Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 139:13-18

13 Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga;
    munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.
14 Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa;
    ntchito zanu ndi zodabwitsa,
    zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.
15 Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu
    pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi,
pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga.
16 Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe.
    Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu
    asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.

17 Zolingalira zanu pa ine ndi zamtengowapatali, Inu Mulungu,
    ndi zosawerengeka ndithu!
18 Ndikanaziwerenga,
    zikanakhala zochuluka kuposa mchenga;
    pamene ndadzuka, ndili nanube.

Genesis 33:1-17

Yakobo Akumana ndi Esau

33 Yakobo atakweza maso ake anaona Esau akubwera ndi anthu ake 400. Choncho ana ake anawagawira Leya, Rakele ndi antchito awiri aja. Anayika antchito ndi ana awo patsogolo, kenaka nʼkubwera Leya ndi ana ake, ndipo pambuyo pawo Rakele ndi Yosefe. Iye mwini anakhala patsogolo nawerama mpaka kukhudza pansi kasanu ndi kawiri pamene amayandikira mʼbale wake.

Koma Esau anathamanga kukakumana ndi Yakobo ndipo anamukupatira namupsompsona. Onse awiri ankangolira. Kenaka Esau ataona amayi ndi ana awo anamufunsa Yakobo kuti, “Kodi anthu amene uli nawowa ndi a ndani?”

Yakobo anayankha kuti, “Awa ndi ana amene Mulungu, mwa kukoma mtima kwake, wapereka kwa mtumiki wanune.”

Tsono antchito aja anayandikira naweramitsa mitu pansi. Kenaka, Leya ndi ana ake anabwera. Nawonso anaweramitsa mitu pansi. Potsiriza pa onse anabwera Yosefe ndi Rakele naweramitsanso mitu yawo pansi.

Esau anafunsa kuti, “Kodi gulu la ziweto ndakumana nalo lija ndi layani?”

Yakobo anayankha nati, “Mbuye wanga, gulu lija ndi lanu kuti mundikomere mtima.”

Koma Esau anati, “Mʼbale wanga, ine ndili nazo kale zambiri. Zinthu zakozi sunga.”

10 Yakobo anati, “Chonde musatero. Ngati mwandikomera mtima, landirani mphatso yangayi kuchokera kwa ine. Pakuti ndi mmene mwandirandira bwinomu, ine ndikamaona nkhope yanu ndikuchita ngati ndikuona nkhope ya Mulungu. 11 Chonde, landirani mphatso imene ndakutengeraniyi, popeza Mulungu wandikomera mtima kwambiri moti ndili ndi zonse zimene ndizifuna.” Ndipo popeza kuti Yakobo anamuwumiriza, Esau analandira.

12 Ndipo Esau anati, “Tiyeni tizipita; nditsagana nanu.”

13 Koma Yakobo anati kwa iye, “Mbuye wanga, inu mudziwa kuti anawa ndi a nthete ndiponso ndiyenera kusamalira nkhosa ndi ngʼombe zimene zikuyamwitsa ana awo. Ngati ndizimenya kuti zifulumire, tsiku limodzi lokha nyamazo zidzafa. 14 Choncho, mbuye wanga lolani kuti mutsogole. Ine ndiziyenda pangʼonopangʼono pambuyo pa ziwetozi ndi anawa mpaka ndikafika ku Seiri.”

15 Esau anati, “Ndiye bwanji ndikusiyireko ena mwa anthu anga.”

Koma Yakobo anati, “Koma muchitiranji zimenezi? Chachikulu nʼkuti mwandilandira bwino, mbuye wanga.”

16 Choncho tsiku limenelo Esau anayamba ulendo wobwerera ku Seiri. 17 Komabe Yakobo anapita ku Sukoti. Kumeneko anamanga nyumba yake ndi makola a ziweto zake. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa Sukoti.

Agalatiya 4:21-5:1

Hagara ndi Sara

21 Tandiwuzani, inu, abale amene mukufuna kukhala pansi pa lamulo, kodi simukudziwa chimene lamulo limanena? 22 Pakuti zinalembedwa kuti Abrahamu anali ndi ana aamuna awiri, wina mayi wake anali kapolo ndipo wina mayi wake anali mfulu. 23 Mwana wake wobadwa mwa kapolo anabadwa mwathupi; koma mwana wake wobadwa mwa mfulu anabadwa monga mwa lonjezo.

24 Zinthu izi zinali ngati fanizo, pakuti amayi awiriwa akuyimira mapangano awiri. Pangano limodzi ndi lochokera mʼPhiri la Sinai, ndiye Hagara, ndipo amabereka ana amene ndi akapolo. 25 Tsono Hagara, akuyimira Phiri la Sinai ku Arabiya amene afanizidwa ndi mzinda wa Yerusalemu wa lero, chifukwa ali mu ukapolo pamodzi ndi ana ake. 26 Koma Yerusalemu wakumwamba ndiye mfulu, ndipo ndiye mayi wathu. 27 Pakuti kwalembedwa kuti,

“Sangalala, iwe mayi wosabala,
    amene sunabalepo mwana;
imba nthungululu ndi kufuwula mwachimwemwe,
    iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka;
chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambiri
    kuposa mkazi wokwatiwa.”

28 Tsono inu abale, ndinu ana alonjezo ngati Isake. 29 Nthawi imeneyo mwana wobadwa mwathupi anazunza mwana wobadwa mwamphamvu za Mzimu. Zili chimodzimodzinso lero. 30 Kodi Malemba akuti chiyani? “Muchotse kapoloyo pamodzi ndi mwana wake, chifukwa mwana wa kapolo sadzagawana chuma ndi mwana wamfulu.” 31 Chifukwa chake, abale, ife sindife ana akapolo, koma ana a mfulu.

Ufulu mwa Khristu

Khristu anatimasula kuti tikhale mfulu. Tsono chirimikani, ndipo musakodwenso mʼgoli la ukapolo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.