Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
105 Yamikani Yehova, itanani dzina lake;
lalikirani pakati pa anthu a mitundu ina zimene Iye wachita.
2 Imbirani Iye, imbani matamando kwa Iyeyo;
fotokozani za machitidwe ake onse odabwitsa.
3 Munyadire dzina lake loyera;
mitima ya iwo amene amafunafuna Yehova ikondwere.
4 Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;
funafunani nkhope yake nthawi yonse.
5 Kumbukirani zodabwitsa zimene Iye anazichita,
zozizwitsa zake ndi maweruzo amene anapereka,
6 inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake,
inu ana a Yakobo, osankhika ake.
37 Yehova anatulutsa Israeli, atatenga siliva ndi golide wambiri,
ndipo pakati pa mafuko awo palibe mmodzi amene anafowoka.
38 Dziko la Igupto linakondwa pamene iwo anachoka,
pakuti kuopsa kwa Israeli kunawagwera iwo.
39 Iye anatambasula mitambo ngati chofunda chawo,
ndi moto owawunikira usiku.
40 Iwo anapempha, ndipo Iye anawabweretsera zinziri
ndipo anawakhutitsa ndi chakudya chochokera kumwamba.
41 Iye anatsekula thanthwe, ndipo madzi anatuluka;
ngati mtsinje anayenda mʼchipululu.
42 Pakuti anakumbukira lonjezo lake loyera limene
linaperekedwa kwa Abrahamu mtumiki wake.
43 Iye anatulutsa anthu ake akukondwera,
osankhika ake akufuwula mwachimwemwe;
44 Iye anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina
ndipo anakhala olowamʼmalo a zimene ena anazivutikira,
45 kuti iwo asunge malangizo ake
ndi kutsatira malamulo ake.
Tamandani Yehova.
Mana ndi Zinziri
16 Pambuyo pake gulu lonse la Aisraeli linachoka ku Elimu, ndipo pa tsiku la khumi ndi chisanu mwezi wachiwiri chichokere mʼdziko la Igupto, anafika ku chipululu cha Sini chimene chinali pakati pa Elimu ndi Sinai. 2 Mʼchipululumo gulu lonse linadandaulira Mose ndi Aaroni 3 kuti, “Kukanakhala bwino Yehova akanatiphera mʼdziko la Igupto! Kumeneko timadya nyama ndi buledi mpaka kukhuta, koma inu mwabwera nafe ku chipululu kudzapha mpingo wonsewu ndi njala!”
4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzakupatsani buledi wogwa kuchokera kumwamba ngati mvula. Anthu azituluka tsiku lililonse kukatola buledi wokwanira tsiku limenelo. Ine ndidzawayesa mʼnjira imeneyi kuti ndione ngati adzatsatira malangizo anga. 5 Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, pamene azidzakonza buledi amene abwera naye, adzapeza kuti ndi wokwanira masiku awiri.”
6 Kotero Mose ndi Aaroni anati kwa Aisraeli onse, “Nthawi yamadzulo inu mudzadziwa kuti ndi Yehova amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto. 7 Ndipo mmawa mudzaona ulemerero wa Yehova pakuti wamva kudandaula kwanu. Kodi ife ndi yani kuti muzitidandaulira?” 8 Mose anati, “Yehova adzakupatsani nyama madzulo aliwonse ndi buledi mmawa uliwonse kuti mukhute chifukwa Iye wamva madandawulo anu. Nanga ife ndi yani? Kudandaula kwanu simudandaulira ife, koma Yehova.”
9 Kenaka Mose anawuza Aaroni kuti, “Uza gulu lonse la Aisraeli kuti, ‘Bwerani pamaso pa Yehova pakuti wamva kudandaula kwanu.’ ”
10 Pamene Aaroni amayankhula ndi gulu lonse la Aisraeli, iwo anayangʼana ku chipululu, ndipo ulemerero wa Yehova umaoneka mu mtambo.
11 Yehova anati kwa Mose, 12 “Ine ndamva kudandaula kwa Aisraeli. Awuze kuti, ‘Madzulo mudzadya nyama ndipo mmawa mudzakhuta buledi. Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”
13 Madzulo amenewo panatuluka zinziri zimene zinali ponseponse pa misasa yawo, ndipo mmawa panali mame kuzungulira misasa yawo. 14 Mamewo atachoka, pa nthaka mʼchipululumo panaoneka tinthu tina topyapyala komanso totuwa ngati chipale. 15 Aisraeli atationa anafunsana wina ndi mnzake nati, “Kodi timeneti nʼchiyani?” Popeza sanatidziwe.
Mose anawawuza kuti, “Uyu ndi buledi amene Yehova wakupatsani kuti mudye. 16 Yehova walamula kuti, ‘Aliyense atole zomukwanira kudya, malita awiri pa munthu mmodzi molingana ndi chiwerengero cha anthu amene ali mu tenti yanu.’ ”
17 Aisraeli anachita zonse anawawuza. Ena anatola zambiri ena zochepa. 18 Ndipo iwo atayeza ndi muyeso wa malita awiri, iye amene anatola zambiri sizinamutsalireko ndipo amene anatola pangʼono sizinamuchepere. Aliyense anatola zomukwanira kudya.
19 Ndipo Mose anawawuza kuti, “Wina aliyense asasunge mpaka mmawa.”
20 Komabe ena sanamvere Mose, anasungako mpaka mmawa. Koma mmawa mwake tonse tinali mphutsi zokhazokha. Kotero Mose anawapsera mtima.
21 Mmawa uliwonse aliyense amatola zimene amazifuna, ndipo dzuwa likatentha zimasungunuka.
5 Tadzisanthulani nokha kuti muone ngati muli mʼchikhulupiriro; dziyeseni nokha. Kodi simuzindikira kuti Khristu Yesu ali mwa inu, ngati si choncho mwalephera mayesowa? 6 Ndipo ndikhulupirira kuti mudzazindikira kuti ife sitinalephere mayesowo. 7 Tsopano tikupemphera kwa Mulungu kuti musadzachite kanthu kena kalikonse kolakwa. Osati chifukwa choti anthu aone kuti ife tapambana mayesowo koma kuti mudzachite zokhoza ngakhale anthu atamationa ngati olephera. 8 Pakuti sitingachite chilichonse chotsutsana ndi choonadi, koma chokhacho chovomerezana ndi choonadi. 9 Ife timasangalala kuti pamene tafowoka, inu muli amphamvu; ndipo pemphero lathu ndi lakuti mukhale angwiro. 10 Nʼchifukwa chake ndimalemba zinthu zoterezi pamene ndili kutali, kuti ndikabwera ndisadzagwiritse ntchito ulamuliro wanga mokalipa, uwu ndi ulamuliro umene Ambuye anandipatsa kuti ndikukuzeni inu osati kukuwonongani.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.