Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 47

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.

47 Ombani mʼmanja, inu anthu onse;
    fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.
Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba;
    Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi!
Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu;
    anayika anthu pansi pa mapazi athu.
Iye anatisankhira cholowa chathu,
    chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda.
            Sela

Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe,
    Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga.
Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando;
    imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando.

Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi;
    imbirani Iye salimo la matamando.
Mulungu akulamulira mitundu ya anthu;
    Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.
Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana
    monga anthu a Mulungu wa Abrahamu,
pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu;
    Iye wakwezedwa kwakukulu.

Yesaya 51:1-3

Chipulumutso Chamuyaya cha Ziyoni

51 “Mverani Ine, inu amene mukufuna chipulumutso
    ndiponso amene mumafunafuna Yehova:
Taganizani za thanthwe kumene munasemedwa
    ndipo ku ngwenya kumene anakukumbani;
taganizani za Abrahamu, kholo lanu,
    ndi Sara, amene anakubalani.
Pamene ndinkamuyitana nʼkuti alibe mwana,
    koma ndinamudalitsa ndi kumupatsa ana ambiri.
Yehova adzatonthozadi Ziyoni,
    ndipo adzachitira chifundo mabwinja ake onse;
Dziko lake la chipululu adzalisandutsa ngati Edeni,
    malo ake owuma ngati munda wa Yehova.
Anthu adzayimba nyimbo zonditamanda
    ndi kundiyamika.

Mateyu 11:20-24

Tsoka la Mizinda Itatu Yosatembenuka mtima

20 Pamenepo Yesu anayamba kudzudzula mizinda imene zodabwitsa zake zambiri zinachitikamo, chifukwa chakuti sinatembenuke mtima. 21 “Tsoka kwa iwe Korazini! Tsoka kwa iwe Betisaida! Ngati zodabwitsa zimene zinachitika mwa iwe zikanachitidwa mu Turo ndi Sidoni, iwo akanalapa kale atavala ziguduli ndi kudzola phulusa. 22 Koma ndikuwuzani inu kuti pa tsiku lachiweruzo mlandu wa Turo ndi Sidoni udzachepako kusiyana ndi wanu. 23 Ndipo iwe Kaperenawo, kodi udzakwezedwa kufika kumwamba? Ayi, udzatsitsidwa mpaka pansi kufika ku Hade. Ngati zodabwitsa zimene zinachitika mwa iwe, zikanachitika mu Sodomu, bwenzi iye alipo kufikira lero. 24 Koma Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku la chiweruziro mlandu wa Sodomu udzachepako kusiyana ndi wanu.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.