Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 133

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

133 Onani, nʼkokoma ndi kokondweretsa ndithu
    pamene abale akhala pamodzi mwachiyanjano!
Zili ngati mafuta amtengowapatali othiridwa pa mutu,
    otsikira ku ndevu,
ku ndevu za Aaroni,
    oyenderera mpaka mʼkhosi mwa mkanjo wake.
Zili ngati mame a ku Heremoni
    otsikira pa Phiri la Ziyoni.
Pakuti pamenepo Yehova amaperekapo dalitso,
    ndiwo moyo wamuyaya.

Genesis 41:14-36

14 Choncho Farao anamuyitanitsa Yosefe, ndipo mofulumira anabwera naye kuchokera mʼdzenje muja. Ndipo atameta, ndi kusintha zovala, anapita kwa Farao.

15 Farao anati kwa Yosefe, “Ndinalota maloto ndipo palibe amene watha kunditanthauzira. Tsono ndawuzidwa kuti iwe ukamva loto umadziwanso kulimasulira.”

16 Yosefe anamuyankha Farao kuti, “Sindingathe koma Mulungu apereka yankho limene Farao akufuna.”

17 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, “Ndinalota nditayimirira mʼmphepete mwa mtsinje wa Nailo, 18 ndipo ngʼombe zisanu ndi ziwiri zonenepa ndi zooneka bwino zinatuluka mu mtsinje muja ndi kumadya msipu wa mu mawango. 19 Kenaka, ngʼombe zina zisanu ndi ziwiri zinatuluka. Izi zinali zosaoneka bwino ndiponso zowonda ndipo sindinaonepo ngʼombe zosaoneka bwino chonchi mʼdziko lonse la Igupto. 20 Ngʼombe zosaoneka bwino ndi zowonda zija zinadya zisanu ndi ziwiri zonenepa zimene zinatuluka poyamba zija. 21 Koma ngakhale ngʼombezi zinadya zinazo, palibe amene akanatha kuzindikira kuti zinatero popeza zinali zosaonekabe bwino monga poyamba. Ndipo ndinadzidzimuka.

22 “Nditagonanso kachiwiri, ndinalota ngala zisanu ndi ziwiri za tirigu zathanzi ndi zonenepa zitabala pa phata limodzi. 23 Kenaka panaphukanso ngala zina zisanu ndi ziwiri zofota, zowonda ndi zowauka ndi mphepo ya kummawa. 24 Ngala zowondazo zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zabwino zija. Ndinawawuza amatsenga koma palibe ndi mmodzi yemwe anatha kundimasulira.”

25 Ndipo Yosefe anati kwa Farao, “Maloto awiriwa ndi ofanana ndipo ali ndi tanthauzo limodzi. Mulungu waululira Farao chimene atachite. 26 Ngʼombe zisanu ndi ziwiri zabwinozo ndi zaka zisanu ndi ziwiri. Ndipo ngala zisanu ndi ziwiri zabwinozo ndi zaka zisanu ndi ziwiri. Kutanthauza kwa maloto nʼkumodzi. 27 Ngʼombe zisanu ndi ziwiri zowonda ndi zosaoneka bwino zimene zinatuluka pambuyozo ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zachabechabe, zowauka ndi mphepo ya kummawa zija ndi zaka zisanu ndi ziwiri za njala.

28 “Tsono ndi monga ndafotokozeramu kuti Mulungu wakuwuziranitu zimene adzachite. 29 Zaka zisanu ndi ziwiri za zokolola zochuluka zikubwera mu dziko lonse la Igupto, 30 koma zidzatsatana ndi zaka zina zisanu ndi ziwiri za njala. Chakudya chochuluka cha mu Igupto chija chidzayiwalika ndipo njalayo idzawononga dziko. 31 Zakudya zochuluka za mʼdzikomo zija sizidzakumbukirikanso chifukwa njala imene iti idzabwereyo idzakhala yoopsa. 32 Popeza kuti malotowa aperekedwa kwa inu Mfumu kawiri, ndiye kuti Mulungu watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi posachedwapa.

33 “Tsopano Farao apezeretu munthu wozindikira ndi wanzeru ndipo amuyike kukhala woyangʼanira dziko lonse la Igupto. 34 Asankhenso akuluakulu a mʼdziko lino. Iwowa azitenga ndi kuyika padera limodzi la magawo asanu aliwonse a zokolola za mʼdziko muno mu zaka zonse zisanu ndi ziwiri za chakudya chochuluka. 35 Iwo asonkhanitse zakudya zonse za mʼzaka zabwino zikubwerazi. Pansi pa ulamuliro wa Farao, akuluakuluwo asonkhanitse ndi kusunga bwino tirigu mʼmizinda yonse. 36 Chakudya chimenechi chisungidwe kuti chidzagwiritsidwe ntchito mʼzaka zisanu ndi ziwiri za njala imene ikubwerayo mu Igupto, kuti anthu a mʼdzikoli asadzafe ndi njalayo.”

Chivumbulutso 15:1-4

Angelo Asanu ndi Awiri Okhala ndi Miliri Isanu ndi Iwiri

15 Kumwamba ndinaona chizindikiro china chachikulu ndi chodabwitsa: angelo asanu ndi awiri ali ndi miliri isanu ndi iwiri yomaliza chifukwa Mulungu anakwiya kotheratu. Ndipo ndinaona chimene chinaoneka ngati nyanja yonyezimira yosakaniza ndi moto, ndipo pambali pa nyanjayo panayima amene anagonjetsa chirombo chija ndi fano lake, ndi nambala yotanthauza dzina lake. Anthuwo ananyamula azeze amene Mulungu anawapatsa. Iwo ankayimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwana Wankhosa. Nyimbo yake inkati,

“Zochita zanu ndi zazikulu ndi zodabwitsa,
    Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse
Njira zanu ndi zachilungamo ndi zoona,
    Mfumu ya mitundu yonse.
Inu Ambuye, ndani angapande kukuopani,
    ndi kulemekeza dzina lanu?
Pakuti Inu nokha ndiye woyera.
Anthu a mitundu yonse adzabwera
    kudzapembedza pamaso panu,
pakuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.