Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 42

BUKU LACHIWIRI

Masalimo 42–72

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora.

42 Monga mbawala ipuma wefuwefu kufunafuna mitsinje yamadzi,
    kotero moyo wanga upuma wefuwefu kufunafuna Inu Mulungu.
Moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Mulungu, lofuna Mulungu wamoyo.
    Kodi ndipite liti kukakumana ndi Mulungu?
Misozi yanga yakhala chakudya changa
    usana ndi usiku,
pamene anthu akunena kwa ine tsiku lonse kuti,
    “Mulungu wako ali kuti?”
Zinthu izi ndimazikumbukira
    pamene ndikukhuthula moyo wanga:
momwe ndinkapitira ndi gulu lalikulu,
    kutsogolera mayendedwe a ku Nyumba ya Mulungu
ndi mfuwu yachimwemwe ndi mayamiko
    pakati pa anthu a pa chikondwerero.

Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni, iwe moyo wanga?
    Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga?
Yembekezera Mulungu,
    pakuti ndidzamulambirabe,
Mpulumutsi wanga ndi     Mulungu wanga.

Moyo wanga uli ndi chisoni mʼkati mwanga
    kotero ndidzakumbukira Inu
kuchokera ku dziko la Yorodani,
    ku mitunda ya Herimoni kuchokera ku phiri la Mizara.
Madzi akuya akuyitana madzi akuya
    mu mkokomo wa mathithi anu;
mafunde anu onse obwera mwamphamvu
    andimiza.

Koma usana Yehova amalamulira chikondi chake,
    nthawi ya usiku nyimbo yake ili nane;
    pemphero kwa Mulungu wa moyo wanga.

Ine ndikuti kwa Mulungu Thanthwe langa,
    “Nʼchifukwa chiyani mwandiyiwala?
Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira,
    woponderezedwa ndi mdani?”
10 Mafupa anga ali ndi ululu wakufa nawo
    pamene adani anga akundinyoza,
tsiku lonse akunena kuti,
    “Mulungu wako ali kuti?”

11 Bwanji ukumva chisoni,
    iwe mtima wanga?
Chifukwa chiyani ukuvutika chonchi mʼkati mwanga?
    Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandanso,
    Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.

Eksodo 18:13-27

13 Mmawa mwake, Mose anakhala pa mpando kuti aweruze milandu ya anthu. Anthu anayima momuzungulira kuyambira mmawa mpaka madzulo. 14 Mpongozi wa Mose ataona zonse zimene iye amawachitira anthu anati, “Nʼchiyani chimene mukuwachitira anthuwa? Nʼchifukwa chiyani mulipo nokha woweruza, pamene anthu onsewa ayimirira kuyambira mmawa mpaka madzulo?”

15 Mose anamuyankha kuti, “Chifukwa anthuwa anabwera kwa ine kudzafunsa zimene Mulungu akufuna. 16 Ngati munthu akangana ndi mʼbale wake, onse awiri amabwera kwa ine, ndipo ine ndimawaweruza. Ndimawawuzanso malamulo a Mulungu ndi malangizo ake.”

17 Mpongozi wa Mose anayankha kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwino. 18 Ntchitoyi ndi yayikulu kuposa mphamvu zanu. Inu simungathe kuyigwira nokha. Inu pamodzi ndi anthuwa amene amabwera kwa inu mudzatopa. 19 Tsono tamverani ndikulangizeni, ndipo Mulungu akhale nanu. Inu muziwayimirira anthuwa pamaso pa Mulungu, ndipo mikangano yawo muzibwera nayo kwa Iye. 20 Aphunzitseni mawu ndi malangizo a Mulungu. Aphunzitseni mmene ayenera kukhalira ndi zimene ayenera kuchita. 21 Koma sankhani amuna odziwa ntchito yawo, anthu owopa Mulungu, anthu odalirika amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo. Tsono muwayike kuti akhale oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50 ndi ena a anthu khumi. 22 Tsono amenewa aziweruza anthu nthawi zonse. Mlandu uliwonse waukulu azibwera nawo kwa inu, koma mlandu waungʼono aziweruza okha. Izi zidzachititsa kuti ntchito yanu ipepuke, popeza mudzagwira ntchito mothandizana. 23 Ngati mutsatira malangizowa monga mmene Mulungu wakulamulirani ndiye kuti simudzafowoka ndipo anthu onsewa adzapita kwawo mu mtendere.”

24 Mose anamvera mpongozi wake ndi kuchita zonse zimene iye ananena. 25 Iye anasankha amuna odziwa bwino ntchito zawo ndipo anawayika kuti akhale atsogoleri, oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 500, ena a anthu makumi asanu ndi ena a anthu khumi. 26 Iwowa ankaweruza anthu nthawi zonse. Milandu yovuta ankabwera nayo kwa Mose, koma yosavuta ankayiweruza okha.

27 Kenaka Mose analola kuti mpongozi wake, Yetero anyamuke kubwerera ku dziko la kwawo.

Afilipi 1:15-21

15 Nʼzoonadi kuti ena amalalikira Khristu chifukwa cha kaduka ndi mikangano, koma ena chifukwa cha zolinga zabwino. 16 Olalikira ndi zolinga zabwinowa amachita izi mwachikondi, podziwa kuti ine ndili muno chifukwa cha kuteteza Uthenga Wabwino. 17 Ena aja amalalikira Khristu modzikonda osati moona mtima namaganiza kuti kutero kubweretsa mavuto pamene ndili mʼmaunyolo. 18 Nanga kodi zimenezo zili ndi ntchito? Chofunika ndi chakuti Khristu alalikidwe, kaya ndi mwachinyengo kapena moona. Ndipo ndikukondwera chifukwa cha chimenechi.

Ndithu, ndidzapitirira kukondwera, 19 pakuti ndikudziwa kuti chifukwa cha mapemphero anu ndi thandizo lochokera kwa Mzimu wa Yesu Khristu, zimene zandionekera zidzathandiza kuti ndimasulidwe. 20 Ndili ndi chiyembekezo chonse kuti sindidzachita manyazi ndi pangʼono pomwe, koma ndidzakhala ndi chilimbikitso chokwanira kuti monga mwa nthawi zonse, tsopano Khristu adzakwezedwa mʼthupi langa kaya ndi mʼmoyo kapena mu imfa. 21 Pakuti kwa ine kukhala moyo ndi Khristu ndipo kufa ndi phindu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.