Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 8

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa gititi. Salimo la Davide.

Inu Yehova Ambuye athu,
    dzina lanu ndi la lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!

Inu mwakhazikitsa ulemerero wanu
    mʼmayiko onse akumwamba.
Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda,
    Inu mwakhazikitsa mphamvu
chifukwa cha adani anu,
    kukhazikitsa bata adani ndi anthu obwezera zoyipa.

Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba,
    ntchito ya zala zanu,
mwezi ndi nyenyezi,
    zimene mwaziyika pa malo ake,
munthu ndani kuti Inu mumamukumbukira,
    ndi mwana wa munthu kuti inu mumacheza naye?
Inu munamupanga kukhala wocheperapo kusiyana ndi zolengedwa zakumwamba
    ndipo mwamuveka ulemerero ndi ulemu.

Inu munamuyika wolamulira ntchito ya manja anu;
    munayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake;
nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe pamodzi
    ndi nyama zakuthengo,
mbalame zamlengalenga
    ndi nsomba zamʼnyanja
    zonse zimene zimayenda pansi pa nyanja.

Inu Yehova, Ambuye athu,
    dzina lanu ndi lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!

Eksodo 2:11-15

Mose Athawira ku Midiyani

11 Tsiku lina, Mose atakula, anapita kumene kunali anthu a mtundu wake ndipo anawaona akugwira ntchito yowawa. Iye anaona Mwigupto akumenya Mhebri, mmodzi mwa anthu a mtundu wake. 12 Atayangʼana uku ndi uku, naona kuti panalibe wina aliyense, Mose anamupha Mwiguptoyo ndipo anamukwirira mu mchenga. 13 Mmawa mwake Mose anapita ndipo anaona anthu awiri a Chihebri akumenyana. Iye anafunsa amene anali wolakwa kuti, “Chifukwa chiyani ukumenya Mhebri mnzako?”

14 Munthu uja anati, “Kodi ndani anakuyika kuti ukhale wotilamulira ndi wotiweruza? Kodi ukufuna kundipha monga momwe unaphera Mwigupto uja?” Mose anachita mantha ndipo anati mu mtima mwake, “Chimene ndinachita chija chadziwika.”

15 Farao atamva zimenezi anafuna kuti aphe Mose, koma Mose anathawa ndipo anapita kukakhala ku Midiyani. Ali kumeneko, tsiku lina anakhala pansi pafupi ndi chitsime.

Aroma 11:33-36

Kulemekeza Mulungu

33 Aa! Nzeru za Mulungu ndi chidziwitso chake ndi zozama kwambiri!
    Ndani angazindikire maweruzidwe ake,
    ndipo njira zake angazitulukire ndani?
34 “Kodi wadziwa ndani maganizo a Ambuye?
    Kapena ndani anakhalapo mlangizi wake?”
35 “Kodi ndani anapereka mphatso kwa Mulungu,
    kuti Mulunguyo amubwezere iye?”
36 Pakuti zinthu zonse nʼzochokera kwa Iye, nʼzolengedwa ndi Iye ndipo zimabweretsa ulemerero kwa Iye.
    Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya! Ameni.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.