Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 106:1-6

106 Tamandani Yehova.

Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
    pakuti chikondi chake ndi chosatha.
Ndani angathe kufotokoza za ntchito zamphamvu za Yehova
    kapena kumutamanda mokwanira?
Odala ndi amene amasunga chilungamo,
    amene amachita zolungama nthawi zonse.
Mundikumbukire Yehova, pamene mukuonetsa kukoma mtima kwanu kwa anthu anu,
    bwerani mudzandithandize pamene mukuwapulumutsa iwo,
kuti ndidzasangalale ndi chuma cha anthu anu osankhika,
    kuti ndidzakhale nacho chimwemwe cha anthu anu
    ndi kukhala pamodzi ndi cholowa chanu pa kukutamandani.

Ife tachimwa monga momwe anachitira makolo athu;
    tachita zolakwa ndipo tachita moyipa.

Masalimo 106:19-23

19 Iwo anapanga mwana wangʼombe pa Horebu
    ndi kulambira fano loyengedwa kuchokera ku chitsulo.
20 Anasinthanitsa ulemerero wawo
    ndi fano la ngʼombe yayimuna imene imadya udzu.
21 Anayiwala Mulungu amene anawapulumutsa,
    amene anachita zinthu zazikulu mu Igupto,
22 zozizwitsa mʼdziko la Hamu
    ndi machitidwe ake woopsa pa Nyanja Yofiira.
23 Choncho Iye anawawuza kuti adzawawononga,
    pakanapanda Mose, mtumiki wake wosankhidwa,
kuyima pamaso pake,
    ndi kuletsa mkwiyo wake kuti usawawononge.

Eksodo 24:12-18

12 Yehova anati kwa Mose, “Bwera kwa ine ku phiri kuno, ndipo udikire konkuno. Ndidzakupatsa miyala imene ndalembapo malemba kuti ndiwaphunzitse.”

13 Ndipo anayamba ulendo wopita ku phiri la Mulungu pamodzi ndi womuthandiza wake Yoswa. 14 Apa nʼkuti Mose atawawuza akuluakulu aja kuti, “Mudikire pano mpaka titabweranso. Aaroni ndi Huri ali nanu, aliyense amene ali ndi milandu apite kwa iwo.”

15 Mose atakwera ku phiri kuja mtambo unaphimba phirilo. 16 Ulemerero wa Yehova unakhala pa phiri la Sinai, ndipo mtambo unaphimba phirilo kwa masiku asanu ndi limodzi. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri Yehova anayitana Mose kuchokera mu mtambowo. 17 Ulemerero wa Yehova uja unkaoneka ngati malawi a moto pamwamba pa phirilo. 18 Ndipo Mose analowa mʼmitambo nakwera phiri. Iye anakhala ku phiriko 40 usana ndi usiku.

Marko 2:18-22

Za Kusala Kudya

18 Ndipo ophunzira a Yohane ndi a Afarisi amasala kudya. Anthu ena anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Zitheka bwanji kuti ophunzira a Yohane ndi ophunzira a Afarisi amasala kudya, koma anu satero?”

19 Yesu anayankha nati, “Kodi alendo a mkwati angasale kudya bwanji pamene iye ali nawo pamodzi? Iwo sangatero, pamene iye ali nawo pamodzi. 20 Koma nthawi idzafika pamene mkwati adzachotsedwa pakati pawo, ndipo pa tsiku limenelo adzasala kudya.

21 “Palibe amene amasokerera chigamba chatsopano pa chovala chakale. Ngati atatero, chigamba chatsopanocho chidzazomola chovala chakalecho, kukulitsa chibowocho. 22 Ndipo palibe amene amathira vinyo watsopano mʼmatumba akale a vinyo. Ngati atatero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba a vinyo ndipo vinyoyo pamodzi ndi matumbawo zidzawonongeka. Ayi, satero, amathira vinyo watsopano mʼmatumba atsopanonso.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.