Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 124

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

124 Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,
    anene tsono Israeli,
akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,
    potiwukira anthuwo,
iwo atatipsera mtima,
    akanatimeza amoyo;
chigumula chikanatimiza,
    mtsinje ukanatikokolola,
madzi a mkokomo
    akanatikokolola.

Atamandike Yehova,
    amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo.
Moyo wathu wawonjoka ngati mbalame
    yokodwa mu msampha wa mlenje;
msampha wathyoka,
    ndipo ife tapulumuka.
Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova
    wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Genesis 49:29-50:14

Kumwalira kwa Yakobo

29 Kenaka Yakobo analamula ana ake nati: “Ine ndatsala pangʼono kufa. Tsono mukandiyike pamodzi ndi makolo anga mʼphanga la mʼmunda wa Efroni Mhiti. 30 Ili ndi phanga la mʼmunda wa Makipela, pafupi ndi Mamre mʼdziko la Kanaani. Abrahamu anagula phangalo pamodzi ndi munda womwe kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda. 31 Kumeneko kunayikidwa Abrahamu ndi mkazi wake Sara, Isake ndi mkazi wake Rebeka ndipo ndinayikakonso Leya. 32 Munda ndi manda amene ali mʼmenemo zinagulidwa kwa Ahiti.”

33 Yakobo atamaliza kupereka malangizo kwa ana ake, anabwezera miyendo yake pa bedi, namwalira ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake.

50 Kenaka Yosefe anadzigwetsa pa nkhope ya abambo ake, nawapsompsona kwinaku akulira. Ndipo Yosefe analamula antchito ake a chipatala kuti akonze thupi la Israeli ndi mankhwala kuti lisawole. Kotero antchitowo anakonzadi thupilo. Antchito aja zinawatengera masiku 40 kuti akonze mtembo uja popeza ntchito ngati imeneyi inafunikira masiku monga amenewa. Ndipo Aigupto anamulira Yakobo kwa masiku makumi asanu ndi awiri.

Yosefe atatha kulira maliro a abambo ake, anayankhula kwa nduna za Farao nati, “Ngati mungandikomere mtima, chonde mundiyankhulire kwa Farao kumuwuza kuti, ‘Abambo anga anandilumbiritsa ndipo anati, ‘Ndatsala pangʼono kumwalira, ukandiyike mʼmanda amene ndinakumba ndekha mʼdziko la Kanaani.’ Tsono mundilole ndikayike abambo anga, ndipo ndikabweranso.’ ”

Farao anati, “Pita ukayike abambo ako monga anakulumbiritsa kuti uchite.”

Kotero Yosefe anapita kukayika abambo ake. Nduna zonse za Farao, akuluakulu a bwalo lake ndi akuluakulu a ku Igupto, anapita naye pamodzi. Anapitanso onse a pa banja la Yosefe ndi abale ake ndi onse amene anali a pa banja la abambo ake. Ana awo okha, nkhosa ndi ngʼombe zinatsala ku Goseni Asilikali okwera pa magaleta ndi asilikali a pa akavalo anapita nayenso pamodzi. Linali gulu lalikulu.

10 Atafika pa Goreni ha-Atadi, pafupi ndi Yorodani, anachita mwambo waukulu wa maliro. Choncho Yosefe analira maliro a abambo ake masiku asanu ndi awiri. 11 Akanaani amene ankakhala ku Goreni ha-Atadi ataona mwambo wa maliro anati, “Aigupto ali ndi mwambo wa maliro a akulu.” Ndi chifukwa chake malo amenewo a pafupi ndi Yorodani amatchedwa Abeli-Mizraimu.

12 Choncho ana a Yakobo anachita monga momwe abambo awo anawalamula: 13 Ndiye kuti ana a Yakobo anamunyamula kupita naye ku Kanaani kuti akamuyike mʼphanga limene lili mʼmunda wa Makipela pafupi ndi Mamre. Abrahamu anagula mundawo kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda. 14 Atatha kuyika abambo ake, Yosefe anabwerera ku Igupto, pamodzi ndi abale ake ndi onse amene anapita nawo kukayika abambo ake.

2 Akorinto 10:12-18

12 Sitikudziyika kapena kudzifananiza tokha ndi anthu ena amene amadziyenereza okha. Pamene akudzifanizira okha podziyerekeza ndi anzawo a mʼgulu lawo lomwe, ndi opanda nzeru. 13 Komabe, ifeyo sitidzitama modutsa malire ake enieni, koma kudzitama kwathu kudzalekeza mʼmalire amene Mulungu anatiyikira, malire ake ndi mpaka kwa inu. 14 Pakuti sitikudzitama modutsa malire ngati kuti sitinafike kwa inu, popeza tinali oyamba kufika kwa inu ndi Uthenga Wabwino wa Khristu. 15 Choncho sitinyadiranso ntchito imene ena anayigwira. Chiyembekezo chathu nʼchakuti, pamene chikhulupiriro chanu chikukulirakulira, dera lathu la ntchito pakati panu lidzakulanso kwambiri, 16 kuti tikalalikire Uthenga Wabwino mu zigawo zina kupitirira kwanuko. Pakuti sitikufuna kudzitama pa ntchito yogwira ena kale mʼdera la munthu wina. 17 Koma, “Ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire mwa Ambuye.” 18 Pakuti munthu amene amavomerezedwa, si amene amadziyenereza yekha, koma munthu amene Ambuye amuyenereza.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.