Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 105:1-11

105 Yamikani Yehova, itanani dzina lake;
    lalikirani pakati pa anthu a mitundu ina zimene Iye wachita.
Imbirani Iye, imbani matamando kwa Iyeyo;
    fotokozani za machitidwe ake onse odabwitsa.
Munyadire dzina lake loyera;
    mitima ya iwo amene amafunafuna Yehova ikondwere.
Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;
    funafunani nkhope yake nthawi yonse.

Kumbukirani zodabwitsa zimene Iye anazichita,
    zozizwitsa zake ndi maweruzo amene anapereka,
inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake,
    inu ana a Yakobo, osankhika ake.
Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;
    maweruzo ake ali pa dziko lonse lapansi.

Iyeyo amakumbukira pangano lake kwamuyaya,
    mawu amene analamula kwa mibado yonse,
pangano limene Iye anapanga ndi Abrahamu,
    lumbiro limene analumbira kwa Isake.
10 Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga zophunzitsa,
    kwa Israeli monga pangano lamuyaya:
11 “Ndidzapereka kwa iwe dziko la Kanaani
    ngati gawo la cholowa chako.”

Masalimo 105:45

45 kuti iwo asunge malangizo ake
    ndi kutsatira malamulo ake.

Tamandani Yehova.

Genesis 29:9-14

Ali chiyankhulire nawo, Rakele anafika ndi nkhosa za abambo ake popeza ndiye amene ankaweta nkhosazo. 10 Yakobo ataona Rakele mwana wa Labani, mlongo wa amayi ake, ali ndi nkhosa za Labani, anapita nawugudubuza mwala uja nazimwetsa madzi nkhosa za amalume akezo. 11 Kenaka Yakobo anapsompsona Rakele nayamba kulira mokweza. 12 Kenaka Yakobo anawuza Rakele kuti iye ndi mwana wa Rebeka, mlongo wa abambo a Rakele uja. Choncho Rakele anathamanga nakawuza abambo ake.

13 Labani atamva za Yakobo, mwana wa mlongo wake, anafulumira kukakumana naye. Anamukupatira napsompsona, napita naye ku nyumba kwake. Yakobo anafotokozera Labani zonse zinachitika. 14 Ndipo, Labani anati kwa iye, “Iwe ndiwe ndithu fupa ndi mnofu wanga.”

Yakobo Akwatira Leya ndi Rakele

Yakobo anakhala ndi Labani mwezi umodzi.

Machitidwe a Atumwi 7:44-53

44 “Makolo athu anali ndi tenti ya msonkhano pakati pawo mʼchipululu. Anayipanga monga momwe Mulungu anawuzira Mose, molingana ndi chithunzi chimene Mose anachiona. 45 Makolo athu, atayilandira Tentiyo, anabwera nayo motsogozedwa ndi Yoswa pamene analanda dziko la mitundu imene Mulungu anayipirikitsa pamaso pawo. Tentiyo inakhala mʼdzikomo mpaka nthawi ya Davide, 46 amene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu ndipo anapempha kuti amʼmangire nyumba Mulungu wa Yakobo. 47 Koma anali Solomoni amene anamanga nyumbayo.

48 “Komatu, Wammwambamwambayo sakhala mʼnyumba zomangidwa ndi anthu. Monga mneneri akunena kuti,

49 “ ‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu,
    ndipo dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga.
Kodi mudzandimangira nyumba yotani?
            Akutero Ambuye.
    Kapena malo opumuliramo Ine ali kuti?
50 Kodi si dzanja langa linapanga zonsezi?’

51 “Anthu wokanika inu, osachita mdulidwe wa mu mtima ndi a makutu ogontha! Inu ofanana ndi makolo anu. Nthawi zonse mumakana kumvera Mzimu Woyera: 52 Kodi analipo mneneri amene makolo anu sanamuzunze? Iwo anapha ngakhale amene ananeneratu za kubwera kwa Wolungamayo. Ndipo tsopano inu munamupereka ndi kumupha Iye. 53 Inu amene munalandira Malamulo amene anaperekedwa ndi angelo ndipo simunawamvere.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.