Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yoswa 3:7-17

Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, “Lero Ine ndidzayamba kukukweza pamaso pa Aisraeli onse kuti adziwe kuti ndili nawe monga ndinalili ndi Mose. Ansembe amene akunyamula Bokosi la Chipangano uwalamule kuti, ‘Mukafika ku mtsinje wa Yorodani mulowe mu mtsinjemo ndi kuyima mʼmphepete.’ ”

Yoswa anati kwa Aisraeli, “Bwerani pano mudzamve mawu a Yehova Mulungu wanu. 10 Umu ndi mmene mudzadziwira kuti Mulungu wamoyo ali pakati panu. Inu mukamadzapita patsogolo Iye adzathamangitsa Akanaani, Ahiti, Ahivi, Aperezi, Agirigasi, Aamori ndi Ayebusi. 11 Pamenepo, Bokosi la Chipangano la Mbuye wa dziko lonse lapansi lidzawoloka mu Yorodani patsogolo panu. 12 Musankhe amuna khumi ndi awiri kuchokera ku fuko lililonse la Israeli. 13 Mapazi a ansembe onyamula Bokosi la Yehova, Mbuye wa dziko lapansi, akadzangoponda mu Yorodani, madzi ake onse ochokera ku mtunda adzaleka kuyenda ndipo adzayima ngati chipupa.”

14 Tsono Aisraeli anachoka ku misasa yawo kukawoloka mtsinje wa Yorodani. Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano ndiwo anatsogolera anthuwo. 15 Nyengo imeneyi inali yokolola ndipo mtsinje wa Yorodani umakhala wodzaza. Komabe, ansembe onyamula Bokosi la Chipangano anafika ku Yorodani, ndipo atangoponda mʼmadzimo, 16 madzi ochokera ku mtunda anasiya kuyenda. Madzi a Yorodani ochokera ku mtunda anawunjikana pamodzi ngati khoma lalitali pa mtunda wautali ndithu ndi mzinda wa Adama chapafupi ndi mzinda wa Zaretani. Madzi othamangira ku nyanja ya Araba, ngakhalenso amene amachokera kuti Nyanja ya Mchere amathera pamenepo. Choncho anthu anawoloka tsidya lina moyangʼanana ndi Yeriko. 17 Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano la Yehova anali chiyimire powuma, pakati pa Yorodani pamene Aisraeli amawoloka mpaka gulu lonse linamaliza kuwoloka powuma.

Masalimo 107:1-7

BUKU LACHISANU

Masalimo 107–150

107 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
    pakuti chikondi chake ndi chosatha.
Owomboledwa a Yehova anene zimenezi
    amene Iyeyo anawawombola mʼdzanja la mdani,
iwo amene anawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko,
    kuchokera kumadzulo ndi kummawa, kuchokera kumpoto ndi kummwera.

Ena anayendayenda mʼchipululu mopanda kanthu,
    osapeza njira yopitira ku mzinda kumene akanakakhazikikako.
Iwo anamva njala ndi ludzu,
    ndipo miyoyo yawo inafowokeratu.
Pamenepo analirira Yehova mʼmavuto awo
    ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awo.
Iye anawatsogolera mʼnjira yowongoka
    kupita ku mzinda umene anakakhazikikako.

Masalimo 107:33-37

33 Iye anasandutsa mitsinje kukhala chipululu,
    akasupe otuluka madzi kukhala nthaka yowuma,
34 ndiponso nthaka yachonde kukhala nthaka yamchere,
    chifukwa cha kuyipa kwa amene amakhala kumeneko.
35 Anasandutsa chipululu kukhala mayiwe a madzi
    ndi nthaka yowuma kukhala akasupe a madzi oyenda;
36 kumeneko Iye anabweretsa anthu anjala kuti azikhalako,
    ndipo iwo anamanga mzinda woti akhazikikeko.
37 Anafesa mbewu mʼminda ndi kudzala mipesa
    ndipo anakolola zipatso zochuluka;

1 Atesalonika 2:9-13

Abale, pakuti mukumbukira kugwira ntchito kwathu kwambiri ndi kuvutika; ife tinagwira ntchito usana ndi usiku ndi cholinga chakuti tisakhale cholemetsa, kwa aliyense pamene ife tinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu.

10 Inu ndinu mboni, ndiponso Mulungu, kuti tinali oyera mtima, olungama ndi wopanda chifukwa pakati panu amene munakhulupirira. 11 Monga mudziwa kuti ife tinkasamala aliyense wa inu monga abambo amasamalira ana ake, 12 kulimbikitsa, kutonthoza ndi kukupemphani kuti mukhale moyo oyenera Mulungu amene anakuyitanani kuti mulowe mu ufumu wake ndi ulemerero.

13 Ndipo ifenso tikuyamika Mulungu kosalekeza chifukwa mutalandira Mawu a Mulungu, amene munawamva kuchokera kwa ife, munawalandira osati ngati mawu a anthu, koma monga momwe alili, Mawu a Mulungu, amene akugwira ntchito mwa inu amene mukhulupirira.

Mateyu 23:1-12

Yesu Adzudzula Aphunzitsi Amalamulo ndi Afarisi

23 Pamenepo Yesu anati kwa magulu a anthu ndi ophunzira ake: “Aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi amakhala pa mpando wa Mose. Choncho muziwamvera ndi kuchita chilichonse chimene akuwuzani. Koma musachite zimene amachita, popeza sachita zimene amaphunzitsa. Amamanga akatundu olemera nawayika pa mapewa a anthu, koma iwo eni safuna kuwanyamula.

“Ntchito zawo amachita ndi cholinga chakuti anthu awaone. Amadzimangirira timaphukusi tikulutikulu ta Mawu a Mulungu pa mphumi ndi pa mkono komanso amatalikitsa mphonje za mikanjo yawo. Amakonda malo aulemu pa maphwando ndi malo ofunika kwambiri mʼmasunagoge. Amakondwera ndi kupatsidwa moni mʼmisika ndi kutchulidwa kuti ‘Aphunzitsi.’

“Koma inu simuyenera kutchulidwa ‘Aphunzitsi,’ popeza muli naye Mbuye mmodzi ndipo inu nonse ndinu abale. Ndipo musamatchule wina aliyense pansi pano kuti ‘Atate,’ pakuti muli ndi Atate mmodzi, ndipo ali kumwamba. 10 Komanso musamatchedwenso ‘Mtsogoleri,’ pakuti muli naye Mtsogoleri mmodzi amene ndi Khristu. 11 Wamkulu pakati panu adzakhala wokutumikirani. 12 Pakuti aliyense amene adzikuza adzachepetsedwa, ndipo aliyense amene adzichepetsa adzakuzidwa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.