Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 77

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Asafu.

77 Ndinafuwulira Mulungu kupempha thandizo;
    ndinafuwula mokweza kwa Mulungu kuti anditcherere khutu.
Pamene ndinali pa masautso ndinafunafuna Ambuye;
    usiku ndinatambasula manja mosalekeza
    ndipo moyo wanga unakana kutonthozedwa.

Ndinakumbukira Inu Mulungu, ndipo ndinabuwula;
    ndinasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unalefuka.
            Sela
Munagwira zikope zanga kuti ndisagone
    ndipo ndinavutika kwambiri kuti ndiyankhule.
Ndinaganizira za masiku akale,
    zaka zamakedzana;
Ndinakumbukira nyimbo zanga usiku.
    Mtima wanga unasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unafunsa kuti,

“Kodi Ambuye adzatikana mpaka muyaya?
    Kodi Iwo sadzaonetsanso kukoma mtima kwawo?
Kodi Chikondi chake chosatha chija chatheratu?
    Kodi malonjezo ake alephera nthawi yonse?
Kodi Mulungu wayiwala kukhala wokoma mtima?
    Kodi mu mkwiyo wake waleka chifundo chake?”

10 Ndipo ndinaganiza, “Pa izi ine ndidzapemphanso:
    zaka za dzanja lamanja la Wammwambamwamba.
11 Ine ndidzakumbukira ntchito za Yehova;
    Ine ndidzakumbukira zodabwitsa zanu za kalekale.
12 Ndidzakumbukira ntchito zanu
    ndi kulingalira zodabwitsa zanu.”

13 Njira zanu Mulungu ndi zoyera.
    Kodi ndi mulungu uti ali wamkulu kuposa Mulungu wathu?
14 Inu ndinu Mulungu wochita zodabwitsa;
    Mumaonetsera mphamvu yanu pakati pa mitundu ya anthu.
15 Ndi dzanja lanu lamphamvu munawombola anthu anu,
    zidzukulu za Yakobo ndi Yosefe.
            Sela

16 Madzi anakuonani Mulungu,
    madzi anakuonani ndipo anachita mantha;
    nyanja yozama inakomoka.
17 Mitambo inakhuthula madzi ake pansi,
    mu mlengalenga munamveka mabingu;
    mivi yanu inawuluka uku ndi uku.
18 Bingu lanu linamveka mʼmphepo ya kamvuluvulu,
    mphenzi yanu inawalitsa dziko lonse;
    dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.
19 Njira yanu inadutsa pa nyanja,
    njira yanu inadutsa pa madzi amphamvu,
    ngakhale zidindo za mapazi anu sizinaoneke.

20 Inu munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa
    mwa dzanja la Mose ndi Aaroni.

Nehemiya 9:9-15

“Munaona kuzunzika kwa makolo athu ku Igupto. Munamva kufuwula kwawo pa Nyanja Yofiira. 10 Inu munachita zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa kutsutsana ndi Farao, pamaso pa Farao, nduna zake ndi anthu onse a mʼdziko lake, pakuti Inu munadziwa kuti anazunza makolo athu. Inu munadzipangira nokha dzina, monga zilili mpaka lero lino. 11 Inu munagawa nyanja anthu anu akupenya, kotero kuti anadutsa powuma, koma munamiza mʼmadzi akuya anthu amene ankawalondola monga mmene uchitira mwala mʼmadzi ozama. 12 Masana munkawunikira ndi chipilala cha mtambo ndipo usiku munkawunikira ndi chipilala cha moto njira yonse imene ankayendamo.

13 “Munatsika pa Phiri la Sinai, ndipo munawayankhula kuchokera kumwamba. Munawapatsa malangizo olungama, ziphunzitso zoona ndiponso malamulo abwino. 14 Inu munawadziwitsa kuti tsiku lanu la Sabata ndi loyera ndipo munawapatsa malamulo ndi ziphunzitso. 15 Pamene anali ndi njala munawapatsa buledi wochokera kumwamba. Pamene anali ndi ludzu munawapatsa madzi otuluka mʼthanthwe. Munawawuza kuti apite kukalanda dziko limene munalonjeza kuti mudzawapatsa.”

Aroma 14:13-15:2

13 Motero, tiyeni tisiye kuweruzana wina ndi mnzake. Mʼmalo mwake, tsimikizani mʼmaganizo anu kuti musayike chokhumudwitsa kapena chotchinga mʼnjira ya mʼbale wanu. 14 Monga mmodzi amene ndili mwa Ambuye Yesu, ndine wotsimikiza mtima kuti palibe chakudya chimene pachokha ndi chodetsedwa. Koma ngati wina atenga china chake kukhala chodetsedwa, kwa iyeyo ndi chodetsedwa. 15 Ngati mʼbale wako akuvutika chifukwa cha chimene umadya, iwe sukuchitanso mwachikondi. Usamuwononge mʼbale wako amene Khristu anamufera chifukwa cha chakudya chakocho. 16 Musalole kuti chimene muchiyesa chabwino achinene ngati choyipa. 17 Pakuti Ufumu wa Mulungu si nkhani yakudya ndi kumwa, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera. 18 Nʼchifukwa chake aliyense amene atumikira Khristu mʼnjira iyi akondweretsa Mulungu ndi kuvomerezedwa ndi anthu.

19 Tsono tiyeni tiyesetse kuchita zimene zidzabweretsa mtendere ndi kulimbikitsana mwachikondi. 20 Musawononge ntchito ya Mulungu chifukwa cha chakudya. Chakudya chonse ndi choyera, koma munthu amalakwa ngati adya chilichonse chimene chimakhumudwitsa wina. 21 Nʼkwabwino kusadya kapena kumwa vinyo kapena kuchita chilichonse chimene chidzachititsa mʼbale wako kugwa.

22 Tsono zimene ukukhulupirira pa zinthu izi zikhale pakati pa iwe ndi Mulungu. Wodala munthu amene sadzitsutsa yekha pa zimene amazivomereza. 23 Koma munthu amene akukayika atsutsidwa ngati adya, chifukwa kudya kwake si kwa chikhulupiriro; ndipo chilichonse chosachokera mʼchikhulupiriro ndi tchimo.

15 Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu tiziwalezera mtima anthu ofowoka, ndipo tisamadzikondweretse tokha. Aliyense wa ife akondweretse mnzake pomuchitira zabwino zomulimbikitsa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.