Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 19

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

19 Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu;
    thambo limalalikira ntchito za manja ake.
Tsiku ndi tsiku zimayankhula mawu ambiri,
    usiku ndi usiku zimaonetsa poyera nzeru.
Palibe kuyankhula, palibe mawu aliwonse;
    liwu lawo silimveka.
Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi,
    mawuwo amafika mpaka
kumalekezero a dziko lapansi.
    Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake,
    ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano.
Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambo
    ndi kuzungulira mpaka mbali inanso;
    palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake.

Lamulo la Yehova ndi langwiro,
    kutsitsimutsa moyo.
Maumboni a Yehova ndi odalirika,
    amapereka nzeru kwa wopanda nzeru.
Malangizo a Yehova ndi olungama,
    amapereka chimwemwe mu mtima.
Malamulo a Yehova ndi onyezimira,
    amapereka kuwala.
Kuopa Yehova ndiye chinthu changwiro,
    chimakhala mpaka muyaya.
Maweruzo a Yehova ndi owona
    ndipo onse ndi olungama;
10 ndi a mtengowapatali kuposa golide,
    kuposa golide weniweni;
ndi otsekemera kuposa uchi,
    kuposa uchi wochokera pa chisa chake.
11 Mtumiki wanu amachenjezedwa nawo;
    powasunga pali mphotho yayikulu.

12 Ndani angathe kudziwa zolakwa zake?
    Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.
13 Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa;
    iwo asandilamulire.
Kotero ndidzakhala wosalakwa,
    wopanda mlandu wa tchimo lalikulu.

14 Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga
    zikhale zokondweretsa pamaso panu,
    Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.

Eksodo 23:1-9

Malamulo a Zachilungamo ndi Zachifundo

23 “Usafalitse mbiri yabodza. Usathandize munthu wolakwa pomuchitira umboni wonama.

“Usatsate gulu la anthu ndi kuchita choyipa. Pamene ukupereka umboni mʼbwalo lamilandu, usakhotetse mlandu chifukwa chofuna kukondweretsa anthu ambiri. Ndipo poweruza mlandu wa munthu wosauka usamukondere.

“Ngati ukumana ndi ngʼombe kapena bulu wa mdani wako zitasochera, uwonetsetse kuti wazitenga kupita nazo kwa mwini wakeyo. Ngati uwona bulu wa munthu wina amene amakuda atagwa ndi katundu, usamusiye pomwepo, uwonetsetse kuti wamuthandiza.

“Usakhotetse milandu ya anthu osauka. Upewe zabodza ndipo usaphetse munthu wosalakwa ndi wolungama, chifukwa Ine sindidzakhululukira wochimwa.

“Musamalandire chiphuphu, pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu oweruza ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa.

“Usamuzunze mlendo, pakuti inu nomwe mukudziwa mmene amamvera mlendo chifukwa nanunso munali alendo mʼdziko la Igupto.

Akolose 2:16-23

Ufulu Wathu

16 Nʼchifukwa chake musalole wina aliyense kukuzengani mlandu chifukwa cha zimene mumadya kapena kumwa, kapena za masiku achikondwerero cha chipembedzo, za chikondwerero cha mwezi watsopano, kapena za tsiku la Sabata. 17 Zimenezi ndi chithunzithunzi chabe cha zinthu zimene zikubwera, koma choonadi chenicheni chikupezeka mwa Khristu. 18 Musalole kuti wina aliyense amene amakonda kudzichepetsa mwachiphamaso ndi kumapembedza angelo akulepheretseni kukalandira mphotho. Munthu woteroyu amayankhulanso mwatsatanetsatane zinthu zimene akuti anaziona mʼmasomphenya. Anthuwa ndi odzitukumula ndi fundo zopanda pake zochokera mʼmaganizo mwawo amene si auzimu. 19 Iwo sakulumikizananso ndi mutu, kumene kumachokera thupi lonse, logwirizidwa ndi kumangiriridwa pamodzi ndi mʼmitsempha yake ndi mnofu, limene limakula monga mmene Mulungu afunira kuti likulire.

20 Popeza munafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nayo miyambo ya dziko lapansi lino, nʼchifukwa chiyani mukukhalanso ngati a dziko lapansi lino? Bwanji mukumvera malamulo monga awa: 21 “Usagwire chakuti,” “Usalawe chakuti,” “Usakhudze chakuti?” 22 Malamulo amenewa amakhudza zinthu zimene zimatha zikamagwiritsidwa ntchito, ndipo malamulo ndi zophunzitsa za anthu chabe. 23 Ndithu malamulo oterewa amaoneka ngati anzeru, pakuti amalamulira anthu ambiri pa zachipembedzo ndi pa zakudzichepetsa kwa chiphamaso, ndi pa zakuzunza thupi lawo, koma alibe mphamvu zoletsa kuchita zofuna za thupilo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.