Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide. Pamene anali mʼchipululu cha Yuda.
63 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga,
moona mtima ine ndimakufunafunani;
moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu,
thupi langa likulakalaka inu,
mʼdziko lowuma ndi lotopetsa
kumene kulibe madzi.
2 Inu ndinakuonani ku malo anu opatulika
ndipo ndinapenya mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.
3 Chifukwa chikondi chanu
ndi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani.
4 Ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga,
ndipo mʼdzina lanu ndidzakweza manja anga.
5 Mudzakhutitsa moyo wanga ndi zonona.
Ine ndidzakutamandani ndi mawu anthetemya.
6 Pa bedi panga ndimakumbukira inu;
ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku.
7 Chifukwa ndinu thandizo langa,
ine ndimayimba mu mthunzi wa mapiko anu.
8 Moyo wanga umakangamira Inu;
dzanja lanu lamanja limandigwiriziza.
Ulemerero wa Yehova
34 Kenaka mtambo unaphimba tenti ya msonkhano, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho. 35 Mose sanathe kulowa mu tenti ya msonkhano chifukwa mtambo unali utakhazikika pa chihemacho, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho.
36 Pa maulendo awo onse, mtambo ukachoka pamwamba pa chihema, Aisraeli ankasamukanso pamene analipo. 37 Koma ngati mtambo sunachoke, iwo sankasamukanso mpaka tsiku limene udzachoke. 38 Kotero mtambo wa Yehova unkakhala pamwamba pa chihema usana, ndi mtambo wamoto umakhala usiku, pamaso pa nyumba yonse ya Israeli pa masiku onse aulendo wawo.
Kugwa kwa Babuloni
18 Zitatha izi ndinaona mngelo wina akutsika kuchokera kumwamba. Iye anali ndi ulamuliro waukulu, ndipo dziko lapansi linawala ndi ulemerero. 2 Mngeloyo anafuwula ndi mawu amphamvu kuti:
“ ‘Wagwa! Wagwa Babuloni Wamkulu!’
Wasandulika mokhalamo ziwanda
ndi kofikako mizimu yonse yoyipa
ndi mbalame zonse zonyansa
ndi zodetsedwa.
3 Pakuti mayiko onse amwa
vinyo ozunguza mutu wazigololo zake.
Mafumu a dziko lapansi achita naye chigololo,
ndipo amalonda a dziko lapansi analemera kuchokera pa zolakalaka zake zosefukira.”
Awachenjeza kuti Athawe Chiweruzo cha Babuloni
4 Ndiponso ndinamva mawu ena kuchokera kumwamba akuti:
“ ‘Anthu anga tulukani, mwa iye,’
mungachimwe naye
kuti musadzalandire nawo gawo lililonse la miliri yake;
5 pakuti machimo ake awunjikana mpaka kumwamba,
ndipo Mulungu wakumbukira milandu yake.
6 Bwezerani Iye monga momwe iye anakuchitirani.
Mubwezereni mowirikiza pa zimene anachita.
Mumusakanizire magawo awiri kuchokera mʼchikho chake.
7 Mumuzunze, kumumvetsa chisoni kwambiri
monga mwaulemerero ndi zolakalaka
zimene anadzaza mu mtima mwake. Iye anadzikuza nʼkumati,
‘Ndinakhala monga mfumu yayikazi,
ine sindine wamasiye
ndipo sindidzalira maliro.’
8 Chifukwa chake miliri yake idzamugonjetsa tsiku limodzi;
imfa, kulira maliro ndi njala.
Iye adzanyeka ndi moto
pakuti wamphamvu ndi Mulungu Ambuye amene wamuweruza.
Tsoka la Babuloni
9 “Mafumu a dziko lapansi, amene anachita naye chigololo nachita naye pamodzi zosangalatsa moyo uno, akadzaona utsi wa kunyeka kwake, adzalira nakhuza maliro ake. 10 Iwo adzayima kutali nalira chifukwa choopsedwa ndi mazunzo ake.
“ ‘Tsoka! Tsoka mzinda waukulu
iwe, Babuloni mzinda wamphamvu!
Mu ora limodzi chiwonongeko chako chafika!’
19 Adzathira fumbi pamitu pawo ndipo adzalira nakhuza maliro kuti,
“Tsoka! Tsoka mzinda waukulu iwe,
kumene onse anali ndi sitima pa nyanja
analemera kudzera mʼchuma chake!
Mu ora limodzi wawonongedwa.
20 “Kondwerani chifukwa cha iye inu kumwamba!
Kondwerani oyera mtima
ndi atumwi ndi aneneri!
Mulungu wamuweruza iye
monga momwe anakuchitirani inu.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.