Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 78

Ndakatulo ya Asafu.

78 Inu anthu anga imvani chiphunzitso changa;
    mvetserani mawu a pakamwa panga.
Ndidzatsekula pakamwa panga mʼmafanizo,
    ndidzayankhula zinthu zobisika, zinthu zakalekale
zimene tinazimva ndi kuzidziwa,
    zimene makolo athu anatiwuza.
Sitidzabisira ana awo,
    tidzafotokozera mʼbado wotsatira
ntchito zotamandika za Yehova,
    mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.
Iye anapereka mawu wodzichitira umboni kwa Yakobo
    ndi kukhazikitsa lamulo mu Israeli,
zimene analamulira makolo athu
    kuphunzitsa ana awo,
kotero kuti mʼbado wotsatira uthe kuzidziwa,
    ngakhale ana amene sanabadwe,
    ndi kuti iwo akafotokozere ana awonso.
Choncho iwo adzakhulupirira Mulungu
    ndipo sadzayiwala ntchito zake
    koma adzasunga malamulo ake.
Iwo asadzakhale monga makolo awo,
    mʼbado wosamvera ndi wowukira,
umene mitima yake inali yosamvera Mulungu,
    umene mizimu yake inali yosakhulupirika kwa Iye.

Anthu a ku Efereimu, ngakhale ananyamula mauta,
    anathawabe pa nthawi ya nkhondo;
10 iwo sanasunge pangano la Mulungu
    ndipo anakana kukhala mʼmoyo wotsatira lamulo lake.
11 Anayiwala zimene Iye anachita,
    zozizwitsa zimene anawaonetsa.
12 Iyeyo anachita zodabwitsa makolo athu akuona,
    mʼdziko la Igupto, mʼchigawo cha Zowani.
13 Anagawa nyanja pakati ndi kudutsitsapo iwowo,
    Iye anachititsa madzi kuyima chilili ngati khoma.
14 Anawatsogolera ndi mtambo masana
    ndi kuwala kwa moto usiku wonse.
15 Iye anangʼamba miyala mʼchipululu
    ndi kuwapatsa madzi ochuluka ngati a mʼnyanja zambiri;
16 Anatulutsa mitsinje kuchokera mʼmingʼalu ya miyala
    ndi kuyenda madzi ngati mitsinje.

17 Komabe iwowo anapitiriza kumuchimwira Iye,
    kuwukira Wammwambamwamba mʼchipululu.
18 Ananyoza Mulungu mwadala
    pomuwumiriza kuti awapatse chakudya chimene anachilakalaka.
19 Iwo anayankhula motsutsana naye ponena kuti,
    “Kodi Mulungu angatipatse chakudya mʼchipululu?
20 Iye atamenya thanthwe
    madzi anatuluka,
    ndipo mitsinje inadzaza ndi madzi.
Koma iye angatipatsenso ife chakudya?
    Kodi angapereke nyama kwa anthu akewa?”
21 Yehova atawamva anakwiya kwambiri;
    moto wake unayaka kutsutsana ndi Yakobo,
    ndipo mkwiyo wake unauka kutsutsana ndi Israeli,
22 pakuti iwo sanakhulupirire Mulungu
    kapena kudalira chipulumutso chake.
23 Komabe Iye anapereka lamulo kwa mitambo mmwamba
    ndi kutsekula makomo a mayiko akumwamba;
24 anagwetsa mana kuti anthu adye,
    anawapatsa tirigu wakumwamba.
25 Anthu anadya buledi wa angelo,
    Iye anawatumizira chakudya chonse chimene akanatha kudya.
26 Anamasula mphepo ya kummwera kuchokera kumwamba,
    ndi kutsogolera mphepo ya kummwera mwa mphamvu zake.
27 Iye anawagwetsera nyama ngati fumbi,
    mbalame zowuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.
28 Anazibweretsa kwa iwo mʼkati mwa misasa yawo,
    kuzungulira matenti awo onse.
29 Iwo anadya mpaka anatsala nazo zochuluka
    pakuti Iye anawapatsa zimene anazilakalaka.
30 Koma iwowo anasiya kudya chakudya anachilakalakacho,
    chakudya chili mʼkamwa mwawobe,
31 mkwiyo wa Mulungu unawayakira;
    Iye anapha amphamvu onse pakati pawo,
    kugwetsa anyamata abwino kwambiri mu Israeli.

32 Ngakhale zinali chomwechi, iwo anapitirira kuchimwa;
    ngakhale anaona zozizwitsa zakezo iwowo sanakhulupirirebe.
33 Kotero Mulungu anachepetsa masiku awo kuti azimirire ngati mpweya.
    Iye anachepetsa zaka zawo kuti zithere mʼmasautso.
34 Mulungu atawapha, iwo amamufunafuna Iyeyo;
    iwo ankatembenukiranso kwa Iye mwachangu.
35 Ankakumbukira kuti Mulungu ndiye Thanthwe lawo,
    kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye Mpulumutsi wawo.
36 Komabe ankamuthyasika ndi pakamwa pawo,
    kumunamiza ndi malilime awo;
37 Mitima yawo sinali yokhazikika pa Iye,
    iwo sanakhulupirike ku pangano lake.
38 Komabe Iye anali wachifundo;
    anakhululukira mphulupulu zawo
    ndipo sanawawononge.
Nthawi ndi nthawi Iye anabweza mkwiyo wake
    ndipo sanawutse ukali wake wonse.
39 Iye anakumbukira kuti iwo anali anthu chabe,
    mphepo yopita imene sibwereranso.

40 Nthawi zambiri iwo ankamuwukira Iye mʼchipululu
    ndi kumumvetsa chisoni mʼdziko lopanda kanthu!
41 Kawirikawiri iwo ankamuyesa Mulungu;
    ankamuputa Woyera wa Israeli.
42 Sanakumbukire mphamvu zake,
    tsiku limene Iye anawawombola kwa ozunza,
43 tsiku limene Iyeyo anaonetsa poyera zizindikiro zozizwitsa zake mu Igupto,
    zozizwitsa zake mʼchigawo cha Zowani.
44 Iye anasandutsa mitsinje yawo kukhala magazi;
    Iwo sanathe kumwa madzi ochokera mʼmitsinje yawo.
45 Iye anawatumizira magulu a ntchentche zimene zinawawononga,
    ndiponso achule amene anawasakaza.
46 Iye anapereka mbewu zawo kwa ziwala,
    zokolola zawo kwa dzombe.
47 Iye anawononga mphesa zawo ndi matalala
    ndiponso mitengo yawo yankhuyu ndi chisanu.
48 Iye anapereka ngʼombe zawo ku matalala,
    zoweta zawo ku zingʼaningʼani.
49 Anakhuthula moto wa ukali wake pa iwo,
    anawapsera mtima nawakwiyira nʼkuwabweretsera masautso.
    Zimenezi zinali ngati gulu la angelo osakaza.
50 Analolera kukwiya,
    sanawapulumutse ku imfa
    koma anawapereka ku mliri.
51 Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto,
    zipatso zoyamba kucha za mphamvu zawo mʼmatenti a Hamu
52 Koma Iye anatulutsa anthu ake ngati ziweto;
    anawatsogolera ngati nkhosa kudutsa mʼchipululu.
53 Anawatsogolera bwinobwino kotero kuti analibe mantha
    koma nyanja inamiza adani awo.
54 Kotero anawafikitsa ku malire a dziko lake loyera,
    ku dziko lamapiri limene dzanja lake lamanja linawatengera.
55 Iye anathamangitsa mitundu ya anthu patsogolo pawo
    ndipo anapereka mayiko awo kwa Aisraeli kuti akhale awo;
    Iye anakhazikitsa mafuko a Israeli mʼnyumba zawo.

56 Koma iwo anayesa Mulungu
    ndi kuwukira Wammwambamwamba;
    sanasunge malamulo ake.
57 Anakhala okanika ndi osakhulupirika monga makolo awo,
    anapotoka monga uta wosakhulupirika.
58 Anakwiyitsa Iyeyo ndi malo awo opembedzera mafano;
    anawutsa nsanje yake ndi mafano awo.
59 Pamene Mulungu anamva zimenezi, anakwiya kwambiri;
    Iye anakana Israeli kwathunthu.
60 Anasiya nyumba ya ku Silo,
    tenti imene Iyeyo anayimanga pakati pa anthu.
61 Anatumiza mphamvu zake ku ukapolo,
    ulemerero wake mʼmanja mwa adani.
62 Anapereka anthu ake ku lupanga;
    anakwiya kwambiri ndi cholowa chake.
63 Moto unanyeketsa anyamata awo,
    ndipo anamwali awo analibe nyimbo za ukwati;
64 ansembe awo anaphedwa ndi lupanga,
    ndipo amayi awo amasiye sanathe kulira.

65 Kenaka Ambuye anakhala ngati akudzuka kutulo,
    ngati munthu wamphamvu wofuwula chifukwa cha vinyo.
66 Iye anathamangitsa adani ake;
    anawachititsa manyazi ku nthawi zonse.
67 Kenaka Iye anakana matenti a Yosefe,
    sanasankhe fuko la Efereimu;
68 Koma anasankha fuko la Yuda,
    phiri la Ziyoni limene analikonda.
69 Iye anamanga malo ake opatulika ngati zitunda,
    dziko limene analikhazikitsa kwamuyaya.
70 Anasankha Davide mtumiki wake
    ndi kumuchotsa pakati pa makola ankhosa;
71 kuchokera koyangʼanira nkhosa anamubweretsa
    kuti akhale mʼbusa wa anthu ake, Yakobo,
    wa Israeli cholowa chake.
72 Ndipo Davide anawaweta ndi mtima wolungama;
    ndi manja aluso anawatsogolera.

Nehemiya 8:1-12

Anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi pabwalo limene lili patsogolo pa Chipata cha Madzi. Iwo anawuza mlembi Ezara kuti abwere ndi buku la malamulo a Mose limene Yehova anapereka kwa Aisraeli.

Choncho pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri wansembe Ezara, anabwera ndi buku la malamulo ku msonkhano wa amuna, akazi ndi ana onse amene ankatha kumvetsa zinthu bwino. Choncho Ezara anawerenga bukulo atayangʼana bwalo la Chipata cha Madzi kuyambira mmawa mpaka masana pamaso pa amuna, akazi ndi onse amene ankamvetsa bwino zinthu. Ndipo anthu onse anatchera khutu kuti amve malamulowo.

Mlembi Ezara anayimirira pa nsanja ya mitengo imene anthu anamanga chifukwa cha msonkhanowu. Ku dzanja lake lamanja kunayimirira Matitiya, Sema, Anaya, Uriya, Hilikiya ndi Maaseya, ndipo kudzanja lake lamanzere kunali Pedaya, Misaeli, Malikiya, Hasumu, Hasibadana, Zekariya ndi Mesulamu.

Tsono Ezara anatsekula buku, akuona popeza anayima pa nsanja. Pamene anafutukula bukulo anthu onse anayimirira. Ezara anatamanda Yehova, Mulungu wamkulu, ndipo anthu onse anakweza manja awo ndi kuyankha kuti, “Ameni, ameni.” Pambuyo pake onse anaweramitsa pansi mitu yawo napembedza Yehova akanali chizolikire choncho.

Anthuwo atayimiriranso Alevi awa: Yesuwa, Bani, Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetayi, Hodiya, Maaseya, Kerita, Azariya, Yozabadi, Hanani ndi Pelaya anawathandiza kuti amvetse bwino malamulowo. Iwo anawerenga buku la malamulo a Mulungu momveka bwino ndi kutanthauzira mawuwo kuti anthu amvetse bwino zowerengedwazo.

Tsono bwanamkubwa Nehemiya pamodzi ndi wansembe ndi mlembi Ezara komanso Alevi amene amaphunzitsa anthu anati kwa anthu onse, “Lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova Mulungu wanu. Musakhale ndi chisoni ndipo musalire.” Anayankhula choncho popeza anthu onse ankalira atamva mawu a buku la malamulo lija.

10 Nehemiya anatinso, “Pitani, kachiteni phwando ku nyumba ndipo mukawagawireko ena amene alibe kanthu kalikonse popeza lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova. Musakhale ndi chisoni, pakuti chimwemwe cha Yehova ndiye mphamvu yanu.”

11 Alevi anakhalitsa bata anthu onse powawuza kuti, “Khalani chete, pakuti lero ndi tsiku lopatulika ndipo musakhale ndi chisoni.”

12 Anthu onse anachoka kupita kukadya ndi kumwa. Chakudya china anatumiza kwa anzawo. Choncho panali chikondwerero chachikulu popeza tsopano anali atamvetsa bwino mawu a Mulungu amene anawawerengera ndi kuwafotokozerawo.

1 Atesalonika 3:6-13

Nkhani Yolimbikitsa Kuchokera kwa Timoteyo

Koma tsopano Timoteyo wabwera kuchokera kwanuko ndipo watibweretsera nkhani yabwino ya chikhulupiriro chanu ndi chikondi chanu. Iye watiwuzanso kuti masiku onse mumatikumbukira mokondwa, ndipo kuti mumafunitsitsa kutionanso, monga momwe ifenso timalakalakira kukuonani inuyo. Motero abale, mʼmasautso ndi mʼmazunzo athu onse, chikhulupiriro chanu chatilimbikitsa. Ife tsopano tili moyodi, pakuti mukuyima molimbika mwa Ambuye. Tingathe bwanji kuyamika Mulungu mokwanira poona chimwemwe chonse chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu chifukwa cha inu? 10 Usana ndi usiku timapemphera ndi mtima wonse kuti tionanenso nanu, ndi kukwaniritsa zimene zikusowa pa chikhulupiriro chanu.

11 Tikupempha kuti Mulungu ndi Atate athu mwini, ndi Ambuye athu Yesu, atikonzere njira yabwino kuti tidzafike kwanuko. 12 Ambuye achulukitse chikondi chanu ndi kuti chisefukire kwa wina ndi mnzake ndiponso kwa wina aliyense, monga momwe chikondi chathu chichitira kwa inu. 13 Iye alimbikitse mitima yanu kuti mukhale opanda cholakwa ndi oyera mtima pamaso pa Mulungu ndi Atate athu pamene Ambuye athu Yesu akubwera ndi oyera ake onse.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.