Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 139:13-18

13 Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga;
    munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.
14 Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa;
    ntchito zanu ndi zodabwitsa,
    zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.
15 Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu
    pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi,
pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga.
16 Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe.
    Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu
    asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.

17 Zolingalira zanu pa ine ndi zamtengowapatali, Inu Mulungu,
    ndi zosawerengeka ndithu!
18 Ndikanaziwerenga,
    zikanakhala zochuluka kuposa mchenga;
    pamene ndadzuka, ndili nanube.

Genesis 32:3-21

Yakobo anatumiza amithenga ake kwa mʼbale wake Esau ku dera la Seiri, dziko la Edomu. Anawalangiza kuti, “Zimene mukanene ndi izi kwa mbuye wanga Esau: ‘Mtumiki wanu Yakobo akuti, Ine ndakhala ndi kukhala ndi Labani mpaka tsopano. Ndili ndi ngʼombe, abulu, nkhosa ndi mbuzi, antchito aamuna ndi aakazi. Tsopano ndikutumiza mawu amenewa kwa mbuye wanga, kuti mundikomere mtima.’ ”

Pamene amithenga aja anabwerera kwa Yakobo, anati, “Tinapita kwa mʼbale wanu Esau, ndipo tsopano iye akubwera kudzakumana nanu. Ali ndi anthu 400.”

Yakobo anali ndi mantha ndi nkhawa yayikulu kwambiri. Tsono anagawa anthu onse amene anali naye, ndiponso nkhosa, mbuzi, ngʼombe ndi ngamira mʼmagulu awiri. Mʼmaganizo ake iye ankanena kuti, “Ngati Esau atabwera ndi kuthira nkhondo gulu limodzi, gulu lina lotsalalo likhoza kupulumuka.”

Pamenepo Yakobo anapemphera, “Haa, Mulungu wa kholo langa Abrahamu, Mulungu wa abambo anga Isake, Aa Yehova amene munati kwa ine, ‘Bwerera ku dziko la kwanu ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira zabwino.’ 10 Ine siwoyenera kulandira kukoma mtima kwanu ndi kukhulupirika kwanu kumene mwaonetsa wantchito wanu. Ndinali ndi ndodo yokha pamene ndinawoloka Yorodani uyu koma tsopano ndili ndi magulu awiri. 11 Ndipulumutseni mʼdzanja la mʼbale wanga Esau, popeza ndikuopa kuti mwina akubwera kudzandithira nkhondo pamodzi ndi akazi ndi ana omwe. 12 Paja Inu munandilonjeza kuti simudzalephera kundichitira zabwino ndi kuti zidzukulu zanga zidzakhala zosawerengeka ngati mchenga wa ku nyanja.”

13 Iye anagona pomwepo usiku umenewo. Pambuyo pake anasankhula pa chuma chimene anali nacho zinthu izi ngati mphatso za Esau, mʼbale wake: 14 Anasankhula mbuzi zazikazi 200 ndi atonde makumi awiri, nkhosa zazikazi 200 ndi nkhosa zazimuna makumi awiri, 15 ngamira za mkaka 30 ndi ana awo, ngʼombe zazikazi 40 ndi zazimuna khumi, ndipo abulu aakazi makumi awiri ndi abulu aamuna khumi. 16 Iye anazipereka kwa antchito ake kuti azikuse, gulu lililonse pa lokha, ndipo anati kwa antchito akewo, “Tsogolani ndipo muonetsetse kuti pali mpata pakati pa gulu ndi gulu linzake.”

17 Anawuza mnyamata wa gulu loyamba kuti, “Ngati ukumana naye mʼbale wanga Esau nakufunsa kuti, ‘Ndinu antchito a yani, ndipo mukupita kuti? Nanga ziweto zonse zili patsogolo pakozi ndi za yani?’ 18 Pamenepo ukayankhe kuti, ‘Zimenezi ndi za wantchito wanu, Yakobo, ndipo wazipereka kwa inu, Esau, mbuye wake ngati mphatso. Mtumiki wanuyu akubwera mʼmbuyo mwathumu.’ ”

19 Anawuza mawu omwewo kwa wachiwiri, wachitatu ndi ena onse amene ankayenda motsogoza ziwetozo kuti, “Inunso munene zomwezo kwa Esau mukakumana naye. 20 Muzikanena kuti, ‘Wantchito wanu Yakobo akubwera mʼmbuyo mwathumu.’ ” Popeza anaganiza kuti, “Ndidzamutsitsa mtima ndi mphatso ndazitsogozazi. Apo tsono ndikadzakumana naye, mwina adzandilandira bwino.” 21 Choncho mphatso za Yakobo zinatsogola, koma iye mwini anagona pa msasa pomwepo usiku umenewo.

Chivumbulutso 14:12-20

12 Pamenepa ndi pofunika kupirira kwa anthu oyera mtima amene amasunga malamulo a Mulungu ndi kukhalabe okhulupirika kwa Yesu.

13 Kenaka ndinamva mawu kuchokera kumwamba akuti, “Lemba kuti, Odala anthu amene akufa ali mwa Ambuye kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo.”

“Inde,” akutero Mzimu, “akapumule ntchito zawo zotopetsa pakuti ntchito zawo zidzawatsata.”

Zokolola za Dziko la Pansi

14 Ndinayangʼana patsogolo panga ndinaona mtambo woyera patakhalapo wina ngati Mwana wa Munthu, kumutu atavala chipewa chaufumu chagolide ndipo mʼdzanja mwake munali chikwakwa chakunthwa. 15 Tsono mngelo wina anatuluka mʼNyumba ya Mulungu nafuwula mwamphamvu kwa uja wokhala pa mtamboyu. Mngeloyo anati, “Tenga chikwakwa chako ndipo kolola, pakuti nthawi yokolola ya dziko la pansi yakwana” 16 Choncho wokhala pa mtambo uja anayamba kukolola dzinthu pa dziko lapansi ndi chikwakwa chakecho.

17 Mngelo wina anatuluka mʼNyumba ya Mulungu kumwamba ndipo nayenso anali ndi chikwakwa chakunthwa. 18 Kenaka mngelo winanso amene amalamulira moto, anatuluka kuchokera ku guwa lansembe nayitana mwamphamvu mngelo uja amene anali ndi chikwakwa chakunthwa chija, nati, “Tenga chikwakwa chako chakunthwacho yamba kudula mphesa za mʼmunda wamphesa wa pa dziko lapansi, pakuti mphesa zapsa kale.” 19 Pamenepo mngeloyo anayambadi kugwiritsa ntchito chikwakwa chake nadula mphesa za dziko lapansi, naziponya mʼchopondera mphesa chachikulu cha ukali woopsa wa Mulungu. 20 Mphesazo zinapondedwa mʼchopondera mphesa kunja kwa mzinda. Mʼchopondera mphesamo munatuluka magazi amene anayenderera ngati mtsinje, kuzama kwake mita ndi theka ndipo kutalika kwake makilomita 300.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.