Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Nyimbo ya Solomoni 2:8-13

Tamverani bwenzi langa!
    Taonani! Uyu akubwera apayu,
akulumphalumpha pa mapiri,
    akujowajowa pa zitunda.
Bwenzi langa ali ngati gwape kapena mwana wa mbawala.
    Taonani! Uyo wayima kuseri kwa khoma lathulo,
akusuzumira mʼmazenera,
    akuyangʼana pa mpata wa zenera.
10 Bwenzi langa anayankha ndipo anati kwa ine,
    “Dzuka bwenzi langa,
    wokongola wanga, ndipo tiye tizipita.
11 Ona, nyengo yozizira yatha;
    mvula yatha ndipo yapitiratu.
12 Maluwa ayamba kuoneka pa dziko lapansi;
    nthawi yoyimba yafika,
kulira kwa njiwa kukumveka
    mʼdziko lathu.
13 Mtengo wankhuyu ukubereka zipatso zake zoyambirira;
    mitengo ya mpesa ya maluwa ikutulutsa fungo lake.
Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga
    tiye tizipita.”

Genesis 29:31-35

Ana a Yakobo

31 Pamene Mulungu anaona kuti Yakobo sankamukonda Leya kwambiri, Iye analola kuti Leya uja akhale ndi ana, ndi kuti Rakele akhale wosabala. 32 Leya anakhala ndi pathupi ndipo anabereka mwana wamwamuna. Anamutcha Rubeni pakuti anati, “Yehova waona kusauka kwanga. Zoonadi, mwamuna wanga adzandikonda tsopano.”

33 Anakhalanso ndi pathupi ndipo pamene anabereka mwana wamwamuna anati, “Yehova anamva kuti mwamuna wanga sakundikonda, choncho wandipatsanso mwana winayu.” Ndipo anamutcha dzina lake Simeoni.

34 Anatenganso pathupi kachitatu, ndipo pamene anabereka mwana wamwamuna anati, “Pano pokha tidzaphatikana kwambiri ndi mwamuna wanga, chifukwa ndamubalira ana aamuna atatu.” Kotero anamutcha dzina lake Levi.

35 Anatenganso pathupi pena, ndipo pamene anabereka mwana wamwamuna, iye anati, “Nthawi ino ndidzalemekeza Yehova.” Choncho anamutcha Yuda. Kenaka analeka kubereka.

Yohane 13:1-17

Yesu Asambitsa Mapazi a Ophunzira Ake

13 Inali pafupifupi nthawi ya phwando la Paska. Yesu anadziwa kuti nthawi yafika yoti achoke mʼdziko lapansi ndi kupita kwa Atate. Atawakonda ake amene anali mʼdziko lapansi, Iye anawaonetsa chikondi chake chonse.

Atayamba kudya mgonero, mdierekezi anali atalowa kale mu mtima wa Yudasi Isikarioti mwana wa Simoni, kuti amupereke Yesu. Yesu podziwa kuti Atate anamupatsa Iye zonse mʼmanja mwake, ndi kuti Iye anachokera kwa Mulungu ndipo amabwerera kwa Mulunguyo; anayimirira kuchoka pa chakudya navula zovala zake natenga nsalu yopukutira nadzimanga mʼchiwuno mwake. Atachita izi, anathira madzi mʼbeseni ndi kuyamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira chimene anachimanga mʼchiwuno mwake.

Atafika pa Petro, Petroyo anati kwa Iye, “Ambuye, kodi mudzandisambitsa mapazi anga?”

Yesu anayankha kuti, “Iwe sukuzindikira tsopano chimene ndikuchita, koma udzazindikira mʼtsogolo.”

Petro anati, “Ayi, Inu simudzandisambitsa konse mapazi anga.”

Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine sindisambitsa mapazi ako, ulibe gawo mwa Ine.”

Simoni Petro anayankha kuti, “Ambuye, osati mapazi okha komanso manja anga ndi mutu wanga womwe!”

10 Yesu anayankha kuti, “Munthu amene wasamba amangofunika kusamba mapazi ake okha chifukwa thupi lake lonse ndi loyera. Ndipo inu ndinu oyera, ngakhale kuti si aliyense mwa inu.” 11 Pakuti Iye anadziwa amene adzamupereka, ndipo nʼchifukwa chake anati saliyense wa inu ali woyera.

12 Iye atamaliza kusambitsa mapazi awo anavala zovala zake ndi kubwerera pamalo pake. Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukuzindikira zimene ndakuchitirani inu? 13 Inu mumanditcha Ine, ‘Mphunzitsi’ ndi ‘Mbuye,’ ndipo mumakhoza mukamatero, pakuti ichi ndi chimene Ine ndili. 14 Tsono ngati Ine, Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi anu. 15 Ine ndakupatsani chitsanzo kuti muzichita monga Ine ndachitira. 16 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti wantchito saposa mbuye wake, kapena wotumidwa kuposa amene wamutuma. 17 Ngati inu mudziwa zinthu zimenezi, mudzakhala odala mukamazichita.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.