisoni anthu okhala mʼdziko,” akutero Yehova. “Ndidzapereka munthu aliyense mʼmanja mwa mnansi wake ndi mwa mfumu yake. Iwo adzazunza dziko, ndipo Ine sindidzawapulumutsa mʼmanja mwawo.”

Choncho ine ndinadyetsa nkhosa zokaphedwa, makamaka nkhosa zoponderezedwa. Pamenepo ndinatenga ndodo ziwiri ndipo yoyamba ndinayitcha Kukoma mtima ndipo yachiwiri ndinayitcha Umodzi ndipo ndinadyetsa nkhosazo. Pa mwezi umodzi ndinachotsa abusa atatu.

Abusawo anadana nane, ndipo ndinatopa nawo. Ndinawuza gulu la nkhosalo kuti, “Sindidzakhalanso mʼbusa wanu. Imene ikufa, ife, ndipo imene ikuwonongeka, iwonongeke, zimene zatsala zizidyana.”

10 Kenaka ndinatenga ndodo yanga yotchedwa Kukoma mtima ndi kuyithyola, kuphwanya pangano limene ndinachita ndi mitundu yonse ya anthu. 11 Linaphwanyidwa tsiku limenelo ndipo nkhosa zosautsidwa zimene zimandiyangʼanitsitsa zinadziwa kuti anali mawu a Yehova.

12 Ndinawawuza kuti, “Ngati mukuganiza kuti zili bwino, patseni malipiro anga; koma ngati si choncho, sungani malipirowo.” Kotero anandipatsa ndalama zasiliva makumi atatu.

13 Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Ziponye kwa wowumba mbiya,” mtengo woyenera umene anapereka pondigula Ine! Choncho ndinatenga ndalama zasiliva makumi atatu ndi kuziponya mʼnyumba ya Yehova kwa wowumba mbiya.

14 Kenaka ndinathyola ndodo yanga yachiwiri yotchedwa Umodzi, kuthetsa ubale pakati pa Yuda ndi Israeli.

15 Pamenepo Yehova anayankhula nane kuti, “Tenganso zida za mʼbusa wopusa. 16 Pakuti ndidzawutsa mʼbusa mʼdzikomo amene sadzasamalira zotayika, kapena kufunafuna zazingʼono, kapena zovulala, kapena kudyetsa nkhosa zabwino, koma iye adzadya nyama ya nkhosa zonenepa, nʼkumakukuta ndi ziboda zomwe.

17 “Tsoka kwa mʼbusa wopandapake,
    amene amasiya nkhosa!
Lupanga limukanthe pa mkono wake ndi pa diso lake lakumanja!
    Mkono wake ufote kotheratu,
    diso lake lamanja lisaonenso.”

Chivumbulutso 19:1-9

Babuloni Wagwa, Haleluya!

19 Zitatha izi, ndinamva chimene chinamveka ngati phokoso la gulu lalikulu mmwamba likufuwula kuti,

“Haleluya!
Chipulumutso ndi ulemerero ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu,
    pakuti chiweruzo chake ndi choona ndi cha chilungamo.
Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja
    amene anayipitsa dziko lonse lapansi ndi zigololo zake.
Iye wabwezera pa mkaziyo magazi a atumiki ake.”

Ndipo anafuwulanso kuti,

“Haleluya!
Utsi wochokera kwa mkazi wadamayo udzakwera kumwamba mpaka muyaya.”

Akuluakulu 24 aja ndi zamoyo zinayi zija anadzigwetsa pansi kupembedza Mulungu amene anakhala pa mpando waufumu. Ndipo anafuwula kuti,

“Ameni, Haleluya!”

Kenaka mawu anachoka ku mpando waufumu kuti,

“Lemekezani Mulungu wathu
    inu nonse atumiki ake,
inu amene mumamuopa,
    nonse angʼono ndi akulu!”

Kenaka ndinamva chimene chinamveka ngati gulu lalikulu, ngati mkokomo wamadzi othamanga ndipo ngati kugunda kwakukulu kwa bingu, ndipo anati,

“Haleluya!
    Pakuti Ambuye Mulungu wathu Wamphamvuzonse akulamulira.
Tiyeni tisangalale ndi kukondwera
    ndi kumutamanda!
Pakuti nthawi ya ukwati wa Mwana Wankhosa yafika,
    ndipo Mkwatibwi wakonzekeratu.
Wapatsidwa nsalu yoyera kwambiri, yowala ndi yosada
    kuti avale.”

(Nsalu yoyera kwambiri ikuyimira ntchito zolungama za oyera mtima).

Kenaka mngelo anandiwuza kuti, “Lemba kuti, Odala amene ayitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwana Wankhosa.” Ndipo anatinso, “Awa ndiwo mawu woona a Mulungu.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.