Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
123 Ndikweza maso anga kwa Inu,
kwa Inu amene mumakhala kumwamba.
2 Taonani, monga momwe maso a akapolo amayangʼana mʼdzanja la mbuye wawo,
monga momwenso maso a mdzakazi amayangʼana mʼdzanja la dona wake,
choncho maso athu ali kwa Yehova Mulungu wathu,
mpaka atichitire chifundo.
3 Mutichitire chifundo, Inu Yehova mutichitire chifundo,
pakuti tapirira chitonzo chachikulu.
4 Ife tapirira mnyozo wambiri kuchokera kwa anthu odzikuza,
chitonzo chachikulu kuchokera kwa anthu onyada.
16 Choncho Yehova anawawutsira atsogoleri amene ankawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amene ankasakaza zinthu zawo. 17 Komabe iwo sanawamvere atsogoleri awowo popeza ankapembedza milungu ina ndi kumayigwadira. Iwo anapatuka msangamsanga mu njira imene ankayendamo makolo awo. Iwo aja ankamvera malamulo a Yehova, koma mʼbado uwu ayi. 18 Nthawi zonse Yehova akawautsira mtsogoleri, Iye amakhala naye, ndipo mtsogoleriyo ankawapulumutsa Aisraeliwo mʼmanja mwa adani awo mʼnthawi imene anali moyo. Yehova ankawamvera chisoni Aisraeli pamene ankabuwula chifukwa cha anthu owazunza ndi kuwasautsa. 19 Koma nthawi zonse mtsogoleri akamwalira, Aisraeli ankabwerera mʼmbuyo. Iwo amadzisandutsa oyipa kupambana makolo awo popeza ankatsata milungu ina, kuyitumikira ndi kumayigwadira. Anakana kusiya makhalidwe awo oyipa ndi njira zawo zamakani.
20 Choncho Yehova anawapsera mtima Aisraeli ndipo anati, “Chifukwa mtundu uwu waswa pangano limene ndinakhazikitsa ndi makolo awo ndipo sanandimvere, 21 Inenso sindidzapirikitsanso mtundu uli wonse wa anthu amene Yoswa anawasiya pomwalira. 22 Ndidzatero kuti ndiwayese Aisraeli ndi kuona ngati adzasamala kuyenda mʼnjira ya Ine Yehova monga momwe ankachitira makolo awo.” 23 Choncho Yehova anayileka mitundu imeneyi ndipo sanayithamangitse kapena kuyipereka mʼmanja mwa Yoswa.
8 Mngelo wachinayi anapita natsanula mbale yake pa dzuwa ndipo dzuwa linapatsidwa mphamvu yopsereza anthu ndi moto. 9 Anapserera nako kutentha kwakukuluko ndipo anatukwana Mulungu, amene anali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi, koma anakana kulapa ndi kumulemekeza.
10 Mngelo wachisanu anapita natsanula mbale yake pa mpando waufumu wa chirombo chija ndipo mdima unagwa ponse pamene panali ufumu wake. Anthu analuma malilime awo chifukwa cha ululu. 11 Ndipo anatukwana Mulungu wakumwamba chifukwa cha maululu awo ndi zilonda zawo koma anakana kulapa pa zimene anachita.
12 Mngelo wachisanu ndi chimodzi anapita natsanula mbale yake pa mtsinje waukulu wa Yufurate, ndipo madzi ake anaphwa kuti pakhale njira yodzera mafumu ochokera kummawa. 13 Kenaka ndinaona mizimu yoyipa itatu imene inkaoneka ngati achule; inatuluka mʼkamwa mwa chinjoka chija, mʼkamwa mwa chirombo chija ndi mʼkamwa mwa mneneri wonyenga uja. 14 Imeneyi ndiyo mizimu ya ziwanda imene imachita zizindikiro zodabwitsa ndipo imatuluka kupita kwa mafumu a dziko lonse, kukawasonkhanitsa ku nkhondo ya pa tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuzonse.
15 “Taonani, ndikubwera ngati mbala! Wodala munthu amene ali maso, nasunga zovala zake, kuti asayende maliseche kuti angaonetse maliseche ake.”
16 Kenaka mizimu ija inasonkhanitsa pamodzi mafumu ku malo amene mʼChihebri amatchedwa Armagedo.
17 Mngelo wachisanu ndi chiwiri anatsanulira mbale yake mu mlengalenga ndipo ku Nyumba ya Mulungu kunamveka mawu ofuwula kuchokera ku mpando waufumu kuti, “Kwatha!” 18 Kenaka kunachitika mphenzi, phokoso, mabingu ndi chivomerezi choopsa. Chivomerezi ngati ichi sichinachitikepo chikhalire cha munthu pa dziko lapansi. Chinali chivomerezi choopsa kwambiri. 19 Mzinda waukuluwo unagawika magawo atatu ndipo mizinda ya mitundu ya anthu inagwa. Mulungu anakumbukira Babuloni Wamkulu namupatsa chikho chake chodzaza ndi vinyo wa ukali wa mkwiyo wake. 20 Chilumba chilichonse chinathawa ndipo mapiri sanaonekenso. 21 Matalala akuluakulu olemera pafupifupi makilogalamu makumi asanu anagwa kuchokera kumwamba kugwera pa anthu. Ndipo anthu anatukwana Mulungu chifukwa cha mliri wa matalala popeza unali mliri woopsa kwambiri.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.