Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
114 Pamene Israeli anatuluka mu Igupto,
nyumba ya Yakobo kuchoka ku mtundu wa anthu a chiyankhulo chachilendo,
2 Yuda anasanduka malo opatulika a Mulungu,
Israeli anasanduka ufumu wake.
3 Nyanja inaona ndi kuthawa,
mtsinje wa Yorodani unabwerera mʼmbuyo;
4 mapiri analumphalumpha ngati nkhosa zazimuna,
timapiri ngati ana ankhosa.
5 Nʼchifukwa chiyani iwe unathawa?
iwe mtsinje wa Yorodani unabwereranji mʼmbuyo?
6 inu mapiri, munalumphalumphiranji ngati nkhosa zazimuna,
inu timapiri, ngati ana ankhosa?
7 Njenjemera pamaso pa Ambuye iwe dziko lapansi,
pamaso pa Mulungu wa Yakobo,
8 amene anasandutsa thanthwe kukhala chitsime,
thanthwe lolimba kukhala akasupe a madzi.
Kuwoloka Nyanja
17 Farao atalola anthu aja kuti atuluke, Mulungu sanawadzeretse njira yodutsa dziko la Afilisti, ngakhale kuti inali yachidule popeza Mulungu anati, “Ngati anthuwa atadzakumana ndi nkhondo angadzakhumudwe ndi kubwerera ku Igupto.” 18 Choncho Mulungu anawadzeretsa anthuwo njira yozungulira ya mʼchipululu kulowera ku Nyanja Yofiira. Komabe Aisraeli anatuluka mʼdziko la Igupto atakonzekera nkhondo.
19 Mose ananyamula mafupa a Yosefe chifukwa Yosefe anawalumbiritsa ana a Israeli. Iye anawawuza kuti, “Mulungu adzabwera ndithu kudzakuthandizani, ndipo mudzanyamule mafupa anga pochoka ku malo ano.”
20 Atachoka ku Sukoti anakagona ku Etamu mʼmphepete mwa chipululu. 21 Nthawi yamasana Yehova amakhala patsogolo pa anthu kuwatsogolera njira ndi chipilala cha mtambo, ndipo usiku Yehova ankawatsogolera ndi chipilala cha moto, kuwawunikira njira kuti athe kuyenda masana ndi usiku. 22 Usana, chipilala cha mtambo ndi usiku, chipilala cha moto zinali patsogolo kuwatsogolera anthu aja.
Kukondana Wina ndi Mnzake
11 Uthenga umene munawumva kuyambira pachiyambi ndi uwu: Tizikondana wina ndi mnzake. 12 Musakhale ngati Kaini, amene anali wa woyipayo ndipo anapha mʼbale wake. Nanga anamupha chifukwa chiyani? Chifukwa zochita zake zinali zoyipa ndipo zochita za mʼbale wake zinali zolungama. 13 Abale anga, musadabwe ngati dziko lapansi lidana nanu. 14 Ife tikudziwa kuti tinatuluka mu imfa ndi kulowa mʼmoyo, chifukwa timakonda abale athu. Aliyense amene sakonda mʼbale wake akanali mu imfa. 15 Aliyense amene amadana ndi mʼbale wake ndi wakupha, ndipo inu mukudziwa kuti wopha anthu mwa iye mulibe moyo wosatha.
16 Mmene timadziwira chikondi chenicheni ndi umu: Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Ndipo nafenso tiyenera kupereka miyoyo yathu chifukwa cha abale athu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.