Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 100

Salimo. Nyimbo yothokoza.

100 Fuwulani kwa Yehova mwachimwemwe, inu dziko lonse lapansi.
    Mulambireni Yehova mosangalala;
    bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero.
Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu.
    Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake;
    ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake.

Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko
    ndi ku mabwalo ake ndi matamando;
    muyamikeni ndi kutamanda dzina lake.
Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya;
    kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.

Genesis 48:15-22

15 Kenaka anadalitsa Yosefe nati,

“Mulungu amene makolo anga
    Abrahamu ndi Isake anamutumikira,
Mulungu amene wakhala ali mʼbusa wanga
    moyo wanga wonse kufikira lero,
16 mngelo amene wandipulumutsa ine ku zovuta zonse,
    ameneyo adalitse anyamata awa.
Kudzera mwa iwowa
    dzina langa ndi mayina a makolo anga, Abrahamu ndi Isake, adzamveka.
Iwowa adzakhala ndi ana ambiri nadzasanduka mtundu waukulu
    pa dziko lapansi.”

17 Yosefe ataona kuti abambo ake ayika dzanja lamanja pa Efereimu, sanakondwere. Choncho anagwira dzanja la abambo ake kuti alichotse pamutu pa Efereimu ndi kuliyika pamutu pa Manase, 18 nati kwa abambo ake, “Ayi, abambo anga, uyu ndiye woyamba kubadwa, ikani dzanja lanu lamanja pamutu pake.”

19 Koma abambo ake anakana nati, “Ndikudziwa, mwana wanga, ndikudziwa. Adzukulu a iyeyunso adzakhala mtundu waukulu. Komabe mʼbale wake wamngʼonoyu adzakhala wamkulu kuposa iye, ndipo zidzukulu zake zidzakhala mitundu yayikulu ya anthu.” 20 Tsono iye anawadalitsa tsiku limenelo nati,

“Aisraeli adzagwiritsa ntchito dzina lanu podalitsa nadzati:
    Mulungu akudalitseni monga Efereimu ndi Manase.”

Choncho anayika Efereimu patsogolo pa Manase.

21 Kenaka Israeli anati kwa Yosefe, “Ine ndatsala pangʼono kufa, koma Mulungu adzakhala ndipo adzakutenganinso kubwerera nanu ku dziko la makolo anu. 22 Ndiponso iwe wekha ndikupatsa moposera abale ako, malo woonjezera, Sekemu, malo amene ndinalanda kwa Aamori ndi lupanga ndi uta wanga.”

Chivumbulutso 14:1-11

Mwana Wankhosa ndi Anthu 144,000

14 Kenaka ndinaona patsogolo panga panali Mwana Wankhosa, atayimirira pa Phiri la Ziyoni, ndipo Iye anali pamodzi ndi anthu 144,000 amene pa mphumi pawo panalembedwa dzina la Mwana Wankhosayo ndi la Atate ake. Ndipo ndinamva liwu lochokera kumwamba ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Liwu limene ndinamvalo linali ngati a anthu akuyimba azeze awo. Anthuwo ankayimba nyimbo yatsopano patsogolo pa mpando waufumu ndi zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu aja. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatha kuphunzira nyimboyo kupatula anthu 144,000 aja amene anawomboledwa pa dziko lapansi. Awa ndiwo amene sanadzidetse koma anadzisunga ndipo sanadziyipitse ndi akazi. Anthu amenewa ndiwo ankatsatira Mwana Wankhosa kulikonse kumene ankapita. Ndiwo amene anagulidwa pakati pa anthu a dziko lapansi kuti akhale oyambirira kuperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwana Wankhosa. Iwo sananenepo bodza ndipo alibe cholakwa.

Angelo Atatu

Kenaka ndinaona mngelo wina akuwuluka mu mlengalenga ndipo anali ndi Uthenga Wabwino wamuyaya woti akalalikire kwa anthu okhala pa dziko lapansi, kwa a mtundu uliwonse, a fuko lililonse, a chiyankhulo chilichonse ndi kwa anthu onse. Mngeloyo anayankhula mokweza mawu kuti, “Wopani Mulungu ndi kumutamanda, chifukwa nthawi yoweruza anthu yafika. Mumupembedze Iye amene analenga thambo, dziko lapansi, nyanja ndi akasupe amadzi.”

Mngelo wachiwiri anatsatana naye ndipo anati, “Wagwa! Wagwa Babuloni womveka uja, amene anachititsa anthu a mitundu yonse kumwa vinyo wa zilakolako zake zachigololo.”

Mngelo wachitatu anatsatana nawo ndi mawu ofuwula anati, “Ngati wina apembedza chirombo chija ndi fano lake ndi kulembedwa chizindikiro pa mphumi kapena pa dzanja, 10 nayenso adzamwa vinyo waukali wa Mulungu, umene wathiridwa popanda kuchepetsa mphamvu zake mʼchikho cha ukali wa Mulungu. Munthuyo adzazunzidwa ndi moto wamiyala yasulufure pamaso pa angelo oyera ndi pa Mwana Wankhosa. 11 Ndipo utsi wa moto wowazunzawo udzakwera kumwamba mpaka muyaya. Sikudzakhala kupumula usana ndi usiku kwa amene anapembedza chirombo chija ndi fano lake kapena kwa aliyense amene analembedwa chizindikiro cha dzina lake lija.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.