Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide.
28 Kwa Inu ine ndiyitana, Yehova ndinu Thanthwe langa;
musakhale osamva kwa ine.
Pakuti mukapitirira kukhala chete,
ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.
2 Imvani kupempha chifundo kwanga
pomwe ndikuyitana kwa Inu kuti mundithandize,
pomwe ndikukweza manja anga
kuloza ku malo anu oyeretsetsa.
3 Musandikokere kutali pamodzi ndi anthu oyipa,
pamodzi ndi iwo amene amachita zoyipa,
amene amayankhula mwachikondi ndi anzawo
koma akusunga chiwembu mʼmitima mwawo.
4 Muwabwezere chifukwa cha zochita zawo
ndi ntchito zawo zoyipa;
abwezereni chifuwa cha zimene manja awo achita
ndipo mubweretse pa iwo zimene zowayenera.
5 Popeza iwowo sakhudzidwa ndi ntchito za Yehova,
ndi zimene manja ake anazichita,
Iye adzawakhadzula
ndipo sadzawathandizanso.
6 Matamando apite kwa Yehova,
popeza Iye wamva kupempha chifundo kwanga.
7 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa;
mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa.
Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe
ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.
8 Yehova ndi mphamvu ya anthu ake,
linga la chipulumutso kwa wodzozedwa wake.
9 Pulumutsani anthu anu ndipo mudalitse cholowa chanu;
mukhale mʼbusa wawo ndipo muwakweze kwamuyaya.
Yosefe ndi Mkazi wa Potifara
39 Tsopano Yosefe anatengedwa kupita ku Igupto. Potifara Mwigupto amene anali mmodzi wa akuluakulu a Farao ndiponso mkulu wa asilikali olonda ku nyumba kwa Farao, anagula Yosefe kwa Aismaeli amene anapita naye kumeneko.
2 Koma Yehova anali ndi Yosefe ndipo zake zonse zimayenda bwino. Iye ankakhala mʼnyumba ya mbuye wake wa ku Igupto. 3 Mbuye wake anaona kuti Yehova anali naye Yosefe ndi kuti pa chilichonse chimene anachita Yehova ankaonetsetsa kuti achite bwino. 4 Potifara anakondwera ndi Yosefe chifukwa cha matumikiridwe ake. Choncho anamusandutsa woyangʼanira nyumba yake ndi zonse za mʼnyumba yake. 5 Kuchokera pa nthawi imene anamuyika kukhala woyangʼanira wa nyumbayo ndi zonse za mʼnyumbamo, Yehova anadalitsa nyumba ya Mwiguptoyo chifukwa cha Yosefe. Madalitso a Yehova anali pa chilichonse chimene Potifara anali nacho, za mʼnyumba komanso za ku munda. 6 Choncho anasiyira mʼmanja mwa Yosefe chilichonse chomwe anali nacho, kotero kuti samadandaula ndi chilichonse kupatula chakudya chimene ankadya.
Tsopano Yosefe anali wa thupi labwino ndi wokongola. 7 Patapita kanthawi, mkazi wa mbuye wake anayamba kusirira Yosefe nati, “Bwanji ugone nane!”
8 Koma iye anakana namuwuza kuti, “Inu mukuona kuti mbuye wanga sadandaula ndi kena kalikonse mʼnyumba muno, ndipo chawo chilichonse anachiyika mʼmanja mwanga. 9 Motero kuti palibe wina wamkulu kuposa ine mʼnyumba muno. Ndipo palibe chilichonse chimene mbuye wanga sanachipereke kwa ine kupatula inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake. Tsono ndingachite bwanji choyipa choterechi ndi kuchimwira Mulungu?” 10 Ndipo ngakhale kuti iye anayankhula mawu omwewa ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, Yosefe sanalole kugona naye ngakhale kukhala naye pafupi.
11 Tsiku lina Yosefe analowa mʼnyumbamo kukagwira ntchito zake, ndipo munalibe wina aliyense wantchito mʼnyumbamo. 12 Mkazi uja anamugwira mkanjo Yosefe nati, “Tiye ugone nane!” Koma Yosefe anasiya mkanjo wake mʼmanja mwa mkaziyo nathawira kunja kwa nyumba.
13 Pamene mkazi uja anaona kuti Yosefe wamusiyira mkanjo wake mʼmanja mwake nathawira kunja kwa nyumba, 14 iye anayitana antchito ake a mʼnyumba nati, “Taonani mwamuna wanga anabwera ndi Mhebri uyu mʼnyumba muno kuti adzagone nane. Iyeyu analowa ku chipinda kwanga kuti adzagone nane ndipo ine ndinakuwa kwambiri. 15 Atandimva ndikukuwa, anandisiyira mkanjo wakewu nʼkuthawira kunja.”
16 Tsono mkazi wa Potifara uja anasunga mkanjowo mpaka mbuye wake wa Yosefe atabwera ku nyumba. 17 Tsono anamuwuza nkhaniyi nati: “Wantchito Wachihebri amene munatibweretsera uja anabwera kuti adzagone nane. 18 Koma pamene ndinakuwa, iye anandisiyira mkanjo wake nathawira kunja.”
19 Mbuye wake wa Yosefe atamva nkhani imene mkazi wake anamuwuza kuti, “Ndi zimene anandichitira wantchito wanu,” anapsa mtima kwambiri. 20 Tsono iye anatenga Yosefe namuyika mʼndende mmene ankasungiramo amʼndende a mfumu.
Ndipo Yosefe anakhala mʼndendemo 21 koma Yehova anali naye, ndipo anamuonetsa kukoma mtima kwake, kotero kuti woyangʼanira ndende anakondwera ndi Yosefe. 22 Choncho woyangʼanira ndende uja anamuyika Yosefe kukhala woyangʼanira onse amene anayikidwa mʼndende. Ndiponso anamupatsa udindo woyangʼanira zonse zochitika mʼndendemo. 23 Woyangʼanira ndende uja sankayangʼaniranso china chilichonse chimene chinali mu ulamuliro wa Yosefe, chifukwa Yehova anali ndi Yosefe. Ndipo Yehova anaonetsetsa kuti chilichonse chimene Yosefe ankachita chimuyendere bwino.
14 Nanga tsono tidzanena chiyani? Kodi Mulungu ndi osalungama? Ayi, ndi pangʼono pomwe! 15 Pakuti Mulungu anawuza Mose kuti,
“Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo,
ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.”
16 Nʼchifukwa chake, izi sizitengera zokhumba za munthu kapena kuyesetsa koma chifundo cha Mulungu. 17 Malemba akuti Mulungu anamuwuza Farao kuti, “Ine ndakuyika kukhala mfumu ndi cholinga choti ndionetse mphamvu zanga, kuti mwa iwe dzina langa litchuke pa dziko lonse lapansi.” 18 Choncho Mulungu amachitira chifundo munthu amene akufuna kumuchitira chifundo ndipo amawumitsa mtima munthu amene Iye akufuna kumuwumitsa mtima.
19 Tsono mmodzi wa inu nʼkundifunsa kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani Mulungu amatipeza olakwa? Nanga ndani amene amakana chifuniro chake?” 20 Koma ndiwe yani, munthu wamba, woti nʼkutsutsana ndi Mulungu? “Kodi chimene chinawumbidwa nʼkufunsa amene anachiwumba kuti, ‘Kodi unandiwumbiranji motere?’ ” 21 Kodi wowumba alibe ufulu wowumba kuchokera ku dothi lomwelo mbiya yamtengowapatali ndi ina yamtengo wotsika?
22 Koma Mulungu, anafuna kuonetsa mkwiyo wake ndi kuti mphamvu yake idziwike. Iye anapirira modekha mtima kwambiri zochita za anthu omwe anawakwiyirawo amene anayeneradi chiwonongeko. 23 Iye anachita izi kufuna kuonetsa kulemera kwa ulemerero wake ndi kuti udziwike kwa amene analandira chifundo chake. Iye anawakonzeratu kuti alandire ulemerero wake 24 ngakhale ifenso amene anatiyitana osati kuchokera kwa Ayuda okha komanso kwa a mitundu ina. 25 Monga momwe Mulungu akunenera mʼbuku la Hoseya kuti,
“Amene sanali anthu anga ndidzawatcha ‘anthu anga;’
ndipo Ine ndidzatcha ‘wokondedwa wanga’ amene sali wokondedwa wanga,”
26 ndipo,
“Pamalo omwewo pamene ananena kuti,
‘Sindinu anthu anga,’
pomweponso adzawatchula kuti, ‘Ana a Mulungu wamoyo.’ ”
27 Yesaya anafuwula za Aisraeli kuti,
“Ngakhale chiwerengero cha Aisraeli chingakhale ngati mchenga wa ku nyanja,
otsala okha ndiye adzapulumuke.
28 Pakuti Ambuye adzagamula milandu
ya anthu pa dziko lapansi mofulumira ndi kumaliziratu.”
29 Monga momwe Yesaya ananena malo ena kuti,
“Ngati Yehova Wamphamvuzonse
akanapanda kutisiyira zidzukulu,
ife tikanawonongeka
ngati anthu a ku Sodomu, tikanakhala ngati anthu a ku Gomora.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.