Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 78:1-4

Ndakatulo ya Asafu.

78 Inu anthu anga imvani chiphunzitso changa;
    mvetserani mawu a pakamwa panga.
Ndidzatsekula pakamwa panga mʼmafanizo,
    ndidzayankhula zinthu zobisika, zinthu zakalekale
zimene tinazimva ndi kuzidziwa,
    zimene makolo athu anatiwuza.
Sitidzabisira ana awo,
    tidzafotokozera mʼbado wotsatira
ntchito zotamandika za Yehova,
    mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.

Masalimo 78:12-16

12 Iyeyo anachita zodabwitsa makolo athu akuona,
    mʼdziko la Igupto, mʼchigawo cha Zowani.
13 Anagawa nyanja pakati ndi kudutsitsapo iwowo,
    Iye anachititsa madzi kuyima chilili ngati khoma.
14 Anawatsogolera ndi mtambo masana
    ndi kuwala kwa moto usiku wonse.
15 Iye anangʼamba miyala mʼchipululu
    ndi kuwapatsa madzi ochuluka ngati a mʼnyanja zambiri;
16 Anatulutsa mitsinje kuchokera mʼmingʼalu ya miyala
    ndi kuyenda madzi ngati mitsinje.

Yesaya 48:17-21

17 Yehova, Mpulumutsi wanu,
    Woyerayo wa Israeli akuti,
“Ine ndine Yehova Mulungu wanu,
    amene ndimakuphunzitsa kuti upindule,
    ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuyitsata.
18 Ngati iwe ukanangosamalira zolamulira zanga,
    bwenzi mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje,
    ndi chipulumutso chako ngati mafunde a pa nyanja.
19 Zidzukulu zako zikanachuluka ngati mchenga,
    ana ako akanachuluka ngati fumbi;
dzina lawo silikanachotsedwa pamaso panga
    ndipo silikanafafanizidwa konse.”

20 Tulukani mʼdziko la Babuloni!
    Thawani dziko la Kaldeya!
Lengezani zimenezi ndi mawu a chisangalalo
    ndipo muzilalikire
mpaka kumathero a dziko lapansi;
    muzinena kuti, “Yehova wawombola Yakobo mtumiki wake.”
21 Iwo sanamve ludzu pamene Yehova ankawatsogolera mʼchipululu;
    anawapatsa madzi otuluka mʼthanthwe;
anangʼamba thanthwelo ndipo
    munatuluka madzi.

Yakobo 4:11-16

11 Abale musamanenane. Aliyense wonenera zoyipa mʼbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo. Pamene muweruza malamulo, ndiye kuti simukusunga malamulowo, koma mukuwaweruza. 12 Pali mmodzi yekha Wopereka Malamulo ndi Woweruza. Ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuwononga. Kodi ndiwe yani kuti uziweruza mnzako?

Kunyadira za Mawa

13 Tsono tamverani, inu amene mumati, “Lero kapena mawa tipita ku mzinda wakutiwakuti, tikatha chaka chimodzi tikuchita malonda ndi kupanga ndalama.” 14 Chifukwa chiyani mukutero? Inu simukudziwa zimene ziti zichitike mawa. Kodi moyo wanu ndi wotani? Inu muli ngati nkhungu imene imangooneka kwa kanthawi kochepa ndipo kenaka ndikuzimirira. 15 Koma inuyo muyenera kunena kuti, “Ambuye akalola, tikadzakhala ndi moyo, tidzachita zakutizakuti.” 16 Koma mmene zililimu mumangodzitama ndi kudzikuza. Kudzitama konse kotereku ndi koyipa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.