Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
149 Tamandani Yehova.
Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,
matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima.
2 Israeli asangalale mwa mlengi wake;
anthu a ku Ziyoni akondwere mwa Mfumu yawo.
3 Atamande dzina lake povina
ndi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe.
4 Pakuti Yehova amakondwera ndi anthu ake;
Iye amaveka chipulumutso odzichepetsa.
5 Oyera mtima asangalale mu ulemu wake
ndi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo.
6 Matamando a Mulungu akhale pakamwa pawo,
ndi lupanga lakuthwa konsekonse mʼmanja mwawo,
7 kubwezera chilango anthu a mitundu ina,
ndi kulanga anthu a mitundu yonse,
8 kumanga mafumu awo ndi zingwe,
anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo,
9 kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawo
Uwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse.
Tamandani Yehova.
Mliri wa Mdima
21 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Tambasulira dzanja lako kumwamba kuti kukhale mdima umene udzaphimba dziko lonse la Igupto, mdima wandiweyani.” 22 Choncho Mose anakweza dzanja lake kumwamba ndipo mdima wandiweyani unaphimba dziko lonse la Igupto kwa masiku atatu. 23 Palibe amene anatha kuona mnzake kapena kuchoka pa khomo pake kwa masiku atatu. Koma kumalo kumene kumakhala Aisraeli kunali kowala.
24 Kenaka Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni nati, “Pitani kapembedzeni Yehova. Ngakhale akazi ndi ana anu apite pamodzi ndi inu. Koma musatenge ziweto zanu ndi ngʼombe zanu.”
25 Koma Mose anati, “Ndiye inu mutipatse nsembe zopsereza zoti tikapereke kwa Yehova Mulungu wathu. 26 Koma ayi, ife tipita ndi ziweto zathu. Palibe chiweto chilichonse chimene chitatsale kuno, popeza tikasankha komweko ziweto zokapembedzera Yehova. Sitingadziwe zimene tikagwiritse ntchito popembedza Yehova mpaka titakafika kumeneko.”
27 Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao ndipo sanafune kuwalola kuti apite. 28 Farao anati kwa Mose, “Choka pamaso panga! Uwonetsetse kuti usadzaonekerenso pamaso panga! Tsiku limene ndidzakuonenso udzafa.”
29 Mose anayankha kuti, “Monga momwe mwaneneramu, Ine sindidzaonekeranso pamaso panu.”
15 Ndipo iwo adzalalikira bwanji osatumidwa? Kwalembedwa kuti, “Akongoladi mapazi a iwo amene amabweretsa Uthenga Wabwino!”
16 Koma si onse amene anavomereza Uthenga Wabwino. Pakuti Yesaya akuti, “Ambuye, ndani amene wakhulupirira uthenga wathu?” 17 Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu. 18 Koma ndikufunsa kuti kodi iwo anamva? Inde, iwo anamva kuti,
“Liwu lawo linamveka ponseponse pa dziko lapansi.
Mawu awo anafika ku malekezero a dziko lonse.”
19 Ine ndifunsanso kuti, kodi Israeli sanazindikire? Poyamba Mose akuti,
“Ine ndidzawachititsa kuti achite nsanje ndi mtundu wina wopandapake.
Ine ndidzawakwiyitsa ndi mtundu wina wachabechabe.”
20 Ndipo Yesaya molimba mtima akuti,
“Anandipeza anthu amene sanali kundifunafuna.
Ndinadzionetsera kwa amene sanafunse za Ine.”
21 Koma zokhudzana ndi Aisraeli akuti,
“Tsiku lonse ndinatambasulira manja anga
kwa anthu osandimvera ndi okanika.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.