Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 119:41-48

Wawi

41 Chikondi chanu chosasinthika chibwere kwa ine, Inu Yehova,
    chipulumutso chanu monga mwa lonjezo lanu;
42 ndipo ndidzayankha amene amandinyoza,
    popeza ndimadalira mawu anu.
43 Musakwatule mawu a choonadi mʼkamwa mwanga,
    pakuti ndakhazikitsa chiyembekezo changa mʼmalamulo anu.
44 Ndidzasunga malamulo anu nthawi zonse,
    ku nthawi za nthawi.
45 Ndidzayendayenda mwaufulu,
    chifukwa ndinafunafuna malangizo anu.
46 Ndidzayankhula za umboni wanu pamaso pa mfumu
    ndipo sindidzachititsidwa manyazi,
47 popeza ndimakondwera ndi malamulo anu
    chifukwa ndimawakonda.
48 Ndikweza manja anga ku malamulo anu, ku malamulo amene ndimawakonda,
    ndipo ndimalingalira malangizo anu.

Eksodo 34:29-35

Nkhope ya Mose Inyezimira

29 Mose anatsika kuchokera mʼPhiri la Sinai pamodzi ndi miyala iwiri ija ya pangano mʼmanja mwake. Iye sanazindikire kuti nkhope yake imanyezimira pakuti anayankhula ndi Yehova. 30 Aaroni ndi Aisraeli ataona kuti nkhope ya Mose imanyezimira anaopa kumuyandikira. 31 Koma Mose anawayitana. Kotero Aaroni ndi atsogoleri onse a gululo anabwera kwa iye, ndipo anawayankhula. 32 Kenaka Aisraeli onse anamuyandikira, ndipo anawapatsa malamulo onse omwe Yehova anamupatsa pa Phiri la Sinai.

33 Mose atamaliza kuyankhula nawo anaphimba nkhope yake. 34 Koma nthawi zonse popita pamaso pa Yehova kukayankhula naye amachotsa chophimbacho mpaka atatuluka. Ndipo akatuluka kudzawuza Aisraeli zimene walamulidwa, 35 iwo amaona nkhope yake ikunyezimira. Choncho Mose amaphimba nkhope yake ngakhale pamene amapita kukayankhula ndi Yehova.

Yakobo 2:14-26

Chikhulupiriro ndi Ntchito Zabwino

14 Abale anga, phindu lake nʼchiyani ngati munthu anena kuti ali ndi chikhulupiriro koma chopanda ntchito zabwino? Kodi chikhulupiriro choterechi chingamupulumutse? 15 Tangoganizirani, mʼbale kapena mlongo amene ali ndi usiwa, ndipo alibe chakudya cha tsiku ndi tsiku. 16 Ngati mmodzi wa inu amuwuza kuti, “Pita ndi mtendere, ukafundidwe ndipo ukakhute,” koma osamupatsa zimene akuzisowa, phindu lake nʼchiyani pamenepa? 17 Chomwechonso, chikhulupiriro chokha chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.

18 Koma wina anganene kuti, “Inuyo muli ndi chikhulupiriro koma ine ndili ndi ntchito zabwino.”

Onetsani chikhulupiriro chanu chopanda ntchito zabwino ndipo ineyo ndidzakuonetsani chikhulupiriro changa pochita ntchito zabwino. 19 Mumakhulupirira kuti kuli Mulungu mmodzi yekha. Mumachita bwino. Komatu ngakhale ziwanda zimakhulupirira zimenezi ndipo zimanjenjemera ndi mantha.

20 Munthu wopusa iwe, kodi ukufuna umboni woti chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino nʼchakufa? 21 Kodi Abrahamu kholo lathu sanatengedwe kukhala wolungama chifukwa cha zimene anachita pamene anapereka mwana wake Isake pa guwa lansembe? 22 Tsono mukuona kuti chikhulupiriro chake ndi ntchito zabwino zinkachitika pamodzi, ndipo chikhulupiriro chake chinasanduka chenicheni chifukwa cha ntchito zake zabwino. 23 Ndipo Malemba akunena kuti, “Abrahamu anakhulupirira Mulungu ndipo anatengedwa kukhala wolungama,” ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu. 24 Tsono mukuona kuti munthu amasanduka wolungama ndi ntchito zabwino osati ndi chikhulupiriro chokha ayi.

25 Nʼchimodzimodzinso, kodi wadama uja, Rahabe, sanasanduke wolungama chifukwa cha zomwe anachita pamene anapereka malo ogona kwa azondi aja ndi kuwathawitsira mbali ina? 26 Monga thupi lopanda mzimu ndi lakufa, chomwechonso chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.