Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 28

Salimo la Davide.

28 Kwa Inu ine ndiyitana, Yehova ndinu Thanthwe langa;
    musakhale osamva kwa ine.
Pakuti mukapitirira kukhala chete,
    ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.
Imvani kupempha chifundo kwanga
    pomwe ndikuyitana kwa Inu kuti mundithandize,
pomwe ndikukweza manja anga
    kuloza ku malo anu oyeretsetsa.

Musandikokere kutali pamodzi ndi anthu oyipa,
    pamodzi ndi iwo amene amachita zoyipa,
amene amayankhula mwachikondi ndi anzawo
    koma akusunga chiwembu mʼmitima mwawo.
Muwabwezere chifukwa cha zochita zawo
    ndi ntchito zawo zoyipa;
abwezereni chifuwa cha zimene manja awo achita
    ndipo mubweretse pa iwo zimene zowayenera.
Popeza iwowo sakhudzidwa ndi ntchito za Yehova,
    ndi zimene manja ake anazichita,
Iye adzawakhadzula
    ndipo sadzawathandizanso.

Matamando apite kwa Yehova,
    popeza Iye wamva kupempha chifundo kwanga.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa;
    mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa.
Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe
    ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.

Yehova ndi mphamvu ya anthu ake,
    linga la chipulumutso kwa wodzozedwa wake.
Pulumutsani anthu anu ndipo mudalitse cholowa chanu;
    mukhale mʼbusa wawo ndipo muwakweze kwamuyaya.

Genesis 40

Yosefe Amasulira Maloto a Amʼndende Anzake

40 Patapita nthawi, woperekera zakumwa ndi wopanga buledi a ku nyumba kwa mfumu ya ku Igupto analakwira mbuye wawoyo. Farao anapsa mtima ndi akuluakulu awiriwa, ndipo anakawatsekera mʼndende, nakawayika mʼmanja mwa mkulu wa asilikali olonda ku nyumba kwa mfumu kuja, mʼndende momwe Yosefe ankasungidwamo. Mkulu wa alonda aja anawapereka mʼmanja mwa Yosefe, ndipo iye anawasamalira.

Iwo anakhala mʼndendemo kwa kanthawi. Usiku wina, aliyense wa anthu awiriwa, wopereka zakumwa pamodzi ndi wopanga buledi wa ku nyumba ya mfumu ya ku Igupto aja, amene ankasungidwa mʼndende, analota maloto. Malotowo anali ndi tanthauzo lake.

Mmawa wake, Yosefe atabwera, anaona kuti nkhope zawo zinali zakugwa. Choncho anafunsa akuluakulu a kwa Farao amene anali naye mʼndende muja kuti, “Bwanji nkhope zanu zili zachisoni lero?”

Iwo anayankha, “Tonse awiri talota maloto, koma palibe wotitanthauzira malotowo.”

Pamenepo Yosefe anawawuza kuti, “Ndi Mulungu yekha amene amapereka matanthauzo a maloto. Uzeni ine maloto anu.”

Choncho mkulu wa operekera zakumwa uja anamuwuza Yosefe maloto ake. Anati, “Mʼmaloto anga ndinaona mtengo wa mpesa, 10 unali ndi nthambi zitatu. Mpesawo utangophukira, unachita maluwa ndipo maphava ake anabereka mphesa zakupsa. 11 Chikho cha Farao chinali mʼmanja mwanga, ndipo ndinatenga mphesa, kupsinyira mu chikho cha Farao ndi kuchipereka mʼmanja mwake.”

12 Yosefe anati kwa iye, “Tanthauzo lake ndi ili: Nthambi zitatuzo ndi masiku atatu. 13 Pakangopita masiku atatu, Farao adzakutulutsa muno. Udzaperekera zakumwa kwa Farao monga momwe umachitira poyamba. 14 Koma zako zikakuyendera bwino, udzandikumbukire ndi kundikomera mtima. Chonde ukandipepesere kwa Farao kuti anditulutse muno. 15 Popezatu ine anangochita mondiba kubwera nane kuno kuchokera ku dziko la Ahebri, ndipo ngakhale kunoko, ine sindinalakwe kali konse kuti ndizipezeka mʼdzenje muno.”

16 Mkulu wa opanga buledi ataona kuti Yosefe wapereka tanthauzo labwino, anati kwa Yosefe, “Inenso ndinalota nditasenza nsengwa zitatu za buledi. 17 Mu nsengwa yapamwamba munali zakudya zamitundumitundu za Farao, koma mbalame zimadya zakudyazo.”

18 Yosefe anati, “Tanthauzo lake ndi ili: nsengwa zitatuzo ndi masiku atatu. 19 Pakangotha masiku atatu Farao adzakutulutsa muno koma adzakupachika. Ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.”

20 Tsono tsiku lachitatulo linali lokumbukira kubadwa kwa Farao, ndipo anawakonzera phwando akuluakulu ake onse. Anatulutsa mʼndende mkulu wa operekera zakumwa ndi mkulu wa ophika buledi, ndipo anawayimiritsa pamaso pa nduna zake. 21 Tsono Farao anamubwezera mkulu wa operekera zakumwa uja pa udindo wake, kotero kuti anayamba kuperekeranso zakumwa kwa Farao, 22 koma mkulu wa ophika buledi anamupachika, mofanana ndi mmene Yosefe anatanthauzira maloto.

23 Koma mkulu wa operekera zakumwa uja sanamukumbukire Yosefe ndipo anamuyiwaliratu.

Mateyu 8:23-27

Yesu Aletsa Namondwe

23 Iye atalowa mʼbwato, ophunzira ake anamutsatira. 24 Ndipo taonani mwadzidzidzi mphepo yayikulu yamkuntho inawomba pa nyanjapo, kotero kuti bwatolo linayamba kumizidwa ndi mafunde. Koma Yesu anali mtulo. 25 Ophunzira ake anapita namudzutsa nati, “Ambuye! Tipulumutseni! Tikumira!”

26 Iye anawayankha kuti, “Inu achikhulupiriro chochepa, chifukwa chiyani mukuchita mantha?” Ndipo anayimirira nadzudzula mphepoyo ndi mafunde ndipo panali bata lalikulu.

27 Ndipo ophunzirawo anadabwa nafunsa kuti, “Ndi munthu wotani uyu? Kuti ngakhale mphepo ndi mafunde zimvera Iye!”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.