Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 119:97-104

Memu

97 Ndithu, ine ndimakonda malamulo anu!
    Ndimalingaliramo tsiku lonse.
98 Malamulo anu amachititsa kuti ndikhale wanzeru kuposa adani anga,
    popeza malamulowo ali ndi ine nthawi zonse.
99 Ndimamvetsa zinthu kwambiri kuposa aphunzitsi anga onse
    popeza ndimalingalira umboni wanu.
100 Ndili ndi nzeru zochuluka zomvetsera zinthu kuposa anthu okalamba,
    popeza ndimamvera malangizo anu.
101 Ndimaletsa miyendo yanga kuyenda mʼnjira iliyonse yoyipa
    kuti ndithe kumvera mawu anu.
102 Sindinapatuke kuchoka pa malamulo anu,
    pakuti Inu mwini munandiphunzitsa.
103 Mawu anu ndi otsekemera ndikawalawa,
    otsekemera kuposa uchi mʼkamwa mwanga!
104 Ndimapeza nzeru zodziwira zinthu kuchokera mʼmalangizo anu;
    kotero ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa.

Numeri 11:18-23

18 “Uwawuze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse, kukonzekera mawa, pamene mudzadya nyama.’ Yehova anakumvani pamene munkalira kuti, ‘Zikanakhala bwino tikanapeza nyama yoti tidye! Tinkakhala bwino ku Igupto!’ Tsopano Yehova adzakupatsani nyama ndipo mudzayidyadi. 19 Simudzadya tsiku limodzi lokha, kapena masiku awiri, kapena asanu, khumi kapena masiku makumi awiri, 20 koma mwezi wonse, mpaka itakukolani ndi kutopa nayo chifukwa mwakana Yehova yemwe ali pakati panu ndipo mwalira pamaso pake kuti, ‘Bwanji tinachoka ku Igupto?’ ”

21 Koma Mose anati, “Taonani pano ndili pakati pa anthu 600,000 amene ndi kuyenda nawo ndipo Inuyo mukuti, ‘Ndidzawapatsa nyama kuti adye mwezi wathunthu!’ 22 Kodi ngakhale titapha nkhosa ndi ngʼombe, zingawakwanire? Ngakhale titagwira nsomba zonse za mʼnyanja, kodi zingawakwanire iwowa?”

23 Yehova anayankha Mose kuti, “Kodi dzanja langa ndi lalifupi? Uwona tsopano ngati zimene ndanenazo zichitike kapena ayi.”

Numeri 11:31-32

31 Pamenepo Yehova anawutsa mphepo yochokera ku nyanja imene inabweretsa zinziri. Zinzirizo zinagwera pansi kuzungulira msasa, mtunda wa kilomita imodzi mbali zonse ndipo msinkhu wake unali mita imodzi. 32 Tsiku limenelo masana onse mpaka usiku ndiponso tsiku lotsatiralo, anthu anatuluka kunja kukatola zinziri. Palibe amene anasonkhanitsa zochepera makilogalamu 1,000 ndipo anaziyanika kuzungulira msasa wonse.

Mateyu 18:1-5

Wamkulu mu Ufumu Wakumwamba

18 Pa nthawi imeneyo ophunzira anabwera kwa Yesu ndipo anamufunsa kuti, “Wamkulu woposa onse ndani mu ufumu wakumwamba?”

Iye anayitana kamwana kakangʼono ndi kukayimiritsa pakati pawo. Ndipo Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati simusintha ndi kukhala ngati tiana tatingʼono, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba. Chifukwa chake, aliyense amene adzichepetsa yekha ngati kamwana aka, ameneyo ndiye wamkulu koposa onse mu ufumu wakumwamba. Ndipo aliyense amene alandira kamwana kakangʼono ngati aka mu dzina langa, alandira Ine.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.