Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
BUKU LACHINAYI
Masalimo 90–106
Pemphero la Mose munthu wa Mulungu.
90 Ambuye, mwakhala muli malo athu okhalamo
pa mibado yonse.
2 Mapiri asanabadwe,
musanalenge nʼkomwe dziko lapansi ndi dziko lonse,
kuyambira muyaya mpaka muyaya Inu ndinu Mulungu.
3 Inu mumabwezera anthu ku fumbi,
mumati, “Bwerera ku fumbi iwe mwana wa munthu.”
4 Pakuti zaka 1,000 pamaso panu
zili ngati tsiku limene lapita
kapena ngati kamphindi ka usiku.
5 Inu mumasesa anthu mʼtulo ta imfa,
iwo ali ngati udzu watsopano wa mmawa,
6 ngakhale kuti mmawa umaphuka watsopano,
pofika madzulo wauma ndi kufota.
13 Lezani mtima Inu Yehova! Kodi mudzatikwiyira mpaka liti?
Achitireni chifundo atumiki anu.
14 Mutikhutitse mmawa ndi chikondi chanu chosatha,
kuti tiyimbe ndi chimwemwe ndi kukhala okondwa masiku athu onse.
15 Tisangalatseni masiku ambiri monga masiku amene mwatisautsa,
kwa zaka zambiri monga momwe tinaonera mavuto.
16 Ntchito zanu zionetsedwe kwa atumiki anu,
kukongola kwanu kwa ana awo.
17 Kukoma mtima kwa Ambuye Mulungu wathu kukhale pa ife;
tikhazikitsireni ntchito ya manja athu;
inde, khazikitsani ntchito ya manja athu.
44 Mose anabwera ndi Yoswa mwana wa Nuni ndipo anayankhula mawu onsewa mʼnyimbo anthu akumva. 45 Mose atatsiriza kunena mawu onsewa pamtima kwa Aisraeli, 46 iye anawawuza kuti, “Muwasunge bwino mu mtima mwanu, mawu onse amene lero lino ndikukuwuzani kuti mudzawuze ana anu, kuti adzamvere mosamalitsa mawu onse a malamulo amenewa. 47 Mawuwa sikuti ndi mawu achabe kwa inu. Mawuwa ndi moyo wanu. Mukawamvera mudzakhala ndi moyo wautali mʼdziko limene mukukalitenga kukhala lanu mukawoloka Yorodani.”
39 Inu mumasanthula malemba chifukwa mumaganiza kuti mʼmalembamo muli moyo wosatha. Awa ndi malemba amene akundichitira umboni. 40 Koma inu mukukana kubwera kwa Ine kuti mukhale ndi moyo.
41 “Ine sindilandira ulemu kuchokera kwa anthu 42 koma Ine ndikukudziwani. Ndikudziwa kuti mʼmitima mwanu mulibe chikondi cha Mulungu. 43 Ine ndabwera mʼdzina la Atate anga, ndipo inu simukundirandira Ine; koma wina wake akabwera mʼdzina la iye mwini, inu mudzamulandira. 44 Kodi inu mudzakhulupirira bwanji ngati mumapatsana ulemu wina ndi mnzake, ndipo simufuna kulandira ulemu kuchokera kwa Mulungu yekhayo?
45 “Koma inu musaganize kuti Ine ndidzakunenezani kwa Atate. Wokunenezani ndi Mose, amene inu mwayikapo chiyembekezo chanu. 46 Ngati mukanakhulupirira Mose, mukanakhulupiriranso Ine, pakuti iye analemba za Ine. 47 Koma ngati simukhulupirira zimene iye analemba, mudzakhulupirira bwanji zimene Ine ndikunena?”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.