Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Madzi Otuluka Mʼthanthwe
17 Gulu lonse la Aisraeli linachoka ku chipululu cha Sini, ndi kumayenda malo ndi malo monga momwe anawalamulira Yehova. Iwo anamanga misasa yawo ku Refidimu koma kunalibe madzi woti anthu onse ndi kumwa. 2 Kotero iwo anakangana ndi Mose nati, “Tipatse madzi akumwa.”
Mose anayankha kuti, “Chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? Chifukwa chiyani mukumuyesa Yehova?”
3 Koma anthu anali ndi ludzu pamenepo ndipo anangʼungʼudza pamaso pa Mose namufunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani unatitulutsa mʼdziko la Igupto kuti ife, ana athu pamodzi ndi ziweto zathu tife ndi ludzu?”
4 Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, “Kodi ndichite chiyani ndi anthu awa? Iwo atsala pangʼono kundigenda ndi miyala.”
5 Yehova anati kwa Mose, “Pita patsogolo pa anthuwo. Tenga ndodo imene unamenyera nyanja ya Nailo pamodzi ndi akuluakulu ena a Israeli ndi kunyamuka. 6 Ine ndidzayima patsogolo pako pafupi ndi thanthwe la ku Horebu. Ukamenye thanthwelo, madzi adzatuluka kuti anthu amwe.” Motero Mose anachita zimenezi pamaso pa akuluakulu a Israeli. 7 Ndipo iye anatcha malowo Masa ndi Meriba chifukwa Aisraeli anakangana ndi kuyesa Yehova ponena kuti, “Kodi pakati pathu pali Yehova kapena palibe?”
Ndakatulo ya Asafu.
78 Inu anthu anga imvani chiphunzitso changa;
mvetserani mawu a pakamwa panga.
2 Ndidzatsekula pakamwa panga mʼmafanizo,
ndidzayankhula zinthu zobisika, zinthu zakalekale
3 zimene tinazimva ndi kuzidziwa,
zimene makolo athu anatiwuza.
4 Sitidzabisira ana awo,
tidzafotokozera mʼbado wotsatira
ntchito zotamandika za Yehova,
mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.
12 Iyeyo anachita zodabwitsa makolo athu akuona,
mʼdziko la Igupto, mʼchigawo cha Zowani.
13 Anagawa nyanja pakati ndi kudutsitsapo iwowo,
Iye anachititsa madzi kuyima chilili ngati khoma.
14 Anawatsogolera ndi mtambo masana
ndi kuwala kwa moto usiku wonse.
15 Iye anangʼamba miyala mʼchipululu
ndi kuwapatsa madzi ochuluka ngati a mʼnyanja zambiri;
16 Anatulutsa mitsinje kuchokera mʼmingʼalu ya miyala
ndi kuyenda madzi ngati mitsinje.
Kutsanzira Kudzichepetsa kwa Khristu
2 Ngati muli ndi chilimbikitso chilichonse chifukwa cholumikizana ndi Khristu, ngati muli ndi chitonthozo chifukwa cha chikondi chake, ngati muli ndi mtima umodzi mwa Mzimu, ndipo ngati mumakomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, 2 tsono tsirizani chimwemwe changa pokhala amaganizo ofanana, achikondi chimodzimodzi, amodzi mu mzimu ndi acholinga chimodzinso. 3 Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo. 4 Musamangofuna zokomera inu nokha koma aliyense azifuna zokomeranso ena.
5 Pa ubale wanu wina ndi mnzake, mukhale ndi mtima wofanana ndi wa Khristu Yesu:
6 Iyeyu, pokhala Mulungu ndithu,
sanatenge kufanana ndi Mulungu kukhala chinthu choyenera kuchigwiritsa.
7 Koma anadzichepetsa kotheratu
nakhala ndi khalidwe ngati la kapolo
ndi kukhala munthu ngati anthu ena onse.
8 Ndipo pokhala munthu choncho
anadzichepetsa yekha
ndipo anamvera mpaka imfa yake,
imfa yake ya pamtanda!
9 Choncho Mulungu anamukweza Iye kukhala wapamwamba kwambiri,
ndipo anamupatsa dzina loposa dzina lina lililonse
10 kuti pakumva dzina la Yesu, bondo lililonse limugwadire,
kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi pansi pa dziko,
11 ndipo lilime lililonse livomereze kuti Yesu Khristu ndi Ambuye
kuchitira ulemu Mulungu Atate.
Kuwala monga Nyenyezi
12 Tsono, abwenzi anga okondedwa, monga mwakhala omvera nthawi zonse, osati pamene ndinali nanu pokha, koma tsopano koposa pamene ndili kutali. Pitirizani kugwira ntchito ya chipulumutso chanu mwa mantha ndi kunjenjemera, 13 pakuti ndi Mulungu amene amagwira ntchito mwa inu kuti mufune ndi kuchita zimene zimamukondweretsa Iyeyo.
Amufunsa Yesu za Ulamuliro Wake
23 Yesu analowa mʼNyumba ya Mulungu, ndipo pamene ankaphunzitsa, akulu a ansembe ndi akuluakulu anabwera kwa Iye namufunsa kuti, “Muchita izi ndi ulamuliro wanji ndipo anakupatsani ndani ulamuliro umenewu?”
24 Yesu anayankha kuti, “Inenso ndikufunsani funso limodzi, mukandiyankha, Inenso ndikukuwuzani ndi ulamuliro wa yani umene ndikuchitira izi. 25 Ubatizo wa Yohane unachokera kuti? Kumwamba kapena kwa anthu?”
Anakambirana pakati pawo ndipo anati, “Tikati, ‘Kuchokera kumwamba,’ Iye adzafunsa kuti, ‘Bwanji simunakhulupirire?’ 26 Koma tikati, ‘Kuchokera kwa anthu,’ ife tikuopa anthuwa, pakuti onse amakhulupirira kuti Yohane anali mneneri.”
27 Choncho anamuwuza Yesu kuti, “Sitikudziwa.”
Pamenepo Iye anati, “Inenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wa yani umene ndichitira izi.”
Fanizo la Ana Amuna Awiri
28 “Kodi muganiza bwanji? Panali munthu wina anali ndi ana aamuna awiri. Anapita kwa woyamba nati, ‘Mwanawe pita kagwire ntchito lero mʼmunda wamphesa.’
29 “Iye anayankha kuti, ‘Sindipita,’ koma pambuyo pake anasintha maganizo napita.
30 “Kenaka abambowo anapita kwa mwana winayo nanena chimodzimodzi. Iye anayankha kuti, ‘Ndipita abambo,’ koma sanapite.
31 “Ndani wa awiriwa anachita chimene abambo ake amafuna?”
Anamuyankha nati, “Woyambayo.”
Yesu anawawuza kuti, “Ndikuwuzani zoonadi, kuti amisonkho ndi adama akulowa mu ufumu wa Mulungu inu musanalowemo.” 32 Pakuti Yohane anabwera kwa inu kuti akuonetseni njira yachilungamo, koma inu simunakhulupirire iye, koma amisonkho ndi adama anamukhulupirira. Koma ngakhale munaona izi, simunatembenuke mtima ndi kumukhulupirira iye.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.