Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 24:34-38

34 Motero iye anati, “Ine ndine wantchito wa Abrahamu. 35 Yehova wadalitsa mbuye wanga kwambiri, ndiponso walemera. Wamupatsa nkhosa ndi ngʼombe, siliva ndi golide, antchito aamuna ndi antchito aakazi, komanso ngamira ndi abulu. 36 Sara, mkazi wa mbuye wanga anamubalira iye mwana wamwamuna ngakhale kuti Sarayo anali wokalamba. Tsono mbuye wanga wamupatsa mwanayo chuma chonse. 37 Tsono mbuye wanga anandilumbiritsa kuti ndisunge mawu ake akuti, ‘Usadzamupezere mwana wanga mkazi kuchokera mwa atsikana a dziko lino la Kanaani, 38 koma upite ku banja la abambo anga ndi kwa abale anga kuti ukamupezere mkazi mwana wanga.’ ”

Genesis 24:42-49

42 “Tsono lero lino pamene ndafika pa chitsime, ndinapempha kuti, ‘Yehova, Mulungu wa mbuye wanga, Abrahamu, ngati Inu mwandidalitsadi pa ulendowu, 43 taonani ndayima pambali pa chitsime ichi; ndipo ndidzati kwa namwali amene atabwere kudzatunga kuti, chonde nditamwako madzi a mu mtsuko wakowu,’ 44 ndipo ngati adzandiyankha kuti, ‘Imwani ndipo ndizimwetsanso madzi ngamira zanuzi,’ ameneyo akhale yemwe Yehova wamusankhira mwana wa mbuye wanga.”

45 “Ndisanatsirize kupemphera, ndinangoona Rebeka akutulukira mtsuko wake uli pa phewa. Anatsetserekera ku chitsime kukatunga madzi ndipo ndinati kwa iye, ‘Chonde patseko madzi akumwa.’

46 “Mofulumira, anatsitsa mtsuko wake pa phewa pake nati, ‘Imwani ndiponso ndizimwetsa madzi ngamira zanuzi.’ Kotero ine ndinamwa ndipo anamwetsanso ngamirazo.

47 “Ndinamufunsa kuti, ‘Ndiwe mwana wa yani?’

“Iye anati, ‘Ndine mwana wa Betueli mwana wa Nahori, amene Milika anamuberekera.’

“Tsono ndinayika chipini pa mphuno yake ndi kumveka zibangiri mʼmikono yake, 48 kenaka ndinawerama pansi ndi kupembedza Yehova. Ndipo ndinatamanda Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, amene anandilondolera mokhulupirika njira yanga. Iye wandifikitsa kwa mʼbale wake kumene ndapezera mbeta mwana wa mbuye wanga. 49 Tsono ngati mukufuna kuonetsa kukoma mtima kwanu kwa mbuye wanga, ndikuonetsa kukhulupirika kwanu, ndiwuzeni; ndipo ngati si choncho ndiwuzeninso kuti ndidziwe chochita.”

Genesis 24:58-67

58 Choncho iwo anamuyitana Rebeka uja namufunsa kuti, “Kodi ukufuna kupita ndi munthuyu panopa?”

Iye anayankha kuti, “Ndipita.”

59 Kotero anamulola Rebeka pamodzi ndi mlezi wake kuti apite ndi wantchito wa Abrahamu pamodzi ndi anthu amene anali naye. 60 Ndipo iwo anadalitsa Rebeka ndi kumuwuza kuti,

“Iwe ndiwe mlongo wathu, Mulungu akudalitse iwe, ukhale
    mayi wa anthu miyandamiyanda;
ndi kuti zidzukulu zako zidzalanda
    mizinda ya adani awo.”

61 Kenaka Rebeka ndi antchito ake ananyamuka kukakwera ngamira zawo ndipo anapita naye pamodzi munthu uja. Choncho wantchito uja anatenga Rebeka nʼkumapita.

62 Pa nthawiyi nʼkuti Isake atafika kuchokera ku chitsime cha Wamoyo Wondipenya (Beeri-lahai-roi), popeza tsopano ankakhala ku Negevi. 63 Tsiku lina chakumadzulo, Isake anatuluka kukayendayenda ku munda, ndipo atakweza maso anaona ngamira zikubwera. 64 Rebeka nayenso anatukula maso naona Isake. Ndipo anatsika pa ngamira yake 65 nafunsa wantchito uja kuti, “Kodi munthu uyo ndi ndani akuyenda mʼmundamo kubwera kudzakumana nafe?”

Wantchitoyo anayankha, “Ndiye mbuye wanga.” Choncho Rebeka anatenga nsalu ndi kufunda kumaso.

66 Tsono wantchito uja anawuza Isake zonse zimene anazichita. 67 Isake analowa naye Rebeka mu tenti ya amayi ake Sara, ndipo anakhala mkazi wake. Isake anamukonda kwambiri Rebeka mkazi wake motero kuti zimenezi zinamutonthoza imfa ya amayi ake.

Masalimo 45:10-17

10 Tamvera, iwe mwana wa mkazi ganizira ndipo tchera khutu;
    iwala anthu ako ndi nyumba ya abambo ako.
11 Mfumu yathedwa nzeru chifukwa cha kukongola kwako;
    mulemekeze pakuti iyeyo ndiye mbuye wako.
12 Mwana wa mkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso,
    amuna a chuma adzafunafuna kukoma mtima kwako.

13 Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake,
    chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.
14 Atavala zovala zamaluwamaluwa akupita naye kwa mfumu;
    anamwali okhala naye akumutsatira
    ndipo abweretsedwa kwa inu.
15 Iwo akuwaperekeza ndi chimwemwe ndi chisangalalo;
    akulowa mʼnyumba yaufumu.

16 Ana ako aamuna adzatenga malo a makolo ako;
    udzachititsa kuti akhale ana a mfumu mʼdziko lonse.
17 Ndidzabukitsa mbiri yako mʼmibado yonse;
    choncho mitundu yonse idzakutamanda ku nthawi za nthawi.

Nyimbo ya Solomoni 2:8-13

Tamverani bwenzi langa!
    Taonani! Uyu akubwera apayu,
akulumphalumpha pa mapiri,
    akujowajowa pa zitunda.
Bwenzi langa ali ngati gwape kapena mwana wa mbawala.
    Taonani! Uyo wayima kuseri kwa khoma lathulo,
akusuzumira mʼmazenera,
    akuyangʼana pa mpata wa zenera.
10 Bwenzi langa anayankha ndipo anati kwa ine,
    “Dzuka bwenzi langa,
    wokongola wanga, ndipo tiye tizipita.
11 Ona, nyengo yozizira yatha;
    mvula yatha ndipo yapitiratu.
12 Maluwa ayamba kuoneka pa dziko lapansi;
    nthawi yoyimba yafika,
kulira kwa njiwa kukumveka
    mʼdziko lathu.
13 Mtengo wankhuyu ukubereka zipatso zake zoyambirira;
    mitengo ya mpesa ya maluwa ikutulutsa fungo lake.
Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga
    tiye tizipita.”

Aroma 7:15-25

15 Ine sindizindikira zimene ndimachita. Pakuti zimene ndimafuna kuchita sindizichita koma zimene ndimadana nazo ndi zimene ndimazichita. 16 Ndipo ngati ndimachita zimene sindimafuna kuzichita, ndiye kuti ndikuvomereza kuti lamulo ndi labwino. 17 Monga mmene zililimu, si inenso mwini amene ndimazichita zimenezi, koma tchimo limene lili mʼkati mwanga. 18 Ine ndikudziwa kuti mwa ine mulibe kanthu kabwino, ndiye kuti mʼthupi langa lauchimo. Pakuti ndimafuna kuchita zabwino, koma ndimalephera kuzichita. 19 Ine sindichita zabwino zimene ndimafuna koma ndimachita zonyansa zimene sindikuzifuna. 20 Tsopano ngati ine ndimachita zimene sindikuzifuna, si inenso amene ndimazichita, koma ndi tchimo limene lili mʼkati mwanga.

21 Tsono ndapeza kuti lamuloli likugwira ntchito. Ngakhale ndimafuna kuchita zabwino, zoyipa zili nane pomwepo. 22 Mtima wanga umakondwera ndi lamulo la Mulungu. 23 Koma mʼkati mwanga ndimaona lamulo lina likugwira ntchito kulimbana ndi zomwe mtima wanga umavomereza. Lamulo limenelo landisandutsa wamʼndende walamulo la uchimo lomwe likugwira ntchito mʼkati mwa ziwalo zanga. 24 Kalanga ine! Adzandipulumutsa ndani ku thupi la imfali? 25 Atamandike Mulungu, amene amandipulumutsa kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye athu!

Kotero tsono, ineyo ndi mtima wanga ndimatumikira lamulo la Mulungu, koma ndi thupi langa ndimatumikira lamulo la uchimo.

Mateyu 11:16-19

16 “Kodi mʼbado uwu ndingawufanizire ndi chiyani? Uli ngati ana opezeka mʼmisika amene akuyitana anzawo nʼkumati:

17 “ ‘Tinakuyimbirani zitoliro,
    koma inu simunavine;
ife tinayimba nyimbo zamaliro,
    koma inu simunalire.’

18 Pakuti Yohane sanabwerere kudya kapena kumwa koma iwo ankanena kuti, ‘Iye anali ndi chiwanda.’ 19 Mwana wa Munthu anabwera ndi kumadya ndi kumwa koma iwo akuti, ‘Munthu wadyera, woledzera, bwenzi la amisonkho ndi bwenzi la ochimwa.’ Koma nzeru imatsimikizika kuti ndi yolondola mwa ntchito zake.”

Mateyu 11:25-30

Goli la Khristu

25 Pa nthawi imeneyo Yesu anati, “Ine ndikukuyamikani Inu Atate Ambuye akumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa Inu mwawabisira zinthu izi anzeru ndi ophunzira ndi kuziwulula kwa ana angʼonoangʼono. 26 Inde, Atate, ichi chinali chokukomerani Inu.

27 “Zinthu zonse zapatsidwa kwa Ine ndi Atate anga. Palibe mmodzi amene adziwa Mwana kupatula Atate ndipo palibe mmodzi amene adziwa Atate kupatula Mwana ndi kwa iwo amene Mwana awasankha kuwawululira.

28 “Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. 29 Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa. Ndipo inu mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. 30 Pakuti goli langa ndi losavuta ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.