Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Eksodo 16:2-15

Mʼchipululumo gulu lonse linadandaulira Mose ndi Aaroni kuti, “Kukanakhala bwino Yehova akanatiphera mʼdziko la Igupto! Kumeneko timadya nyama ndi buledi mpaka kukhuta, koma inu mwabwera nafe ku chipululu kudzapha mpingo wonsewu ndi njala!”

Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzakupatsani buledi wogwa kuchokera kumwamba ngati mvula. Anthu azituluka tsiku lililonse kukatola buledi wokwanira tsiku limenelo. Ine ndidzawayesa mʼnjira imeneyi kuti ndione ngati adzatsatira malangizo anga. Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, pamene azidzakonza buledi amene abwera naye, adzapeza kuti ndi wokwanira masiku awiri.”

Kotero Mose ndi Aaroni anati kwa Aisraeli onse, “Nthawi yamadzulo inu mudzadziwa kuti ndi Yehova amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto. Ndipo mmawa mudzaona ulemerero wa Yehova pakuti wamva kudandaula kwanu. Kodi ife ndi yani kuti muzitidandaulira?” Mose anati, “Yehova adzakupatsani nyama madzulo aliwonse ndi buledi mmawa uliwonse kuti mukhute chifukwa Iye wamva madandawulo anu. Nanga ife ndi yani? Kudandaula kwanu simudandaulira ife, koma Yehova.”

Kenaka Mose anawuza Aaroni kuti, “Uza gulu lonse la Aisraeli kuti, ‘Bwerani pamaso pa Yehova pakuti wamva kudandaula kwanu.’ ”

10 Pamene Aaroni amayankhula ndi gulu lonse la Aisraeli, iwo anayangʼana ku chipululu, ndipo ulemerero wa Yehova umaoneka mu mtambo.

11 Yehova anati kwa Mose, 12 “Ine ndamva kudandaula kwa Aisraeli. Awuze kuti, ‘Madzulo mudzadya nyama ndipo mmawa mudzakhuta buledi. Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”

13 Madzulo amenewo panatuluka zinziri zimene zinali ponseponse pa misasa yawo, ndipo mmawa panali mame kuzungulira misasa yawo. 14 Mamewo atachoka, pa nthaka mʼchipululumo panaoneka tinthu tina topyapyala komanso totuwa ngati chipale. 15 Aisraeli atationa anafunsana wina ndi mnzake nati, “Kodi timeneti nʼchiyani?” Popeza sanatidziwe.

Mose anawawuza kuti, “Uyu ndi buledi amene Yehova wakupatsani kuti mudye.

Masalimo 105:1-6

105 Yamikani Yehova, itanani dzina lake;
    lalikirani pakati pa anthu a mitundu ina zimene Iye wachita.
Imbirani Iye, imbani matamando kwa Iyeyo;
    fotokozani za machitidwe ake onse odabwitsa.
Munyadire dzina lake loyera;
    mitima ya iwo amene amafunafuna Yehova ikondwere.
Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;
    funafunani nkhope yake nthawi yonse.

Kumbukirani zodabwitsa zimene Iye anazichita,
    zozizwitsa zake ndi maweruzo amene anapereka,
inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake,
    inu ana a Yakobo, osankhika ake.

Masalimo 105:37-45

37 Yehova anatulutsa Israeli, atatenga siliva ndi golide wambiri,
    ndipo pakati pa mafuko awo palibe mmodzi amene anafowoka.
38 Dziko la Igupto linakondwa pamene iwo anachoka,
    pakuti kuopsa kwa Israeli kunawagwera iwo.
39 Iye anatambasula mitambo ngati chofunda chawo,
    ndi moto owawunikira usiku.
40 Iwo anapempha, ndipo Iye anawabweretsera zinziri
    ndipo anawakhutitsa ndi chakudya chochokera kumwamba.
41 Iye anatsekula thanthwe, ndipo madzi anatuluka;
    ngati mtsinje anayenda mʼchipululu.

42 Pakuti anakumbukira lonjezo lake loyera limene
    linaperekedwa kwa Abrahamu mtumiki wake.
43 Iye anatulutsa anthu ake akukondwera,
    osankhika ake akufuwula mwachimwemwe;
44 Iye anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina
    ndipo anakhala olowamʼmalo a zimene ena anazivutikira,
45 kuti iwo asunge malangizo ake
    ndi kutsatira malamulo ake.

Tamandani Yehova.

Afilipi 1:21-30

21 Pakuti kwa ine kukhala moyo ndi Khristu ndipo kufa ndi phindu. 22 Ngati nditi ndipitirire kukhala ndi moyo mʼthupi ndiye kuti kwa ine ndi kugwira ntchito yopindulitsa. Kodi ndisankhe chiyani? Sindikudziwa. 23 Ndathinidwa ndi zinthu ziwirizi: Ndikulakalaka kunyamuka kuti ndikakhale ndi Khristu, chimene ndi chinthu chabwino kwambiri. 24 Komanso nʼkofunika kwambiri kuti ndikhalebe mʼthupi chifukwa cha inu. 25 Ndili ndi chitsimikizo, ndikudziwa kuti ndidzakhala ndi moyo ndipo ndidzapitirira nanu kuti nonse mupite mʼtsogolo ndi kukhala ndi chimwemwe mu chikhulupiriro 26 kuti pokhala nanunso, kudzitamandira kwanu mwa Khristu Yesu kudzasefukire chifukwa cha ine.

Moyo Woyenerana ndi Uthenga Wabwino

27 Chilichonse chimene chingachitike, chachikulu nʼchakuti mukhale moyo ofanana ndi Uthenga Wabwino wa Khristu. Tsono ngati ndingabwere kudzakuonani kapena kumangomva za inu ndili kutali, ndidzadziwa kuti mwayima mwamphamvu mwa Mzimu mmodzi, kulimbika pamodzi ngati munthu mmodzi chifukwa cha chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino 28 osachita mantha ndi pangʼono pomwe ndi amene akutsutsana nanu. Ichi ndi chizindikiro kwa iwo kuti adzawonongedwa, koma inu mudzapulumutsidwa ndi Mulungu. 29 Pakuti inu mwapatsidwa mwayi osati ongokhulupirira Khristu kokha, koma wakumva zowawa mʼmalo mwa Khristu. 30 Inunso mukudutsa mʼzowawa zomwe zija munaona ndikudutsamo inenso ndipo pano mukumva kuti ndikukumana nazobe.

Mateyu 20:1-16

Fanizo la Aganyu Mʼmunda wa Mphesa

20 “Ufumu wakumwamba uli ngati mwini munda amene anapita mmawa kukalemba anthu aganyu kuti akagwire ntchito mʼmunda wake wa mpesa. Anagwirizana kuwalipira dinari monga malipiro a tsiku limodzi ndipo anawatumiza mʼmunda wake wamphesa.

“Nthawi 9 koloko mmawa, anatulukanso naona ena atayimirira pa msika akungokhala. Anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa, ndipo ndidzakulipirani malipiro oyenera.’ Ndipo anapita.

“Anatulukanso nthawi ya 12 koloko masana, ndi nthawi ya 3 koloko masananso nachita chimodzimodzi. Nthawi ya 5 koloko madzulo anatulukanso ndipo anapeza enanso atangoyimirira. Anawafunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mukungoyimirira pano tsiku lonse osagwira ntchito?’

“Iwo anayankha kuti, ‘Chifukwa palibe munthu amene watilemba ganyu.’

“Iye anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa.’

“Ndipo pofika madzulo, mwini munda wamphesa anayitana kapitawo wake nati, ‘Itana antchito ndipo uwapatse malipiro awo, kuyambira omalizira aja mpaka oyamba.’

“Antchito amene anawalemba ganyu pa 5 koloko masana anafika ndipo aliyense analandira dinari. 10 Ndipo atabwera kwa amene analembedwa poyamba anayembekezera kuti alandira zambiri. Koma aliyense wa iwo analandira dinari. 11 Atalandira, anayamba kuderera kwa mwini mundayo. 12 Iwo anati, ‘Anthu amene munawalemba pomalizira agwira ntchito ora limodzi, ndipo mwawafananitsa ndi ife amene tathyoka nayo ntchito ndi kutentha kwa dzuwa tsiku lonse.’

13 “Koma iye anamuyankha mmodzi wa iwo nati, ‘Bwenzi, ine sikuti sindinachite chilungamo. Kodi sunavomereze kuti ugwira ntchito ndi kulandira dinari? 14 Tenga malipiro ako pita. Ndikufuna kumupatsa munthu amene ndinamulemba pomaliza mofanana ndi mmene ndakupatsira iwe. 15 Kodi ndilibe ufulu wochita zimene ndikufuna ndi ndalama zanga? Kapena ukuyipidwa chifukwa ndine wopereka mowolowamanja?’

16 “Momwemo omalizira adzakhala oyamba ndipo oyamba adzakhala omalizira.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.