Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 119:97-104

Memu

97 Ndithu, ine ndimakonda malamulo anu!
    Ndimalingaliramo tsiku lonse.
98 Malamulo anu amachititsa kuti ndikhale wanzeru kuposa adani anga,
    popeza malamulowo ali ndi ine nthawi zonse.
99 Ndimamvetsa zinthu kwambiri kuposa aphunzitsi anga onse
    popeza ndimalingalira umboni wanu.
100 Ndili ndi nzeru zochuluka zomvetsera zinthu kuposa anthu okalamba,
    popeza ndimamvera malangizo anu.
101 Ndimaletsa miyendo yanga kuyenda mʼnjira iliyonse yoyipa
    kuti ndithe kumvera mawu anu.
102 Sindinapatuke kuchoka pa malamulo anu,
    pakuti Inu mwini munandiphunzitsa.
103 Mawu anu ndi otsekemera ndikawalawa,
    otsekemera kuposa uchi mʼkamwa mwanga!
104 Ndimapeza nzeru zodziwira zinthu kuchokera mʼmalangizo anu;
    kotero ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa.

Numeri 11:1-9

Moto Wochokera kwa Yehova

11 Anthu atadandaula kwa Yehova chifukwa cha mavuto awo, Yehovayo anamva ndipo anakwiya kwambiri. Kenaka moto wa Yehova unayaka pakati pawo ndi kutentha zigawo zina za kunja kwa msasa. Anthuwo analira kwa Mose ndipo Moseyo atapemphera kwa Yehova, motowo unazima. Motero malowo anawatcha Tabera, chifukwa moto wa Yehova unayaka pakati pawo.

Zinziri Zochokera kwa Yehova

Anthu ena osokoneza amene anali pakati pa Aisraeli anayamba kukhumba chakudya cha ku Igupto ndipo Aisraeli nawonso anayamba kufuwula kwambiri nʼkumati, “Tikanangopeza nyama yoti nʼkudya! Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinkadya ku Igupto komanso nkhaka, mavwende, anyezi wamitundumitundu ndi adyo. Koma tsopano chilakolako chathu chatha. Sitikuona kanthu kena kakudya koma mana basi!”

Mana ankafanana ndi mbewu zamapira ndipo maonekedwe ake anali ngati ulimbo wowuma. Anthu ankapita kukatola manawo, nʼkumasinja mu mtondo kapena kupera. Ankawaphika mu mʼphika kapena kupanga makeke. Ndipo ankakoma ngati makeke ophikira mafuta a olivi. Mame akamagwa pa msasawo usiku ankagwera kumodzi ndi manawo.

Aroma 16:17-20

17 Abale, ine ndikukupemphani kuti musamale chifukwa cha amene ayambitsa mipatuko ndi kuyika zokhumudwitsa panjira yanu, motsutsana ndi chiphunzitso chimene mwachiphunzira. Muwapewe iwo. 18 Pakuti otero sakutumikira Ambuye athu Khristu koma zilakolako zawo. Ndi mawu okoma ndi oshashalika iwo amanamiza anthu osalakwa. 19 Aliyense anamva za kumvera kwanu, choncho ndine odzaza ndi chimwemwe chifukwa cha inu. Koma ine ndikufuna kuti inu mukhale anzeru pa zabwino, ndi wopanda cholakwa pa zimene zili zoyipa.

20 Mulungu wamtendere adzaphwanya Satana msanga pansi pa mapazi anu.

Chisomo cha Ambuye athu Yesu chikhale ndi inu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.