Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 119:41-48

Wawi

41 Chikondi chanu chosasinthika chibwere kwa ine, Inu Yehova,
    chipulumutso chanu monga mwa lonjezo lanu;
42 ndipo ndidzayankha amene amandinyoza,
    popeza ndimadalira mawu anu.
43 Musakwatule mawu a choonadi mʼkamwa mwanga,
    pakuti ndakhazikitsa chiyembekezo changa mʼmalamulo anu.
44 Ndidzasunga malamulo anu nthawi zonse,
    ku nthawi za nthawi.
45 Ndidzayendayenda mwaufulu,
    chifukwa ndinafunafuna malangizo anu.
46 Ndidzayankhula za umboni wanu pamaso pa mfumu
    ndipo sindidzachititsidwa manyazi,
47 popeza ndimakondwera ndi malamulo anu
    chifukwa ndimawakonda.
48 Ndikweza manja anga ku malamulo anu, ku malamulo amene ndimawakonda,
    ndipo ndimalingalira malangizo anu.

Numeri 33:38-39

38 Molamulidwa ndi Yehova, wansembe Aaroni anakwera ku phiri la Hori kumene anakamwalirira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu, mʼchaka cha makumi anayi, Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto. 39 Aaroni anamwalira pa phiri la Hori ali ndi zaka 123.

Yakobo 2:8-13

Ngati musungadi lamulo laufumu lija lopezeka mʼMalemba lakuti, “Konda mnansi wako monga iwe mwini,” ndiye kuti mukuchita bwino. Koma mukamaonetsa tsankho mukuchimwa, ndipo ndinu wochimwa monga wophwanya lamulo. 10 Pakuti amene amasunga Malamulo onse, akangophwanya fundo imodzi yokha, waphwanya Malamulo onse. 11 Pakuti amene anati “Usachite chigololo” ndi yemweyonso anati “Usaphe.” Ngati suchita chigololo koma umapha, ndiwe wophwanya Malamulo.

12 Muziyankhula ndi kuchita zinthu monga anthu amene mudzaweruzidwe ndi lamulo limene limapereka ufulu, 13 chifukwa munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso adzaweruzidwa mopanda chifundo. Chifundo chimapambana pa chiweruzo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.