Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 119:105-112

Nuni

105 Mawu anu ndi nyale ya kumapazi kwanga
    ndi kuwunika kwa pa njira yanga.
106 Ndalumbira ndipo ndatsimikiza,
    kuti ndidzatsatira malamulo anu olungama.
107 Ndazunzika kwambiri;
    Inu Yehova, sungani moyo wanga molingana ndi mawu anu.
108 Inu Yehova, landirani matamando aufulu ochokera pakamwa panga,
    ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.
109 Ngakhale moyo wanga umakhala mʼzoopsa nthawi ndi nthawi,
    sindidzayiwala malamulo anu.
110 Anthu oyipa anditchera msampha,
    koma sindinasochere kuchoka pa malangizo anu.
111 Umboni wanu ndiye cholowa changa kwamuyaya;
    Iwo ndiye chimwemwe cha mtima wanga.
112 Mtima wanga wakhazikika pa kusunga zophunzitsa zanu
    mpaka kumapeto kwenikweni.

Yesaya 2:1-4

Phiri la Yehova

Nazi zinthu zokhudza Yuda ndi Yerusalemu, zimene Yesaya mwana wa Amozi anaziona mʼmasomphenya:

Mʼmasiku otsiriza,

phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa
    kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse,
lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse,
    ndipo mayiko onse adzathamangira kumeneko.

Anthu ambiri adzabwera ndikunena kuti,

“Tiyeni tikwere ku phiri la Yehova,
    ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo.
Iye adzatiphunzitsa njira zake,
    ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.”
Malangizo adzachokera ku Ziyoni,
    mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu.
Iye adzaweruza pakati pa mayiko,
    ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu ambiri.
Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu
    ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera.
Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina,
    kapena kuphunziranso za nkhondo.

Yohane 12:44-50

44 Kenaka Yesu anafuwula nati, “Munthu aliyense amene akhulupirira Ine, sakhulupirira Ine ndekha, komanso Iye amene anandituma Ine. 45 Iye amene waona Ine, waonanso Iye amene anandituma Ine. 46 Ine ndabwera mʼdziko lapansi monga kuwunika, kotero palibe amene amakhulupirira Ine nʼkumakhalabe mu mdima.

47 “Ndipo munthu amene amva mawu anga koma osawasunga, Ine sindimuweruza. Pakuti Ine sindinabwere kudzaweruza dziko lapansi, koma kudzapulumutsa. 48 Iye amene akana Ine ndipo salandira mawu anga ali ndi womuweruza. Tsiku lomaliza mawu amene ndiyankhulawa adzamutsutsa. 49 Pakuti Ine sindiyankhula mwa Ine ndekha, koma Atate amene anandituma amandilamulira choti ndinene ndi momwe ndinenere. 50 Ine ndikudziwa kuti lamulo lake ndi moyo wosatha. Choncho chilichonse chimene Ine ndinena ndi chimene Atate andiwuza.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.