Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
10 Tamvera, iwe mwana wa mkazi ganizira ndipo tchera khutu;
iwala anthu ako ndi nyumba ya abambo ako.
11 Mfumu yathedwa nzeru chifukwa cha kukongola kwako;
mulemekeze pakuti iyeyo ndiye mbuye wako.
12 Mwana wa mkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso,
amuna a chuma adzafunafuna kukoma mtima kwako.
13 Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake,
chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.
14 Atavala zovala zamaluwamaluwa akupita naye kwa mfumu;
anamwali okhala naye akumutsatira
ndipo abweretsedwa kwa inu.
15 Iwo akuwaperekeza ndi chimwemwe ndi chisangalalo;
akulowa mʼnyumba yaufumu.
16 Ana ako aamuna adzatenga malo a makolo ako;
udzachititsa kuti akhale ana a mfumu mʼdziko lonse.
17 Ndidzabukitsa mbiri yako mʼmibado yonse;
choncho mitundu yonse idzakutamanda ku nthawi za nthawi.
Yakobo ndi Esau
19 Iyi ndi mbiri ya Isake mwana wa Abrahamu.
Abrahamu anabereka Isake 20 ndipo Isake anali ndi zaka makumi anayi pamene anakwatira Rebeka mwana wa Betueli Mwaramu wa ku Padanaramu mlongo wa Labani Mwaramu.
21 Isake anapempherera mkazi wake kwa Yehova popeza iye anali wosabereka. Yehova anayankha pemphero lake ndipo mkazi wake Rebeka anatenga pathupi. 22 Koma pamene anawo amalimbana mʼmimba mwake, iye anati, “Bwanji zikundichitikira zoterezi?” Choncho anapita kukafunsa kwa Yehova.
23 Yehova anati kwa iye,
“Udzabala mafuko awiri a anthu olimbana,
ndipo magulu awiri a anthu ochokera mwa iwe adzasiyana;
fuko limodzi lidzakhala la mphamvu kuposa linzake,
ndipo wamkulu adzatumikira wamngʼono.”
24 Pamene nthawi inakwana yakuti abeleke, Rebeka anaberekadi mapasa. 25 Woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati chovala cha ubweya; choncho anamutcha Esau. 26 Kenaka mʼbale wake anabadwa atagwira chidendene cha Esau; choncho anamutcha Yakobo. Isake anali ndi zaka 60 pamene Rebeka anabereka mapasawa.
27 Anyamatawo anakula ndipo Esau anakhala katswiri wosaka, munthu wamʼthengo, pamene Yakobo anali munthu wofatsa, wokonda kukhala pa nyumba.
Chitsanzo cha Banja pa Mphamvu za Malamulo
7 Kodi simukudziwa abale kuti Malamulo ali ndi ulamuliro pa munthu pokhapokha ngati ali ndi moyo? Ine ndikuyankhula kwa anthu amene akudziwa Malamulo. 2 Mwachitsanzo, Malamulo amati mkazi wokwatiwa ndi womangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wakeyo nthawi yonse pamene mwamuna wakeyo ali moyo. Koma ngati mwamuna wake amwalira, mkaziyo ndi womasulidwa ku lamulo la ukwati. 3 Koma ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina pamene mwamuna wake ali moyo, amatchedwa wachigololo. Koma ngati mwamuna wakeyo amwalira, mkaziyo amasuka ku lamulo ndipo si wachigololo, ngakhale kuti wakwatiwa ndi mwamuna wina.
4 Chimodzimodzi inunso, abale anga, munafa ku Malamulo kudzera mʼthupi la Khristu, kuti mukwatiwe ndi wina, ndi Iye amene anauka kwa akufa kuti tibalire Mulungu chipatso. 5 Pakuti pamene tinkalamulidwa ndi khalidwe lathu lauchimo, zilakolako zauchimo zimene Malamulo anaziwutsa zinkagwira ntchito mʼmatupi mwathu kotero kuti zinabala imfa. 6 Koma tsopano tamasulidwa ku Malamulowo pakuti tinafa ku zimene zinkatimanga, ndipo Mzimu Woyera akutithandiza kutumikira Mulungu mʼnjira yatsopano ndipo osati mʼnjira yakale yolembedwa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.