Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
BUKU LACHIWIRI
Masalimo 42–72
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora.
42 Monga mbawala ipuma wefuwefu kufunafuna mitsinje yamadzi,
kotero moyo wanga upuma wefuwefu kufunafuna Inu Mulungu.
2 Moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Mulungu, lofuna Mulungu wamoyo.
Kodi ndipite liti kukakumana ndi Mulungu?
3 Misozi yanga yakhala chakudya changa
usana ndi usiku,
pamene anthu akunena kwa ine tsiku lonse kuti,
“Mulungu wako ali kuti?”
4 Zinthu izi ndimazikumbukira
pamene ndikukhuthula moyo wanga:
momwe ndinkapitira ndi gulu lalikulu,
kutsogolera mayendedwe a ku Nyumba ya Mulungu
ndi mfuwu yachimwemwe ndi mayamiko
pakati pa anthu a pa chikondwerero.
5 Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni, iwe moyo wanga?
Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga?
Yembekezera Mulungu,
pakuti ndidzamulambirabe,
Mpulumutsi wanga ndi 6 Mulungu wanga.
Moyo wanga uli ndi chisoni mʼkati mwanga
kotero ndidzakumbukira Inu
kuchokera ku dziko la Yorodani,
ku mitunda ya Herimoni kuchokera ku phiri la Mizara.
7 Madzi akuya akuyitana madzi akuya
mu mkokomo wa mathithi anu;
mafunde anu onse obwera mwamphamvu
andimiza.
8 Koma usana Yehova amalamulira chikondi chake,
nthawi ya usiku nyimbo yake ili nane;
pemphero kwa Mulungu wa moyo wanga.
9 Ine ndikuti kwa Mulungu Thanthwe langa,
“Nʼchifukwa chiyani mwandiyiwala?
Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira,
woponderezedwa ndi mdani?”
10 Mafupa anga ali ndi ululu wakufa nawo
pamene adani anga akundinyoza,
tsiku lonse akunena kuti,
“Mulungu wako ali kuti?”
11 Bwanji ukumva chisoni,
iwe mtima wanga?
Chifukwa chiyani ukuvutika chonchi mʼkati mwanga?
Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandanso,
Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
9 Yehova anati kwa Mose, “Ine ndibwera kwa iwe mu mtambo wakuda kuti anthu adzandimve ndikuyankhula ndi iwe. Choncho adzakukhulupirira nthawi zonse.” Kenaka Mose anawuza Yehova zimene anthu ananena.
10 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Pita kwa anthu onse ndi kuwayeretsa lero ndi mawa. Achape zovala zawo 11 ndipo akhale atakonzeka pofika tsiku lachitatu, chifukwa tsiku limenelo Yehova adzatsika pa phiri la Sinai anthu onse akuona. 12 Uwalembere malire anthuwo kuzungulira phirilo ndipo uwawuze kuti, ‘Samalani musakwere phirilo kapena kukhudza tsinde lake. Aliyense wokhudza phiri adzaphedwa ndithu. 13 Aliyense wokhudza phiri adzaphedwa ndi miyala kapena kumulasa ndi mivi. Palibe amene adzamukhudze. Palibe munthu amene adzaloledwa kukhala ndi moyo ngakhale nyama. Iwo adzayenera kuphedwa.’ Koma anthu adzapita ku phirilo akadzamva kulira kwa lipenga la nyanga yankhosa.”
14 Tsono Mose anatsika phiri lija nafika kwa anthu aja ndi kuwayeretsa. Iwo anachapa zovala zawo. 15 Kenaka iye anati kwa anthu, “Konzekerani tsiku lachitatu, musagone pamodzi ndi mkazi.”
16 Mʼmamawa wa tsiku lachitatu kunali mabingu, ziphaliwali ndi mtambo wakuda umene unaphimba phiri, ndiponso lipenga lolira kwambiri. Aliyense ku misasa kuja ananjenjemera ndi mantha. 17 Ndipo Mose anatsogolera anthu kutuluka mʼmisasa kukakumana ndi Mulungu, ndipo anayima mʼmunsi mwa phiri. 18 Phiri la Sinai linakutidwa ndi utsi, chifukwa Yehova anatsika ndi moto pa phiripo. Utsi unakwera ngati wochokera mʼngʼanjo yamoto ndipo phiri lonse linagwedezeka kwambiri. 19 Liwu la lipenga linkakulirakulira. Tsono Mose anayankhula ndipo Yehova anamuyankha ndi mabingu.
20 Yehova anatsika nafika pamwamba pa phiri la Sinai, ndipo anayitana Mose kuti apite pa phiripo. Choncho Mose anakwera, 21 ndipo Yehova anati kwa iye, “Tsika ukawachenjeze anthu kuti asayesere kudutsa malire kuti adzandione chifukwa ambiri a iwo adzafa. 22 Ngakhale ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova ayenera kudziyeretsa kuopa kuti ndingadzawalange.”
23 Mose anati kwa Yehova, “Anthu sangakwere phiri la Sinai chifukwa inu munatichenjeza. Lembani malire kuzungulira phiri ndipo mulipatule kuti likhale loyera.”
24 Yehova anayankha, “Tsika ukamutenge Aaroni. Koma ansembe ndi anthu asayesere kubzola malire kuti abwere kwa Yehova chifukwa Iye adzawalanga.”
25 Ndipo Mose anatsika ndi kukawawuza anthuwo.
2 Amuna ena anabwera ndi munthu wakufa ziwalo kwa Iye atamugoneka pa mphasa. Yesu ataona chikhulupiriro chawo anati kwa wakufa ziwaloyo, “Limba mtima mwana wanga, machimo ako akhululukidwa.”
3 Pamenepo aphunzitsi ena amalamulo anaganiza mu mtima mwawo kuti, “Munthu uyu akuchitira Mulungu mwano.”
4 Ndipo podziwa maganizo awo Yesu anati, “Bwanji mukuganiza zoyipa mʼmitima mwanu? 5 Chapafupi ndi chiti kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa’ kapena kunena kuti, ‘Imirira ndipo yenda?’ 6 Tsono kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko wokhululuka machimo, pamenepo anati kwa wakufa ziwaloyo, ‘Imirira, tenga mphasa yako kazipita kwanu.’ ” 7 Ndipo munthuyo anayimirira napita kwawo. 8 Gulu la anthu litaona izi, linadzazidwa ndi mantha ndipo linalemekeza Mulungu amene anapereka ulamuliro kwa anthu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.