Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 119:105-112

Nuni

105 Mawu anu ndi nyale ya kumapazi kwanga
    ndi kuwunika kwa pa njira yanga.
106 Ndalumbira ndipo ndatsimikiza,
    kuti ndidzatsatira malamulo anu olungama.
107 Ndazunzika kwambiri;
    Inu Yehova, sungani moyo wanga molingana ndi mawu anu.
108 Inu Yehova, landirani matamando aufulu ochokera pakamwa panga,
    ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.
109 Ngakhale moyo wanga umakhala mʼzoopsa nthawi ndi nthawi,
    sindidzayiwala malamulo anu.
110 Anthu oyipa anditchera msampha,
    koma sindinasochere kuchoka pa malangizo anu.
111 Umboni wanu ndiye cholowa changa kwamuyaya;
    Iwo ndiye chimwemwe cha mtima wanga.
112 Mtima wanga wakhazikika pa kusunga zophunzitsa zanu
    mpaka kumapeto kwenikweni.

Deuteronomo 32:1-10

32 Mverani, inu mayiko a mmwamba ndipo ine ndidzayankhula;
    imva, iwe dziko lapansi, mawu a pakamwa panga.
Chiphunzitso changa chigwe ngati mvula
    ndipo mawu anga atsike ngati mame,
ngati mvumbi pa udzu watsopano,
    ngati mvula yochuluka pa zomera zanthete.

Ndidzalalikira dzina la Yehova.
    Aa, tamandani ukulu wa Mulungu wathu!
Iye ndi Thanthwe, ntchito zake ndi zangwiro,
    njira zake zonse ndi zolungama.
Mulungu wokhulupirika amene salakwitsa,
    Iye ndiye wolungama ndi wosalakwa.

Koma iwo achita mosakhulupirika pamaso pake,
    iwo si ana akenso,
    koma iwo ndi mʼbado wachinyengo ndi wokhotakhota.
Kodi mukumubwezera Yehova chotere,
    inu anthu opusa ndi opanda nzeru?
Kodi Iye si Atate anu, Mlengi wanu,
    amene anakupangani ndi kukuwumbani?

Kumbukirani masiku amakedzana;
    ganizirani za mibado yakalekale.
Funsa abambo ako ndipo adzakuwuza,
    akuluakulu ako, ndipo adzakufotokozera.
Pamene Wammwambamwamba anapereka mayiko kwa anthu a mitundu ina kukhala cholowa chawo,
    pamene analekanitsa anthu onse,
anayikira malire anthu onse
    molingana ndi chiwerengero cha ana a Israeli.
Pakuti gawo la Yehova ndi anthu ake,
    Yakobo ndiye cholowa chake.

10 Anamupeza mʼchipululu,
    ku malo owuma ndi kopanda kanthu.
Anamuteteza ndi kumusamalira;
    anamutchinjiriza ngati mwanadiso wake,

Aroma 15:14-21

Paulo Mtumwi wa Anthu a Mitundu Ina

14 Abale anga, ine mwini ndikutsimikiza kuti inuyo ndinu abwino, odzaza ndi chidziwitso ndi okhoza kulangizana wina ndi mnzake. 15 Ine ndakulemberani inu molimba mtima pa fundo zina, kukhala ngati kukukumbutsaninso za zimenezo, chifukwa cha chisomo chimene Mulungu anandipatsa ine 16 kukhala mtumiki wa Khristu Yesu wa a mitundu ina ndi udindo wa wansembe, kulalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti a mitundu ina akhale nsembe yolandiridwa kwa Mulungu, yopatsidwa ndi Mzimu Woyera.

17 Choncho, ine ndikunyadira mwa Khristu Yesu potumikira Mulungu wanga. 18 Ine sindidzayesera kuyankhula za kanthu kalikonse koma zimene Khristu wazichita kudzera mwa ine zotsogolera a mitundu ina kuti amvere Mulungu mwa zimene ndinanena ndi kuzichita 19 mwamphamvu ya zizindikiro ndi zodabwitsa kudzera mwamphamvu ya Mzimu Woyera. Choncho kuchokera ku Yerusalemu ndi kuzungulira ku Iluriko, ine ndalalikira kwathunthu Uthenga Wabwino wa Khristu. 20 Chakhala chilakolako changa nthawi zonse kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kumene Khristu sadziwika, kuti ine ndisamange pa maziko a wina wake. 21 Koma monga kwalembedwa kuti,

“Iwo amene sanawuzidwe za Iye adzaona,
    ndi iwo amene sanamve adzazindikira.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.