Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nyimbo. Salimo la Asafu.
83 Inu Mulungu musakhale chete;
musangoti phee, Mulungu musangoti duu.
2 Onani adani anu akuchita chiwawa,
amene amadana nanu autsa mitu yawo.
3 Mochenjera iwo akukambirana za chiwembu kutsutsana ndi anthu anu;
Iwo akukonzekera kutsutsana ndi omwe mumawakonda.
4 Iwo akunena kuti, “Bwerani” akutero, “Tiyeni tiwononge mtundu wonsewu
kuti dzina la Israeli lisakumbukikenso.”
9 Muwachitire zomwe munachitira Amidiyani,
monga munachitira Sisera ndi Yabini ku mtsinje wa Kisoni.
10 Amene anawonongedwa ku Endori
ndi kukhala ngati zinyalala.
17 Achite manyazi ndi mantha nthawi zonse;
awonongeke mwa manyazi.
18 Adziwe kuti Inu amene dzina lanu ndi Yehova,
ndinu nokha Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi.
Hamani Aphedwa
7 Choncho mfumu ndi Hamani anabwera kudzadya phwando la mfumukazi Estere. 2 Pa tsiku lachiwiri akumwa vinyo, mfumu inafunsanso kuti, “Kodi iwe mfumukazi Estere, chimene ufuna kupempha nʼchiyani? Chimene uti upemphe ndidzakupatsa. Choncho ukufuna chiyani? Ngakhale utafuna theka la ufumu ndidzakupatsa.”
3 Kenaka mfumukazi Estere anayankha kuti, “Ngati mwandikomera mtima, inu mfumu, ndipo ngati chingakukomereni mfumu, pempho ndi chokhumba changa ndi ichi, mulole kuti ine ndi abale anga tisungidwe tonse ndi moyo. 4 Popeza ine ndi anthu a mtundu wanga tagulitsidwa kuti atiwononge, atiphe ndi kutifafaniziratu. Akanangotigulitsa kokha tikanakhala chete, chifukwa chimene mdani wathuyo akanakupatsani mfumu sibwenzi mutasowa nacho mtendere.”
5 Mfumu Ahasiwero anamufunsa mfumukazi Estere, “Kodi iyeyu ndi ndani ndipo ali kuti amene saopa kuchita chinthu chotere?”
6 Estere anati, “Wotizunza ndiponso mdani wathu! Munthu woyipayo ndi Hamani.”
Kenaka Hamani anagwidwa ndi mantha pamaso pa mfumu ndi mfumukazi. 7 Mfumu itakwiya kwambiri inanyamuka pa phwando nipita ku munda wa maluwa wa nyumba yaufumu. Koma Hamani, pozindikira kuti mfumu yaganiza kale kumuchitira choyipa, anatsalira mʼnyumba kupempha Estere kuti apulumutse moyo wake.
8 Mfumu itabwerera kuchokera ku munda wa maluwa wa nyumba yaufumu uja ndi kulowanso mʼchipinda chaphwando, anapeza Hamani atagona chafufumimba pa mpando wa khutagone pomwe Estere anakhalapo.
Mfumu inayankhula mokweza kuti, “Kodi afunanso kuvula mfumukazi momukakamiza pamene ine ndili mʼnyumba?”
Mfumu isanatsirize kuyankhula mawu awa, atumiki ake anaphimba nkhope ya Hamani. 9 Haribona, mmodzi wa adindo ofulidwa amene ankatumikira mfumu anati, “Mtanda wotalika mamita 23 uli mʼnyumba ya Hamani. Mtandawu, Hamani anapangira Mordekai, uja amene anapulumutsa mfumu ku chiwembu.”
Mfumu inati, “Mpachikeni pamenepo!” 10 Choncho anamupachika Hamani pa mtanda umene anakonzera Mordekai. Kenaka mkwiyo wa mfumu unatsika.
Wantchito Wokhulupirika ndi Wosakhulupirika
45 “Kodi wantchito wokhulupirika ndi wanzeru amene ambuye ake anamuyika kukhala woyangʼanira antchito a mʼnyumba kuti awapatse chakudya chawo pa nthawi yake ndani? 46 Chidzakhala chabwino kwa wantchitoyo ngati mbuye wake pofika adzamupeza akuchita zimenezi. 47 Zoonadi, ndikuwuzani kuti adzamuyika kukhala woyangʼanira katundu wake yense. 48 Koma tiyerekeze kuti wantchitoyo ndi woyipa, nati kwa iye yekha, ‘Mbuye wanga akuchedwa kubwera,’ 49 nayamba kumenya antchito anzake, nadya ndi kumwa ndi zidakwa. 50 Mbuye wa wantchitoyo adzabwera pa tsiku limene iye samamuyembekezera ndi pa nthawi imene iye sakuyidziwa. 51 Adzamulanga koopsa ndipo adzamuyika kokhala anthu achiphamaso, kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.