Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 8

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa gititi. Salimo la Davide.

Inu Yehova Ambuye athu,
    dzina lanu ndi la lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!

Inu mwakhazikitsa ulemerero wanu
    mʼmayiko onse akumwamba.
Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda,
    Inu mwakhazikitsa mphamvu
chifukwa cha adani anu,
    kukhazikitsa bata adani ndi anthu obwezera zoyipa.

Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba,
    ntchito ya zala zanu,
mwezi ndi nyenyezi,
    zimene mwaziyika pa malo ake,
munthu ndani kuti Inu mumamukumbukira,
    ndi mwana wa munthu kuti inu mumacheza naye?
Inu munamupanga kukhala wocheperapo kusiyana ndi zolengedwa zakumwamba
    ndipo mwamuveka ulemerero ndi ulemu.

Inu munamuyika wolamulira ntchito ya manja anu;
    munayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake;
nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe pamodzi
    ndi nyama zakuthengo,
mbalame zamlengalenga
    ndi nsomba zamʼnyanja
    zonse zimene zimayenda pansi pa nyanja.

Inu Yehova, Ambuye athu,
    dzina lanu ndi lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!

Eksodo 2:15-22

15 Farao atamva zimenezi anafuna kuti aphe Mose, koma Mose anathawa ndipo anapita kukakhala ku Midiyani. Ali kumeneko, tsiku lina anakhala pansi pafupi ndi chitsime. 16 Wansembe wa ku Midiyaniko anali ndi ana aakazi asanu ndi awiri. Iwowa anabwera kudzatunga madzi ndi kudzaza mu zomwera kuti amwetse nkhosa za abambo awo. 17 Koma kunabwera abusa ena amene anathamangitsa atsikana aja. Ndiye Mose anayimirira nawathandiza atsikana aja ndi kumwetsa nkhosa zawo.

18 Atsikana aja atabwerera kwa abambo awo Reueli, iye anawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani lero mwabwera msanga?”

19 Atsikanawo anayankha kuti, “Mwigupto wina ndiye watilanditsa kwa abusa. Ndiponso anatitungira madzi ndi kumwetsa ziweto zathu.”

20 Tsono Reueli anafunsa ana ake kuti, “Ndiye ali kuti munthuyo? Chifukwa chiyani mwamusiya? Kamuyitaneni kuti adzadye.”

21 Mose anavomera kukhala ndi Reueli, ndipo anamupatsa Zipora kuti akhale mkazi wake. 22 Zipora anabereka mwana wa mwamuna amene Mose anamutcha Geresomu, popeza anati, “Ndakhala mlendo mʼdziko la eni.”

Mateyu 26:6-13

Yesu Adzozedwa ku Betaniya

Yesu ali ku Betaniya mʼnyumba Simoni Wakhate, mayi wina anabwera kwa Iye ndi botolo la mafuta onunkhira a mtengowapatali, amene anathira pa mutu pake Iye akudya pa tebulo.

Ophunzira ataona izi anayipidwa nafunsa kuti, “Chifukwa chiyani akuwononga chotere? Mafuta amenewa akanatha kugulitsidwa pa mtengo waukulu, ndipo ndalama zake zikanaperekedwa kwa osauka.”

10 Yesu podziwa izi anawawuza kuti, “Chifukwa chiyani mukumuvutitsa mayiyu? Wandichitira Ine chinthu chabwino. 11 Osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse. 12 Pamene wathira mafuta onunkhirawa pa thupi langa, wachita izi kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda. 13 Zoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwinowu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi, zimene wachitazi zidzanenedwanso pomukumbukira.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.