Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 97

97 Yehova akulamulira, dziko lapansi lisangalale;
    magombe akutali akondwere.

Mitambo ndi mdima waukulu zamuzungulira;
    chilungamo ndi kuweruza molungama ndiwo maziko a mpando wake waufumu.
Moto umapita patsogolo pake
    ndi kunyeketsa amaliwongo kumbali zonse.
Zingʼaningʼani zake zimawalitsa dziko lonse;
    dziko lapansi limaona ndipo limanjenjemera.
Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova,
    pamaso pa Ambuye a dziko lonse lapansi.
Mayiko akumwamba amalengeza za chilungamo chake,
    ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake.

Onse amene amalambira mafano osema amachititsidwa manyazi,
    iwo amene amanyadira mafano;
    mulambireni, inu milungu yonse!

Ziyoni akumva ndipo akukondwera,
    midzi ya Yuda ikusangalala
    chifukwa cha maweruzo anu Yehova.
Pakuti Inu Yehova ndi Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi;
    ndinu wokwezeka kupambana milungu yonse.

10 Iwo amene amakonda Yehova adane ndi zoyipa
    pakuti Iye amayangʼanira miyoyo ya amene amamukhulupirira
    ndipo amawapulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa
11 Kuwala kumafika pa anthu olungama,
    ndi chimwemwe kwa olungama mtima.
12 Kondwerani mwa Yehova Inu olungama
    ndipo tamandani dzina lake loyera.

2 Mafumu 17:7-20

Israeli Apita ku Ukapolo chifukwa cha Tchimo

Zonsezi zinachitika chifukwa Aisraeli anachimwira Yehova Mulungu wawo, amene anawatulutsa mʼdziko la Igupto pansi pa ulamuliro wa Farao mfumu ya Igupto. Iwo ankapembedza milungu ina, ndiponso ankatsatira miyambo ya anthu a mitundu imene Yehova anayichotsa pamene iwo ankafika mʼdzikomo pamodzinso ndi miyambo yonse imene mafumu a Israeli anayambitsa. Ndipo Aisraeli ankachita zoyipa mwamseri kutsutsana ndi Yehova Mulungu wawo. Kuchokera ku nsanja ya alonda mpaka ku mzinda wotetezedwa, mʼmizinda yawo yonse anamangamo malo opembedzeramo mafano. 10 Anayimika miyala ya chipembedzo ndi mitengo ya mafano a Asera pa phiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri. 11 Pa malo aliwonse opembedzera mafano, anthuwa ankafukiza lubani monga momwe ankachitira anthu a mitundu imene Yehova anayichotsa pamene iwo ankafika. Iwo anachita zinthu zoyipa zomwe zinaputa mkwiyo wa Yehova. 12 Ndipo iwowo ankapembedza mafano ngakhale Yehova ananena kuti, “Musadzachite zimenezi.” 13 Yehova anachenjeza Israeli ndi Yuda kudzera mwa aneneri ake onse ndi alosi kuti, “Lekani mchitidwe wanu woyipawo. Mverani malamulo anga ndi malangizo anga potsatira zonse zolembedwa mʼmalamulo a Mose, zimene ndinalamulira makolo anu kuti azimvere, kudzera mwa aneneri, atumiki anga.”

14 Koma anthuwa sanamvere ndipo anawumitsa khosi ngati momwe analili makolo awo, amene sanadalire Yehova Mulungu wawo. 15 Anakana malangizo ake ndi pangano anachita ndi makolo awo ndipo ananyoza zochenjeza za Yehova. Iwo anatsatira mafano achabechabe nasanduka achabechabe. Anthuwa anatsanzira mitundu ya anthu owazungulira ngakhale kuti Yehova anawalamula kuti, “Musamachite zomwe iwo amachita,” koma iwo anachita zomwe Yehova anawaletsa.

16 Iwowo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wawo, nadzipangira mafano awiri osungunula a ana angʼombe ndiponso fano la Asera, napembedza zonse zamlengalenga ndi kutumikira Baala. 17 Ndipo anadutsitsa mʼmoto ana awo aamuna ndi aakazi. Iwo ankawombeza mawula, namachitanso zanyanga ndipo anadzipereka kuchita zoyipa pamaso pa Yehova namukwiyitsa.

18 Choncho Yehova anakwiya nawo kwambiri Aisraeli ndipo anawachotsa pamaso pake. Palibe amene anatsala kupatula fuko la Yuda lokha. 19 Yuda nayenso sanasunge malamulo a Yehova Mulungu wawo. Iwo ankatsatira machitidwe amene Israeli anayambitsa. 20 Motero Yehova anakana Aisraeli onse. Iye anawazunza nawapereka mʼmanja mwa anthu ofunkha mpaka Iye atawachotseratu pamaso pake.

Yohane 6:25-35

Yesu Chakudya Chamoyo

25 Atamupeza mbali ina ya nyanjayo, iwo anamufunsa Iye kuti, “Rabi, mwafika nthawi yanji kuno?”

26 Yesu anawayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mukundifuna, osati chifukwa munaona zizindikiro zodabwitsa koma chifukwa munadya chakudya ndi kukhuta. 27 Gwirani ntchito, osati chifukwa cha chakudya chimene chimawonongeka koma chifukwa cha chakudya chimene sichiwonongeka mpaka ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani. Mulungu Atate anamusindikiza chizindikiro chomuvomereza.”

28 Kenaka anamufunsa Iye kuti, “Kodi tichite chiyani kuti tigwire ntchito za Mulungu?”

29 Yesu anayankha kuti, “Ntchito ya Mulungu ndi iyi: Kukhulupirira Iye amene anamutuma.”

30 Choncho iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi mudzatipatsa chizindikiro chodabwitsa chotani kuti ife tichione ndi kukhulupirira Inu? Kodi mudzachita chiyani? 31 Makolo athu akale anadya mana mʼchipululu; monga zalembedwa: ‘anawapatsa buledi wochokera kumwamba kuti adye.’ ”

32 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti si Mose amene ankakupatsani chakudya chochokera kumwamba, koma ndi Atate anga amene ankakupatsani chakudya chenicheni chochokera kumwamba. 33 Pakuti chakudya cha Mulungu ndi Iye amene wabwera kuchokera kumwamba ndi kupereka moyo ku dziko la pansi.”

34 Iwo anati, “Ambuye, kuyambira tsopano muzitipatsa buledi ameneyu.”

35 Kenaka Yesu ananenetsa kuti, “Ine ndine chakudya chamoyo. Iye amene abwera kwa Ine sadzamva njala, ndipo iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.